Nyimbo 113
Tikuyamikira Mulungu Kuti Anatipatsa Mawu Ake
(Afilipi 2:16)
1. Yehova Atate, tikuyamika
Chifukwa mawu anu mwatipatsa.
Munauzira anthu kulemba za inu.
Malemba ’matitsogolera ndithu.
2. Aneneri anu anali anthu,
Ankamvadi mmene timamveratu.
Ndipo za moyo wawo tikamaphunzira
Timakhala anthu olimba mtima.
3. Mawu anu amatikhudza mtima.
Moyo ndi mzimu amalekanitsa.
Afufuza zolinga za mumtima wathu.
Atithandiza kukhala ndi nzeru.
(Onaninso Sal. 119:16, 162; 2 Tim. 3:16; Yak. 5:17; 2 Pet. 1:21.)