GAO 1
Kodi Tingamumvetsele Bwanji Mulungu?
Mulungu amakamba ndi ife kupitila m’Baibo. 2 Timoteyo 3:16
Mulungu woona anauza amuna ena kulemba maganizo ake m’buku lapadela. Buku limenelo ni Baibo. M’Baibo muli uthenga wofunika umene Mulungu afuna kuti mudziŵe.
Mulungu amadziŵa zinthu zabwino kwa ife ndipo ni Kasupe wa nzelu. Ngati mumvetsela kwa iye, mudzakhala anzelu.—Miyambo 1:5.
Mulungu afuna kuti aliyense padziko lapansi aziŵelenga Baibo. Ndipo masiku ano Baibo ili m’zitundu zambili.
Kuti mumvetsele kwa Mulungu, muyenela kuŵelenga Baibo ndi kuimvetsetsa.
Anthu kulikonse akuphunzila za Mulungu. Mateyu 28:19
Mboni za Yehova zingakuthandizeni kumvetsetsa Baibo.
Zimaphunzitsa coonadi ca Mulungu padziko lonse.
Simufunika kulipila ndalama iliyonse kuti muphunzile coonadi. Ndiponso mungaphunzile za Mulungu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kumene mumakhala.