GAO 9
Kodi Paladaiso Idzabwela Liti?
Mavuto amene ali padziko lapansi aonetsa kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Luka 21:10, 11; 2 Timoteyo 3:1-5
Zinthu zambili zimene zicitika masiku ano, Baibo inakambilatu kuti zidzacitika. Inakamba kuti anthu adzakhala okonda ndalama, osamvela makolo, oopsa, ndi okonda zosangalatsa.
Kudzakhala zivomezi zazikulu, nkhondo, njala, ndi matenda oculuka. Zinthu zimenezi zikucitika masiku ano.
Yesu anakambanso kuti uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.—Mateyu 24:14.
Ufumu wa Mulungu udzacotsa zoipa zonse. 2 Petulo 3:13
Posacedwa Yehova adzaononga anthu onse oipa.
Satana ndi viŵanda vake adzalangidwa.
Amene amamvetsela kwa Mulungu adzapulumuka ndi kukhala m’dziko latsopano lolungama, limene simudzakhalanso mantha, ndipo anthu adzakhulupililana ndi kukondana.