GAO 11
Kodi Yehova Amamvetsela kwa Ife?
Mulungu amamva mapemphelo athu. 1 Petulo 3:12
Yehova amamva mapemphelo. (Salimo 65:2) Amafuna kuti tizikamba naye kucokela mumtima.
Muzipemphela kwa Yehova osati kwa wina aliyense.
Tingapemphelele zinthu zambili. 1 Yohane 5:14
Muzipemphela kuti cifunilo ca Mulungu cicitike kumwamba ndi pano padziko.
Muzipemphela m’dzina la Yesu, kuonetsa kuti mumayamikila zimene anakucitilani.
Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kucita zabwino. Ndiponso mungapemphe za cakudya, nchito, nyumba, zovala, ndi thanzi lanu.