Phunzilo 1
Chivumbulutso 4:11
Ndani anapanga dziko?
Ndani anapanga nyanja?
Ndani anapanga iwe ndi ine?
Ndani anapanga gulugufe ndi mapiko ake okongola?
Yehova Mulungu analenga zinthu zonse.
ZOCITA
Muŵelengeleni mwana wanu:
Chivumbulutso 4:11
Uzani mwana wanu kuti aloze:
Nyenyezi Mitambo Dzuŵa
Boti Dziko Nyumba
Nyanja Gulugufe
M’funseni mwana wanu:
Dzina la Mulungu ndani?
Yehova akhala kuti?
Anapanga ciani?
[Cithunzi 4, 5]