LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • yc phunzilo 6 masa. 14-15
  • Davide Sanacite Mantha

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Davide Sanacite Mantha
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Zofanana
  • Davide na Goliyati
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • “Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Davide Ndi Goliyati
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Dalilani Yehova Kuti Akulimbitseni Mtima
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Phunzitsani Ana Anu
yc phunzilo 6 masa. 14-15

PHUNZILO 6

Davide Sanacite Mantha

Kodi ukacita mantha umacita ciani?— Mwina umapita kwa amai kapena atate ako kuti akuthandize. Koma palinso wina amene angakuthandize. Iye ndi wamphamvu kuposa aliyense. Kodi munthu ameneyo umudziŵa?— Inde, ndi Yehova Mulungu. Tiye tikambilane za mnyamata wina wa m’Baibulo dzina lake Davide. Iye anadziŵa kuti Yehova adzamuthandiza nthawi zonse, conco sanali kucita mantha.

Kuyambila nthawi imene Davide anali khanda, makolo ake anam’phunzitsa kukonda Yehova. Izi zinathandiza Davide kukhala wolimba mtima ngakhale pamene anakumana ndi zinthu zocititsa mantha. Iye anadziŵa kuti Yehova ndi Bwenzi lake ndipo adzamuthandiza. Tsiku lina pamene Davide anali kusamalila nkhosa, mkango waukulu unabwela ndi kugwila nkhosa. Kodi udziŵa zimene Davide anacita? Iye anauthamangitsa ndi kuupha ndi manja ake. Ndiyeno panthawi ina cimbalangondo cinagwila nkhosa, naconso Davide anacipha. Kodi uganiza kuti ndani anathandiza Davide?— Inde, anali Yehova.

Panali nthawi inanso pamene Davide analimba mtima kwambili. Nthawi imeneyo Aisiraeli anali kumenyana nkhondo ndi Afilisiti. Mmodzi wa asilikali acifilisiti anali wamtali kwambili, iye anali cimphona. Dzina lake linali Goliyati. Cimphona cimeneci cinali kunyoza asilikali aciisiraeli ndi Yehova. Goliyati anali kuuza asilikali aciisiraeli kuti amene ali ndi mphamvu abwele timenyane nane. Koma Aisiraeli onse anacita mantha kwambili kumenyana naco. Pamene Davide anamva zimenezo, anauza Goliyati kuti: ‘Tiye timenyane! Yehova adzandithandiza ndipo ndidzakugonjetsa.’ Kodi uganiza kuti Davide anali wolimba mtima?— Inde, iye analidi wolimba mtima kwambili. Kodi ufuna kudziŵa zimene zinacitika pambuyo pake?

Davide anatenga coponyela mwala [gulaye] ndi miyala isanu yosalala ndi kupita kukamenyana ndi cimphona cimeneco. Pamene Goliyati anaona kuti Davide ndi kamnyamata, anayamba kumunyoza. Koma Davide anamuuza kuti: ‘Iwe ubwela kwa ine ndi lupanga, koma ine ndibwela kwa iwe m’dzina la Yehova.’ Kenako iye anaika mwala m’gulaye kapena kuti coponyela ndi kuthamangila kumene kunali Goliyati, ndipo anaponya mwala umenewo kwa iye. Mwala umenewo unamenya Goliyati pamphumi. Cimphona cimeneco cinagwa pansi ndi kufa. Afilisiti anacita mantha kwambili cakuti onse anathawa. Kodi kamnyamata monga Davide kanakwanitsa bwanji kugonjetsa cimphona?— Yehova anam’thandiza ndipo iye anali ndi mphamvu kwambili kuposa cimphona.

Davide akupha Goliyati

Davide sanacite mantha cifukwa anadziŵa kuti Yehova adzamuthandiza

Kodi uphunzilapo ciani pa nkhani ya Davide?— Yehova ndi wamphamvu kuposa aliyense. Ndipo ndi mnzako. Conco, nthawi ina ukadzacita mantha, uzikumbukila kuti Yehova angakuthandize kukhala wolimba mtima.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • Salimo 56:3, 4

  • 1 Samueli 17:20-54

MAFUNSO:

  • Kodi Davide anacita ciani pamene mkango ndi cimbalangondo zinafuna kugwila nkhosa zake?

  • Pamene Goliyati ananyoza Yehova kodi Davide anamuuza ciani?

  • Kodi Davide anamugonjetsa bwanji Goliyati?

  • N’cifukwa ciani Davide sanaope mkango, cimbalangondo ndi cimphona?

  • Kodi uphunzilapo ciani pa nkhani ya Davide?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani