LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • yc phunzilo 8 masa. 18-19
  • Yosiya Anali ndi Anzake Abwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yosiya Anali ndi Anzake Abwino
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Zofanana
  • Yosiya Anali Kukonda Cilamulo ca Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mfumu Yabwino Yotsilizila Ya Isiraeli
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Acinyamata—Kodi Mudzakhala na Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Phunzitsani Ana Anu
yc phunzilo 8 masa. 18-19
Mfumu Yosiya ikumvetsela kwa mnzake Yeremiya

PHUNZILO 8

Yosiya Anali ndi Anzake Abwino

Kodi umaona kuti kucita zabwino ndi kovuta?— Ambili amaganiza conco. Baibulo limatiuza kuti mnyamata wina dzina lake Yosiya anali kuvutika kwambili kucita zabwino. Koma iye anali ndi anzake abwino amene anam’thandiza. Tiye tiphunzile zambili za Yosiya ndi anzake.

Atate a Yosiya anali Amoni, ndipo anali mfumu ya Yuda. Amoni anali kucita zinthu zoipa ndipo anali kulambila mafano. Pamene atate a Yosiya anamwalila, iye anakhala mfumu ya Yuda. Nthawi imeneyo iye anali ndi zaka 8 cabe. Kodi uganiza kuti nayenso anali kucita zoipa monga atate wake?— Iyai, iye anali kucita zabwino.

Mneneli Zefaniya akufotokoza uthenga wa Yehova kwa anthu a ku Yuda

Zefaniya anacenjeza anthu kuti asazilambila mafano

Ngakhale pamene anali wamng’ono kwambili, Yosiya anali kumvela kwambili Yehova. Conco, anthu amene iye anasankha kukhala mabwenzi ake anali cabe aja amene anali kukonda Yehova. Ndipo io anathandiza Yosiya kucita zabwino. Kodi anzake a Yosiya anali ndani?

Mmodzi wa io anali Zefaniya. Zefaniya anali mneneli amene anacenjeza anthu a ku Yuda kuti, ngati alambila mafano adzakumana ndi mavuto. Yosiya anatsatila zimene Zefaniya anamuuza ndipo anali kulambila Yehova osati mafano.

Mnzake wina wa Yosiya anali Yeremiya. Iye anali ndi zaka zofanana ndi Yosiya, ndipo pamene anali kukula anali kukhala moyandikana. Anali mabwenzi apamtima cakuti pamene Yosiya anafa, Yeremiya analemba nyimbo yacisoni yosonyeza mmene anali kumukondela. Yeremiya ndi Yosiya anali kuthandizana pocita zabwino ndi pomvela Yehova.

Yosiya ndi Yeremiya anali kuthandizana kucita zabwino

Kodi uphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yosiya?— Ngakhale pamene anali kamnyamata, Yosiya anali wofunitsitsa kucita zabwino. Iye anali kudziŵa kuti ayenela kukhala paubwenzi ndi anthu amene amakonda Yehova. Iwenso uyenela kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova ndipo amene angakuthandize kucita zabwino.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • 2 Mbiri 33:21-25; 34:1, 2; 35:25

MAFUNSO:

  • Kodi atate a Yosiya anali ndani? Nanga io anali kucita zinthu zotani?

  • Kodi Yosiya anali kufunitsitsa kucita ciani ngakhale pamene anali kamnyamata?

  • Kodi anzake aŵili a Yosiya anali ndani?

  • Kodi uphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yosiya?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani