LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • hf section 6 gao 1-3
  • Mmene Ana Amasinthila Banja

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Ana Amasinthila Banja
  • N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1 M’POFUNIKA KUMVETSA MMENE MWANA AMASINTHILA UMOYO WANU
  • 2 LIMBITSANI CIKWATI CANU
  • 3 KUPHUNZITSA MWANA WANU
  • Dalilani Mulungu Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
hf section 6 gao 1-3
Nasi apeleka mwana amene wangobadwa kwa makolo ake

GAWO 6

Mmene Ana Amasinthila Banja

“Ana ndi colowa cocokela kwa Yehova.”—Salimo 127:3

Kubadwa kwa mwana kungakhale kokondweletsa komanso kolemetsa kwa anthu okwatilana. Monga makolo atsopano, mungadabwe kuti mukuthela nthawi yaitali ndiponso mphamvu zanu pa kusamalila mwana wanu wakhanda. Kusagona mokwanila ndi kusintha kwa maganizo kungapangitse kuti cikwati canu cisaziyenda bwino. Inu nonse aŵili mudzafunika kusintha zinthu zina kuti musamalile mwana wanu ndiponso kusunga cikwati canu. Kodi uphungu wa m’Baibulo ungakuthandizeni bwanji kulimbana ndi mavuto amenewa?

1 M’POFUNIKA KUMVETSA MMENE MWANA AMASINTHILA UMOYO WANU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.” Komanso cikondi “sicisamala zofuna zake zokha, sicikwiya.” (1 Akorinto 13:4, 5) Popeza kuti tsopano mwakhala ndi mwana, mwacibadwa mumaika maganizo anu pa kusamalila mwana wanu. Komabe, mwamuna wanu angayambe kuona kuti simukumusamala, conco musaiŵale kuti nayenso akufunika cisamalilo canu. Moleza mtima ndiponso mokoma mtima, mungamuthandize kuona kuti mumamuganizila ndi kuti iyenso ayenela kuthandizako posamalila mwana wanuyo.

Tate athandiza kudyetsa mwana, ndipo akumusamalila nthawi yausiku

“Inunso amuna pitilizani kukhala ndi akazi anu mowadziŵa bwino.” (1 Petulo 3:7) Mufunika kumvetsa kuti tsopano mkazi wanu adzayamba kuthela mphamvu zake zambili kusamalila mwana wanu. Iye tsopano wakhala ndi maudindo ena amene mwina angamucititse kukhala ndi nkhawa, kukhala wolema komanso kukhala wosakondwela. Nthawi zina akhoza kumakukwiyilani, koma yesetsani kuugwila mtima cifukwa “munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.” (Miyambo 16:32) Khalani wozindikila ndipo muthandizeni pa zimene akufunikila.—Miyambo 14:29.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Atate: Thandizani mkazi wanu kusamalila mwana ngakhale usiku. Mucepetseko nthawi imene mumathela pocita zinthu zina n’colinga cakuti mupeze nthawi yambili yokhala ndi mkazi wanu ndiponso mwana wanu

  • Amai: Mwamuna wanu akafuna kukuthandizani kusamalila mwana musazikana. Ngati sacita bwino nchito imeneyi, muyamikileni ndipo mokoma mtima muonetseni mmene mumacitila

2 LIMBITSANI CIKWATI CANU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Ngakhale kuti m’banja lanu mwabwela wina watsopano, kumbukilani kuti inu ndi mnzanu wa m’cikwati mukali “thupi limodzi.” Yesetsani kulimbitsa cikwati canu.

Akazi, muziyamikila thandizo limene mwamuna wanu amapeleka. Mau anu oyamikila angakhale ‘ocilitsa.’ (Miyambo 12:18) Amuna, muuzeni mkazi wanu kuti ndi wofunika kwambili ndipo mumamukonda. Muyamikileni cifukwa ca mmene amasamalila banja.—Miyambo 31:10, 28.

“Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Nthawi zonse muzimucitila zabwino mnzanu wa m’cikwati. Monga okwatilana, khalani ndi nthawi yokambitsilana, kumvetselana ndi kuyamikilana. Ikafika nthawi ya kugonana musamanane. Ganizilani zofuna za mnzanu wa m’cikwati. Baibulo limati: “Musamanane kupatulapo ngati mwagwilizana kuimitsa kaye mangawawo kwa nthawi yodziŵika.” (1 Akorinto 7:3-5) Conco muli aŵili muyenela kukambilana nkhaniyi moona mtima. Kumvetsetsa kwanu ndi kuleza mtima kudzalimbitsa cikwati canu.

Tate ndi mai akuceza pamodzi pamene mwana wagona

ZIMENE MUNGACITE:

  • Musaiŵale kupeza nthawi yoceza ndi mnzanu wa m’cikwati

  • Muzicita tunthu tung’onotung’ono tumene tungapangitse mnzanu wa m’cikwati kumva kuti akukondedwa. Mukhoza kumubweletsela kamphatso kakang’ono kapena kumutumilako kamesegi.

3 KUPHUNZITSA MWANA WANU

Mai aŵelengela mwana wake

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Kuyambila pamene unali wakhanda, wadziŵa malemba oyela amene angathe kukupatsa nzelu zokuthandiza kuti udzapulumuke.” (2 Timoteyo 3:15) Onani zimene mungacite kuti muphunzitse mwana wanu. Mwana akhoza kuphunzila zambili, ngakhale asanabadwe. Mwana wanu akali m’mimba, amadziŵa mau anu ndipo angakhudzidwe ndi mmene inuyo mukumvela. Akali wakhanda muzimuŵelengela. Ngakhale kuti sangamvetse zimene mukuŵelengazo, akadzakula zidzamuthandiza kuti adzakonde kuŵelenga.

Ngakhale ndi wamng’ono kwambili, mwana wanu angakumvetseleni mukamakamba za Mulungu. Muloleni kuti azikumvetselani mukamapemphela kwa Yehova. (Deuteronomo 11:19) Pamene museŵela naye muzikamba za zinthu zimene Mulungu anapanga. (Salimo 78:3, 4) Pamene mwana wanu akula, adzazindikila kuti mumakonda Yehova ndipo iyenso adzaphunzila kukonda Yehova.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Pemphani nzelu kwa Mulungu zakuti muphunzitse bwino mwana wanu

  • Kuti mwana wanu aphunzile zinthu mwamsanga, muzibweleza mau amene ali ndi mfundo zikuluzikulu

KUBADWA KWA MWANA KUNGAKHALE NDI ZOTSATILAPO ZABWINO M’CIKWATI

M’kupita kwa nthawi, inu ndi mnzanu wa m’cikwati monga makolo mudzadzimva kukhala otonthozedwa ndiponso odalilana. Kulela mwana kungakucititseni kuti muonjezele cikondi, kuleza mtima, ndi kukoma mtima. Ngati mucitila zinthu pamodzi ndi kuthandizana, kukhala ndi mwana m’banja kudzalimbitsa cikwati canu. Mukatelo, mau a pa Salimo 127:3 adzakhala oona kwa inu, ndipo amati: “Cipatso ca mimba ndico mphoto.”

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Mlungu wathawu, ndi zinthu zotani zimene ndinacita zoonetsa kuti ndimayamikila zimene mwamuna kapena mkazi wanga amacitila banja lathu?

  • Kodi ndi liti pamene ine ndi mnzanga wa m’cikwati tinakambilanako za cikwati cathu m’malo mongolankhula za mwana wathu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani