LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 1 masa. 6-11
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • GAWO LAKUMWAMBA LA GULU LA YEHOVA
  • GULU LA YEHOVA LILI PA ULENDO
  • Kodi Mumayendela Limodzi ndi Gulu la Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Yehova Akutsogolela Gulu Lake
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kodi Mumalemekeza Buku Lake la Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 1 masa. 6-11

MUTU 1

Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova

PADZIKO lonse lapansi, pali zipembedzo zambili, zipani zandale, mabungwe azamalonda, komanso mabungwe olimbikitsa zacikhalidwe. Magulu onsewa ni osiyana-siyana m’macitidwe awo a zinthu, zolinga zawo, maganizo awo, na ziphunzitso zawo. Koma pali gulu limodzi losiyana kwambili na magulu ena onsewa. Mawu a Mulungu amaonetsa kuti gulu limenelo ni Mboni za Yehova.

2 N’cokondweletsa kuti na imwe muli m’gulu la Yehova limeneli. Mumacita cifunilo ca Mulungu cifukwa munafika pocimvetsetsa bwino. (Sal. 143:10; Aroma 12:2) Inde, ndimwe mtumiki wa Mulungu wokangalika, wotumikila pamodzi na gulu la abale la padziko lonse. (2 Akor. 6:4; 1 Pet. 2:17; 5:9) Monga mmene Mawu a Mulungu amanenela, izi zimakubweletselani madalitso oŵilikiza, komanso cimwemwe cacikulu. (Miy. 10:22; Maliko 10:30) Pocita cifunilo ca Yehova mokhulupilika, muli na tsogolo la madalitso amuyaya.—1 Tim. 6:18, 19; 1 Yoh. 2:17.

3 Mlengi wathu Wamkulu ali na gulu limodzi cabe padziko lapansi limene amaliyendetsa mwaumulungu. Iye ndiye Mutu pamwamba pa wina aliyense, ndipo ndiye amalilamulila. Tili na cidalilo conse mwa iye. Iye ni Woweluza wathu, Wotipatsa malamulo, komanso Mfumu yathu. (Yes. 33:22) Pokhala Mulungu wadongosolo, anaika makonzedwe akuti ‘tizigwila naye nchito pamodzi,’ pofuna kukwanilitsa cifunilo cake.—2 Akor. 6:1, 2.

4 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikilila-yandikilila, ife tidzatumikilabe pansi pa utsogoleli wa Mfumu yolongedwayo, Khristu Yesu. (Yes. 55:4; Chiv. 6:2; 11:15) Yesu anakambilatu kuti otsatila ake adzacita nchito zambili kupambana zimene iye anacita ali padziko lapansi. (Yoh. 14:12) Zimenezi n’zoona cifukwa otsatila a Yesu akhala akuculukila-culukilabe, ndipo agwila nchito yolalikila kwa zaka zambili, komanso m’maiko ambili-mbili. Inde, akulalikiladi uthenga wabwino wa Ufumu mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.—Mat. 24:14; 28:19, 20; Mac. 1:8.

5 Izi n’zimene zakhala zikucitikadi. Komabe, monga Yesu anakambila, nchito yolengeza uthenga wabwino idzatha panthawi imene Yehova anaikilatu. Maulosi ambili a m’Baibo amaonetsa kuti tsiku lalikulu la Yehova, ndiponso locititsa mantha, lili pafupi kwambili.—Yow. 2:31; Zef. 1:14-18; 2:2, 3; 1 Pet. 4:7.

Tiyesetse ndithu mwakhama kucita zimene Mulungu akufuna. Kuti izi zitheke, tiyenela kumvetsa bwino-bwino mmene gulu la Mulungu limagwilila nchito

6 Ifeyo pokhala ocidziŵa bwino cifunilo ca Yehova masiku ano otsiliza, tiyeni tilimbikile kucita zimene Mulungu akufuna. Cotelo, tifunika kudziŵa bwino mmene gulu la Mulungu limagwilila nchito, komanso kugwilizana nalo kweni-kweni. Gululi limacita zinthu moyendela mfundo za m’Malemba, malamulo, na ziphunzitso za m’Mawu a Mulungu ouzilidwa.—Sal. 19:7-9.

7 Pamene anthu a Yehova atsatila malangizo a m’Baibo, amakhala mwamtendele, na kugwila nchito mogwilizana. (Sal. 133:1; Yes. 60:17; Aroma 14:19) Kodi n’ciani cimalimbikitsa mgwilizano pakati pathu kulikonse? Cikondi. Inde, tikacivala cikondi, cimatilimbikitsa kucitilana zinthu zabwino. (Yoh. 13:34, 35; Akol. 3:14) Posunga khalidwe laumulungu limeneli, timayendela pamodzi na gawo lakumwamba la gulu la Yehova.

GAWO LAKUMWAMBA LA GULU LA YEHOVA

8 Aneneli atatu aŵa: Yesaya, Ezekieli, na Danieli, anaona masomphenya a gawo lakumwamba la gulu la Yehova. (Yes., capu. 6; Ezek., capu. 1; Dan. 7:9, 10) Nayenso mtumwi Yohane anaona masomphenya a makonzedwe akumwamba amenewo, ndipo amatipatsako kadyonkho m’buku la Chivumbulutso. Iye anaona Yehova ali pa mpando wacifumu waulemelelo, atazingidwa na angelo akutamanda kuti: “Woyela, woyela, woyela ndiye Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene analipo, amene alipo, ndi amene akubwela.” (Chiv. 4:8) Yohane anaonanso “mwana wa nkhosa . . . , ataimilila pafupi ndi mpando wacifumu.” Inde, Mwanawankhosa wa Mulungu, Yesu Khristu.—Chiv. 5:6, 13, 14; Yoh. 1:29.

9 Masomphenya oonetsa Yehova atakhala pa mpando wacifumu, aonetsa kuti iye ndiye Mutu wa gulu lake lonse. Ponena za udindo wake wapamwambawo, 1 Mbiri 29:11, 12 imati: “Inu Yehova, ukulu, mphamvu, kukongola, ulemelelo, ndi ulemu ndi zanu, cifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi ndi zanu. Ufumu ndi wanu, inu Yehova, ndinunso Wokwezeka monga mutu pa onse. Cuma ndi ulemelelo zimacokela kwa inu. Inu mumalamulila ciliconse. M’dzanja lanu muli mphamvu ndi nyonga, ndipo dzanja lanu limatha kukweza ndiponso kupeleka mphamvu kwa onse.”

10 Yesu Khristu, wanchito mnzake wa Yehova, nayenso ali na udindo waukulu kumwamba. Iye anapatsidwa mphamvu zambili ndithu. Mulungu “anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi a iyeyo, ndipo anamuika mutu wa zinthu zonse cifukwa ca mpingo.” (Aef. 1:22) Pokamba za Yesu, mtumwi Paulo anati: “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomela mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anacita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo. Kutinso aliyense avomeleze poyela ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afil. 2:9-11) Conco, timakhulupilila na mtima wonse kuti Yesu Khristu alidi mtsogoleli wacilungamo.

11 Danieli anaona masomphenya oonetsa Wamasiku Ambiliyo atakhala pa mpando wacifumu kumwamba. Anaonanso angelo okwana “miliyoni imodzi amene anali kumutumikila nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimilila pamaso pake nthawi zonse.” (Dan. 7:10) Baibo imachula gulu la angelo amenewa kuti ni “mizimu yotumikila ena, yotumidwa kukatumikila amene adzalandile cipulumutso monga colowa cawo.” (Aheb. 1:14) Angelo onsewa anaikidwa pa maudindo olekana-lekana m’gulu la Mulungu.—Akol. 1:16.

12 Tikaganizila mbali zimenezi zokhudza gawo lakumwamba la gulu la Yehova, tingamvetse mmene zinam’gwilila mtima Yesaya ataona masomphenya oonetsa “Yehova atakhala pampando wacifumu,” komanso “pamwamba pake panali aserafi.” Iye ananena kuti: “Tsoka kwa ine! Popeza maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu. Nditsikila kuli cete pakuti ndine munthu wa milomo yodetsedwa, ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.” Inde, Yesaya anacita mantha, ndipo anadzicepetsa ataona ukulu wa gulu la Yehova. Zimenezo zinam’khudza mtima kwambili, cakuti Yehova atafunsa kuti angatume ndani kukagwila nchito yapadela yolengeza ciweluzo cake, iye anati: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”—Yes. 6:1-5, 8.

13 Kuzindikila na kuyamikila gulu la Yehova, kumalimbikitsanso anthu a Mulungu masiku ano. Ndipo pamene gululo likupita patsogolo, timayesetsa kuyendela nalo pamodzi, na kulikhulupilila kweni-kweni.

GULU LA YEHOVA LILI PA ULENDO

14 Ulosi wa Ezekieli wopezeka m’caputala 1, uonetsa Yehova atakwela galeta lakumwamba. Galeta laulemelelo limenelo liimilako gawo losaoneka la gulu la Yehova. Amakwela galeta limenelo m’lingalilo lakuti iye ndiye akutsogolela gulu lake kuti lizicita cifunilo cake.—Sal. 103:20.

15 Wilo iliyonse ya galeta limeneli ili na wilo inzake yopingasa mkati mwake. Izi zimathandiza kuti galetalo likamayenda, mawilo ake akhoza “kuloŵela kumbali zonse zinayi.” (Ezek. 1:17) Mawilowo amathanso kusintha mwamsanga kumene akupita. Koma sikuti galeta limeneli limangodziyendela lokha popanda wina wanzelu woliyendetsa ayi. Yehova salekelela gulu lake kuti lizingopita kulikonse kumene lifuna. Pa Ezekieli 1:20 pamati: “Kulikonse kumene mzimu ukufuna kupita, zamoyozo zinali kupita kumeneko.” Conco, Yehova ndiye amapangitsa gulu lake kupita kulikonse kumene mzimu wake walitsogolela. Ndiye cifukwa cake funso loyenela kudzifunsa n’lakuti, ‘Kodi nimayendela nalo pamodzi?’

16 Kuyendela pamodzi na gulu la Yehova sikutanthauza kupita ku misonkhano na mu ulaliki cabe ayi. Kwakukulu-kulu, kumatanthauza kupita kwathu patsogolo kuuzimu. Tiyenela ‘kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ni ziti,’ komanso kumadya cakudya cauzimu nthawi zonse. (Afil. 1:10; 4:8, 9; Yoh. 17:3) Tizikumbukilanso kuti, pamene pali dongosolo, pamakhalanso mgwilizano. Conco, tiyenela kuseŵenzetsa bwino cuma cathu cauzimu komanso cakuthupi cimene Yehova watipatsa, kuti tikwanilitse nchito yake. Tikamayendela pamodzi na galeta la Yehova lakumwamba, umoyo wathu udzagwilizana na uthenga umene timalalikila.

17 Gulu la Yehova limatithandizadi kupita patsogolo pocita cifunilo ca Mulungu. Kumbukilani kuti Woyendetsa galeta lakumwamba limeneli ni Yehova mwiniwake. Mwa ici, kuyendela nalo pamodzi kumaonetsa kuti timam’lemekeza na kum’dalila monga Thanthwe lathu. (Sal. 18:31) Baibo inatilonjeza kuti: “Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu. Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendele.” (Sal. 29:11) Pokhala m’gulu la Yehova masiku ano, nafenso timalandila mphamvu imene amapeleka, ndipo timasangalala na mtendele wopezeka m’gulu lake. Inde, n’zosacita kufunsa kuti tidzapitiliza kulandila madalitso kwa Yehova, pocita cifunilo cake lelo, mpaka muyaya wonse.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani