MUTU 5
Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
PA NTHAWI ya utumiki wake padziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti anali “m’busa wabwino.” (Yoh. 10:11) Poona gulu limene linali kum’tsatila, “iye anawamvela cisoni, cifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Petulo na atumwi ena anaona kuti Yesu anakhudzikadi mtima. Inde, iye anali wosiyana kothelatu na abusa aciisiraeli, amene ananyanyala nkhosa, cakuti zinakhala zomwazikana, komanso zanjala kuuzimu. (Ezek. 34:7, 8) Citsanzo ca Yesu cophunzitsa na kusamalila nkhosa mpaka kutailapo moyo wake, cinathandiza atumwiwo kuona mmene angathandizile anthu a cikhulupililo kubwelela kwa Yehova, “m’busa ndi woyang’anila miyoyo [yawo].”—1 Pet. 2:25.
2 Pokamba na Petulo pa nthawi inayake, Yesu anagogomeza za kufunika kodyetsa nkhosa na kuziweta. (Yoh. 21:15-17) Mosakaika, Petulo anakhudzidwa kwambili, cakuti pambuyo pake analangiza akulu a mpingo wacikhristu woyambilila kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso cifukwa cofunapo phindu, koma ndi mtima wonse. Osati mocita ufumu pa anthu amene ali colowa cocokela kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo ku gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:1-3) Mawu a Petulo amenewa amapitanso kwa oyang’anila mpingo masiku ano. Motengela citsanzo ca Yesu, akulu amatumikila modzipeleka potsogolela m’nchito ya Yehova.—Aheb. 13:7.
Motengela citsanzo ca Yesu, akulu amatumikila modzipeleka monga zitsanzo ku nkhosa. Iwo amatsogolela m’nchito ya Yehova.
3 Timayamikila kukhala na oyang’anila oikidwa na mzimu amenewa mumpingo. Timapeza mapindu ambili cifukwa ca cisamalilo cawo. Mwacitsanzo, oyang’anila amatilimbikitsa na kuthandiza aliyense mumpingo. Mlungu uliwonse, amacititsa misonkhano ya mpingo, imene imalimbikitsa cikhulupililo ca onse. (Aroma 12:8) Amacita zonse zotheka kuti ateteze nkhosa kwa anthu oipa, komanso ku zovulaza zina. (Yes. 32:2; Tito 1:9-11) Utsogoleli wawo pa nchito yolalikila umatilimbikitsa kulalikila mokangalika mwezi na mwezi. (Aheb. 13:15-17) Inde, Yehova amalimbikitsa mpingo kupitila mwa “mphatso za amuna” zimenezi.—Aef. 4:8, 11, 12.
ZIYENELEZO ZA OYANG’ANILA
4 Kuti mpingo usamalidwe bwino, amuna ofika pa ziyenelezo amaikidwa pa udindo kuti akhale oyang’anila. Ziyenelezo zimenezo zimapezeka m’Mawu a Mulungu. Okhawo amene akwanilitsa ziyenelezo ni amene timati aikidwa na mzimu woyela. (Mac. 20:28) Kunena zoona, miyezo ya m’Malemba ya oyang’anila ni yapamwamba. Ndipo m’pake, cifukwa udindo wa woyang’anila ni udindo waukulu kwambili. Komabe, miyezo imeneyo si yapamwamba kwambili cakuti amuna a pa udindo sangaifikile ayi. Ni yosavuta kwa munthu wokonda Yehova, komanso wodzipeleka kuti am’gwilitsile nchito. Mwa ici, woyang’anila aliyense ayenela kukhala wodziŵika kwa onse monga citsanzo cabwino potsatila malangizo a m’Baibo mu umoyo wake wa tsiku na tsiku.
Kuti mpingo usamalidwe bwino, amuna osankhidwa kukhala oyang’anila afunika kufikila ziyenelezo zopelekedwa m’Mawu a Mulungu
5 Mtumwi Paulo anandandalika ziyenelezo za m’Malemba zofunikila kwa oyang’anila, m’kalata yake yoyamba kwa Timoteyo, komanso ina yopita kwa Tito. Pa 1 Timoteyo 3:1-7 pamati: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anila, akufuna nchito yabwino. Conco woyang’anila akhale wopanda cifukwa comunenezela, mwamuna wa mkazi mmodzi, wosacita zinthu mopitilila malile, woganiza bwino, wadongosolo, woceleza alendo, ndiponso wotha kuphunzitsa. Asakhale munthu womwa moŵa mwaucidakwa, kapena wandewu, koma wololela. Asakhale waukali, kapena wokonda ndalama. Akhale mwamuna woyang’anila bwino banja lake. Wa ana omumvela ndi mtima wonse. (Ndithudi, ngati munthu sadziŵa kuyang’anila banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalile bwanji?) Asakhale wotembenuka kumene, kuopela kuti angakhale wotukumuka cifukwa ca kunyada, n’kulandila ciweluzo cofanana ndi cimene Mdyelekezi analandila. Komanso, akhale woti ngakhale anthu akunja akumucitila umboni wabwino, kuti asatonzedwe ndi kukodwa mu msampha wa Mdyelekezi.”
6 Paulo analembela Tito kuti: “Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo amene ndinakupatsa. Mkulu ayenela kukhala wopanda cifukwa comunenezela, mwamuna wa mkazi mmodzi, wa ana okhulupilila ndi osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulilika. Pakuti woyang’anila ayenela kukhala wopanda cifukwa comunenezela. Pokhala mtumiki wa Mulungu, asakhale womva zake zokha, wa mtima wapacala, womwa moŵa mwaucidakwa, wandewu, kapena wokonda kupeza phindu mwacinyengo. Koma akhale woceleza alendo, wokonda zabwino, woganiza bwino, wolungama, wokhulupilika, wodziletsa, wogwila mwamphamvu mawu okhulupilika pamene akuphunzitsa mwaluso, kuti athe kulimbikitsa anthu ndi ciphunzitso colondola ndiponso kudzudzula otsutsa.”—Tito 1:5-9.
7 Olo kuti poyamba ziyenelezo za m’Malemba zimenezi zingaoneke monga zovuta kuzifikila, amuna acikhristu sayenela kudodoma pokalamila udindo. Ngati alimbikila kukhala na makhalidwe acikhristu ofunikila kwa oyang’anila, amalimbikitsanso ena mumpingo kukalamila maudindo. Paulo analemba kuti colinga cotipatsila amunawo amene ni “mphatso,” n’cakuti “awongolele oyelawo, acite nchito yotumikila, amange thupi la Khristu, kufikila tonse tidzafike pa umodzi m’cikhulupililo komanso pa kumudziŵa molondola Mwana wa Mulungu, inde, kufikila tidzakhale munthu wacikulile, wofika pa msinkhu waucikulile umene Khristu anafikapo.”—Aef. 4:8, 12, 13.
8 Woyang’anila sayenela kukhala wacicepele kapena mwamuna wongophunzila kumene coonadi. Ayenela kukhala m’bale wokhwima bwino pa umoyo wacikhristu, wacidziŵitso cozama pa Baibo, woyamvetsetsa bwino Malemba, komanso wa cikondi ceni-ceni pa abale na alongo. Ayenela kukhala wosaopa kulankhula na kudzudzula ocita zoipa, kuti ateteze nkhosa kwa aliyense amene angafune kuzidyela masuku pamutu. (Yes. 32:2) Inde, oyang’anila ayenela kudziŵika kwa onse mumpingo kuti ni amuna okhwima mwauzimu, amene amasamala nkhosa za Mulungu.
9 Oyenelela kukhala oyang’anila, ni aja amene amacita zinthu mwanzelu pa umoyo wawo. Ngati woyang’anila ni wokwatila, ayenela kukhala mwamuna wa mkazi mmodzi, komanso woyang’anila bwino banja lake. Ngati woyang’anila ali na ana okhulupilila amene amamumvela na mtima wonse, ndipo sanenezedwa kuti ni amakhalidwe oipa kapena osalamulilika, abale akhoza kumufikila mwacidalilo kufunsilako malangizo kapena nzelu pa nkhani zokhudza banja kapena umoyo wacikhristu. Ayenelanso kukhala wopanda cifukwa comuneneza naco, ndipo akhale munthu wakuti, ngakhale anthu akunja akumucitila umboni wabwino. Akhale woti sanganenezedwe za khalidwe loipa, zimene zingatonzetse mpingo. Asakhale woti anadzudzulidwa posacedwa cifukwa ca colakwa cacikulu. Ayenela kukhala citsanzo cimene ena mumpingo amafuna kutengelako, ndipo amamva bwino kuikiza miyoyo yawo yauzimu m’cisamalilo cake.—1 Akor. 11:1; 16:15, 16.
10 Abale oyenelela amenewa, amatumikila mumpingo wacikhristu pa udindo wolingana na uja wa akulu mu Isiraeli, amene anali amuna “anzelu, aluso ndi ozindikila.” (Deut. 1:13) Sikuti akulu ni anthu osacimwa ayi. Ngakhale n’conco, afunikabe kudziŵika mumpingo komanso kudela kumene akhala kuti amaopa Mulungu, ndipo aonetsa kwa nthawi yaitali kuti amayendela mfundo za Mulungu pa umoyo wawo. Kukhala kwawo opanda cifukwa cowaneneza naco, kumawapatsa ufulu wa kulankhula mumpingo.—Aroma 3:23.
11 Abale oikidwa kukhala oyang’anila amaonetsa kuti ni odziletsa m’zocita zawo, komanso pocita zinthu na ena. Sacita zinthu mopitilila malile. Amadziŵika kukhala acikatikati, komanso a khalidwe lodziletsa. Ucikatikati wawo umaonekela pa zinthu monga kudya, kumwa, maseŵela, makonda ake, komanso zosangalatsa. Ni acikatikatinso pa nkhani ya moŵa, kuti asanenezedwe za kuledzela kapena ucidakwa. Munthu akakhuta moŵa, sakwanitsa kudziletsa bwino-bwino, ndipo sangathe kuyang’anila zinthu zauzimu za mpingo.
12 Munthu woyenelela kukhala woyang’anila mumpingo afunikanso kukhala wadongosolo. Ndipo dongosolo limaonekela m’maonekedwe ake, pakhomo pake, komanso m’zocita zake za masiku onse. Munthu wotelo alibe cizolowezi cocedwetsa zinthu. Amaona zofunikila, ndipo amalinganiza bwino zocita. Komanso, amakonda kuyendela mfundo za umulungu.
13 Woyang’anila ayenela kukhala wololela. Ayenela kucita zinthu molimbikitsa mgwilizano pakati pawo monga akulu, komanso kucilikiza bungwe la akulu. Sayenela kudziona kukhala wofunika kuposa anzake, kapena kuyembekezela zambili kwa ena. Pokhala wololela, woyang’anila saumilila maganizo ake, kuona monga ndiye amaganiza bwino kuposa akulu anzake. Amazindikila kuti akulu ena angakhale na makhalidwe kapena maluso ena amene iye alibe. Mkulu amaonetsa kuti ni wololela ngati mfundo zake zimazikidwa pa Malemba, potengela citsanzo ca Yesu Khristu. (Afil. 2:2-8) Mkulu sayenela kukhala wokonda kukangana na anzake kapena waciwawa. Ayenela kuonetsa ulemu kwa ena, powaona kukhala omuposa. Sakhala na mzimu wa zimene ndanena-ndanena, nthawi zonse woumilila kuti ena atsatile maganizo ake. Asakhale wa mtima wapacala, (wokwiya msanga), koma wamtendele pocita zinthu na anthu ena.
14 Woyang’anila ayenelanso kukhala munthu woganiza bwino. Izi zitanthauza kukhala womvetsa zinthu, wosafulumila kuweluza. Amamvetsa bwino mfundo za Yehova, na mmene zimathandizila. Munthu woganiza bwino amalabadila malangizo na uphungu. Sakhala waciphamaso.
15 Paulo anakumbutsa Tito kuti woyang’anila ni munthu wokonda zabwino. Ayenela kukhala wolungama ndiponso wokhulupilika. Makhalidwe amenewa amaonekela pocita zinthu na ena, komanso posalola kupatutsidwa pa coyenela. Sagwedezeka pa cifunilo ca Yehova, ndiponso sasunthika pa miyezo yolungama. Amadziŵa kusunga cinsinsi. Amakhalanso woceleza, wodzipeleka kuthandiza ena, ndiponso alibe kaso na zinthu zake pothandiza ena.—Mac. 20:33-35.
16 Kuti atumikile bwino, woyang’anila ayenela kukhala wokhoza kuphunzitsa bwino. Malinga na zimene Paulo anauza Tito, woyang’anila ayenela ‘kugwila mwamphamvu mawu okhulupilika pamene akuphunzitsa mwaluso, kuti athe kulimbikitsa anthu ndi ciphunzitso colondola ndiponso kudzudzula otsutsa.’ (Tito 1:9) Ayenela kukhala woganiza bwino, wokhoza kufotokoza umboni, wodziŵa kuyankha otsutsa, ndiponso waluso poseŵenzetsa Malemba kuti akhutilitse ena, na kulimbikitsa cikhulupililo cawo. Woyang’anila amatha kuphunzitsa mwaluso pa nthawi yabwino komanso pa nthawi yovuta. (2 Tim. 4:2) Munthu wina akalakwa, iye amakhala woleza mtima kuti am’dzudzule modekha, kapena kuti akhutilitse munthu wokaikila, kapena kum’limbikitsa kuti acite zabwino cifukwa ca cikhulupililo. Luso lake la kuphunzitsa limaonekela pophunzitsa gulu kapena munthu aliyense payekha.
17 Akulu ayenela kukhala okangalika pa nchito yolalikila. Ayenela kuonetsa kuti amatengela citsanzo ca Yesu, amene anaika patsogolo nchito yolalikila uthenga wabwino. Ndipo powaganizila ophunzila ake, Yesu anawaphunzitsa kulalikila mogwila mtima. (Maliko 1:38; Luka 8:1) Akulu akamacita khama kupezeka mu ulaliki, olo kuti ali na zambili zowatangwanitsa, mpingo wonse umatengela cangu cawo. Ndipo akulu akamalalikila pamodzi na a m’banja mwawo, komanso ofalitsa mumpingo, pamakhala kulimbikitsana cikhulupililo.—Aroma 1:11, 12.
18 Zonsezi zingaoneke monga zovuta kuti woyang’anila azikwanilitse. N’zoona kuti palibe woyang’anila amene angafikepo ndendende pa muyezo wapamwamba wa m’Baibo. Ngakhale n’telo, woyang’anila sayenela kucita kupeleŵela kwambili pa makhalidwe ofunikila. Akulu ena angakhale ocita bwino kwambili m’makhalidwe ena, pamene enanso angapambane m’mbali zina. Pothela pake, bungwe la akulu limakhala na makhalidwe onse abwino omwe amathandiza kuti ayang’anile bwino mpingo wa Mulungu.
19 Pamene akulu monga bungwe apenda abale amene angaikidwe kukhala oyang’anila, nthawi zonse azikumbukila mawu a mtumwi Paulo akuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino, malinga ndi cikhulupililo cimene Mulungu wamupatsa.” (Aroma 12:3) Mkulu aliyense ayenela kudziona kukhala wotsikilapo. Pasapezeke woyesa kukhala “wolungama mopitilila muyezo” popenda ziyenelezo za m’bale. (Mlal. 7:16) Atapendanso bwino-bwino ziyenelezo za m’Malemba za oyang’anila, bungwe la akulu limakambilana kuona ngati m’baleyo akukwanilitsa ziyenelezo pa mlingo wabwino, osati wacikwane-kwane. Ngati akulu apenda m’bale mosayang’ana pa kupanda ungwilo kwake, mosakondela, komanso mopanda kaduka, adzaonetsa kuti amalemekeza miyezo yolungama ya Yehova, ndipo mpingo udzadalitsika. Popenda abale, akulu ayenela kupemphela kuti mzimu wa Mulungu uwathandize kuona bwino-bwino ngati m’bale akufikapo pa ziyenelezo za oyang’anila. Umenewu ni udindo waukulu kwambili umene akulu ali nawo. Conco popenda abale, akulu ayenela kukumbukila cenjezo la mtumwi Paulo lakuti: “Usafulumile kuika munthu aliyense pa udindo.”—1 Tim. 5:21, 22.
MAKHALIDWE AMENE MZIMU WOYELA UMABALA
20 Mu umoyo wawo, oyang’anila ofikapo mwauzimu amaonetsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala, umboni wakuti mzimu woyela umawatsogolela. Paulo anandandalika makhalidwe 9 amene mzimu woyela umabala, amene ni “cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, kufatsa, ndi kudziletsa.” (Agal. 5:22, 23) Oyang’anila otelo amakhala otsitsimula kwa abale, ndipo amathandiza mpingo kukhala wogwilizana potumikila Mulungu. Makhalidwe awo abwino komanso zotulukapo zabwino za khama lawo, zimacitila umboni kuti anaikidwadi na mzimu woyela.—Mac. 20:28.
AMUNA OLIMBIKITSA MGWILIZANO
21 N’cinthu cofunika kwambili kuti akulu azilimbikitsa mgwilizano mumpingo. Olo akhale na zibadwa zosiyana-siyana, ayenela kusunga umodzi wa bungwe lawo mwa kumvetselana mwaulemu, ngakhale kuti angasiyane malingalilo pa nkhani zina. Ngati palibe mfundo iliyonse ya m’Baibo imene yaphwanyidwa, mkulu aliyense ayenela kulolela na kucilikiza cigamulo ca bungwe la akulu. Mzimu wololela umaonetsa kuti mkuluyo amatsogoleledwa na “nzelu yocokela kumwamba,” imene ni “yamtendele, [komanso] yololela.” (Yak. 3:17, 18) Pasapezeke mkulu woganiza kuti amapambana ena, kapena wofuna kulamulila akulu anzake. Kugwilizana kwa akulu potumikila, kumakhalanso kugwilizana na Yehova pom’tumikila, pofuna kupindulitsa mpingo.—1 Akor. capu. 12., Akol. 2:19.
KUKALAMILA UDINDO
22 Amuna acikhristu ofikapo mwauzimu, ayenela kukhala na cifuno cokhala oyang’anila. (1 Tim. 3:1) Koma ayenela kudziŵa kuti kukhala mkulu ni nchito yofuna kudzimana kwambili. Ukulu umafuna kudzipeleka pa kutumikila ena, kusamalila zosoŵa zawo zauzimu. Conco, kukalamila udindo kumatanthauza kulimbikila kuti mufikile ziyenelezo za m’Malemba.
ZINTHU ZINGASINTHE
23 M’bale amene watumikila mokhulupilika kwa nthawi yaitali angadwale kapena kulemala. Mwina cifukwa ca ukalamba, angamalephele kusamalila maudindo a uyang’anilo. Ngakhale n’telo, mpingo uyenela kum’lemekezabe monga mkulu. M’baleyo asafulumile kuganiza zotula pansi udindo cabe cifukwa ca zovuta zimenezo. Iye ni wofunikabe, ndipo ayenela kupatsidwabe ulemu wowilikiza woyenelela akulu onse ogwila nchito molimbika pa kuweta nkhosa za Mulungu.
24 Koma ngati m’bale akuona kuti zingam’khalile bwino kutula pansi udindo cifukwa umoyo wake wasintha kwambili, cakuti n’zovuta kuti apitilize kutumikila, angasankhe kutelo. (1 Pet. 5:2) Koma mpingo uyenela kumamulemekezabe. Ngakhale kuti alibenso maudindo opatsidwa kwa akulu, pakali zambili zimene angathandize mumpingo.
MAUDINDO MUMPINGO
25 Akulu amasamalila maudindo olekana-lekana mumpingo. Pali mgwilizanitsi wa bungwe la akulu, kalembela, woyang’anila utumiki, wotsogoza Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, na woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Akulu ambili amatumikilanso monga oyang’anila tumagulu. Akulu amatumikila pa maudindo amenewa ku nthawi yosaikika. Koma ngati m’bale wasamuka, kapena akulephela kusamalila maudindo ake cifukwa ca thanzi, olo ngati wacotsedwa pa udindo cifukwa copeleŵela pa ziyenelezo za m’Malemba, mkulu wina amasankhidwa pa udindowo. M’mipingo imene akulu ni ocepa, mkulu mmodzi angasamalile maudindo angapo mpaka pamene abale ena angaikidwe pa ukulu.
26 Mgwilizanitsi wa bungwe la akulu ndiye amakhala cheyamani pa miting’i ya bungwe la akulu. Iye amatumikila modzicepetsa pamodzi na akulu ena posamalila nkhosa za Mulungu. (Aroma 12:10; 1 Pet. 5:2, 3) Ayenela kukhala wodziŵa kulinganiza zinthu, komanso wotsogolela mwanzelu.—Aroma 12:8.
27 Kalembela amasamalila mafaelo a mpingo, ndipo amadziŵitsa akulu zinthu zofunikila. Ngati kungakhale kofunikila, pangasankhidwe mkulu wina kapena mtumiki wothandiza kuti azimuthandiza.
28 Woyang’anila utumiki ndiye amayang’anila nchito yolalikila komanso mbali zina zokhudza ulaliki. Amalinganiza maulendo oyendela tumagulu tonse twa ulaliki. Pamapeto a mlungu umodzi m’mwezi uliwonse amayendela kagulu kosiyana. M’mipingo ing’ono-ing’ono yokhala na tumagulu tocepa, kagulu kalikonse angakayendele kaŵili pacaka. Pocezela kagulu, iye ndiye amatengetsa malangizo a ulaliki, kuyenda na kaguluko mu ulaliki, ndiponso kuthandiza ofalitsa mocitila maulendo obwelelako na maphunzilo a Baibo.
OYANG’ANILA TUMAGULU
29 Udindo wina wofunika kwambili mumpingo ni uja wa woyang’anila kagulu. Nchito zake ni izi: (1) kukhala na cidwi pa umoyo wauzimu wa wofalitsa aliyense m’kagulu kake; (2) kuthandiza aliyense m’kagulu kake kutengako mbali mokwanila mu ulaliki, kukhala wokangalika, komanso wokonda nchito yolalikila. Ndipo (3) kuthandiza na kuphunzitsa atumiki othandiza m’kagulu kake kuti akalamile maudindo mumpingo. Bungwe la akulu ndilo limasankha abale omwe angasamalile bwino mbali zimenezi za udindowu.
30 Cifukwa ca mtundu wake wa nchitoyi, ngati n’kotheka, oyang’anila kagulu azikhala akulu. Apo ayi, mtumiki wothandiza wokhoza bwino angasamalile udindowu kufikila mkulu atapezeka. Mtumiki wothandiza amene akusamalila udindo umenewu amachedwa mtumiki wa kagulu, cifukwa si woyang’anila mumpingo. Amatumikila pansi pa uyang’anilo wa akulu posamalila udindo umenewu.
31 Mbali yaikulu ya woyang’anila kagulu ni kutsogolela pa nchito yolalikila. Kupezeka kwake mu ulaliki, kukangalika kwake, na kukonda kwake ulaliki, kumalimbikitsa ofalitsa a m’kagulu kake. Ulaliki wa kagulu umalimbikitsa ndipo umathandiza ofalitsa ambili. Conco, ayenela kukonza pulogilamu ya ulaliki wa kagulu yokomela unyinji. (Luka 10:1-16) Woyang’anila kagulu ayenela kuonetsetsa kuti pali gawo lokwanila kulifola. Ayenela kumatengetsa malangizo a ulaliki, na kugaŵa ofalitsa mmene angayendele pa tsikulo. Ngati sadzapezekapo, apemphe mkulu wina kapena mtumiki wothandiza kuti akatengetse malangizo. Ngati onsewa palibe, angapemphe wofalitsa wacitsanzo cabwino kuti akasamalile mbali imeneyi kuti ofalitsa akakhale na wowatsogolela.
32 Woyang’anila kagulu ayenela kukonzekela pasadakhale kucezela kwa woyang’anila utumiki, na kudziŵitsa ofalitsa a m’kagulu kake za kucezelako, komanso kuwathandiza kuyembekezela mwacidwi kuti akapindule na ulendowo. Ngati ofalitsa onse m’kagulu adziŵitsidwa pasadakhale za kucezela kumeneku, amadzakucilikiza mosangalala.
33 Kagulu kalikonse kayenela kukhala na ofalitsa ocepa cabe. Izi zimathandiza woyang’anila kagulu kuwadziŵa bwino ofalitsa onse a m’kagulu kake. Monga m’busa wacikondi, ayenela kukhala na cidwi pa wofalitsa aliyense. Amayesetsa kulimbikitsa na kuthandiza aliyense pa nchito yolalikila, ndipo amacilikiza misonkhano ya mpingo. Amacitanso zonse zotheka kuthandiza wina aliyense kukhala wolimba kuuzimu. Odwala kapena opsinjika maganizo, amawayendela na kuwalimbikitsa. Pamene auza ena mawu olimbikitsa, kapena uphungu wabwino, ena angalimbikitsidwe na kufuna kukalamila maudindo mumpingo kuti nawonso akatumikile abale na alongo awo. Woyang’anila kagulu aliyense, azicita khama maka-maka posamalila a m’kagulu kake. Ngakhale n’telo, pokhala mkulu komanso m’busa, amasamalanso za ofalitsa onse mumpingo, ndipo ni wokonzeka kuthandiza aliyense wofunikila thandizo.—Mac. 20:17, 28.
34 Udindo winanso wa woyang’anila kagulu ni kusonkhanitsa malipoti a utumiki wa kumunda kwa a m’kagulu kake. Akatelo, amatumiza malipotiwo kwa kalembela. Ofalitsa angathandize woyang’anila kagulu mwa kupeleka malipoti awo mwamsanga. Angapeleke malipotiwo mwacindunji kwa woyang’anila kagulu kumapeto kwa mwezi, kapena kuponya m’kabokosi koponyamo malipoti a utumiki pa Nyumba ya Ufumu.
KOMITI YA UTUMIKI YA MPINGO
35 Pali nchito zina zimene zimasamalidwa na Komiti ya Utumiki ya Mpingo, imene imapangidwa na mgwilizanitsi wa bungwe la akulu, kalembela, na woyang’anila utumiki. Mwacitsanzo, komiti ya utumiki ndiyo imapeleka cilolezo coseŵenzetsa Nyumba ya Ufumu kuti akambilemo nkhani ya cikwati kapena ya malilo. Ndiyo imagaŵilanso ofalitsa ku tumagulu twa ulaliki. Komitiyi imavomelezanso mafomu ofunsila upainiya wanthawi zonse, wothandiza, kapenanso mautumiki ena. Komabe, komiti ya utumiki imagwila nchito pansi pa bungwe la akulu.
36 Nchito za aliyense wa m’komiti ya utumiki, kuphatikizapo wotsogoza Nsanja ya Mlonda, woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, pamodzi na akulu ena onse a m’bungwe la akulu, zimaunikidwa bwino na ofesi ya nthambi.
37 Bungwe la akulu mumpingo uliwonse limakumana nthawi na nthawi kuti akambilane nkhani zokhudza kupita patsogolo kwa mpingo kuuzimu. Kuwonjezela pa miting’i imene akulu amacita pamene wadela ayendela mpingo wawo, amakhalanso na miting’i ina pakapita pafupi-fupi miyezi itatu pambuyo pa kucezeledwa na wadela. Komabe, akulu angakumane nthawi iliyonse pakakhala zofunikila.
KHALANI OGONJELA KWA IWO
38 Oyang’anila nawonso ni anthu opanda ungwilo. Ngakhale n’telo, tikulimbikitsa onse mumpingo kuti aziwagonjela cifukwa ni makonzedwe a Yehova. Iwo adzayankha mlandu kwa Yehova pa zocita zawo. Amaimilako Yehova na ulamulilo wake. Aheberi 13:17 imakamba kuti: “Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela. Iwo amayang’anila miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvela ndi kuwagonjela kuti agwile nchito yawo mwacimwemwe, osati modandaula, pakuti akatelo zingakhale zokuvulazani.” Yehova amaseŵenzetsa mzimu woyela kuika munthu pa udindo, ndipo amaseŵenzetsanso mzimu umodzimodziwo kucotsa munthu pa udindo. Inde, munthu amacotsedwa pa udindo ngati alephela kuonetsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala. Inde, ngati umoyo wake upeleŵela pa ziyenelezo za m’Malemba.
39 Kodi sitili oyamikila ngako nchito yakhama komanso citsanzo cabwino ca oyang’anila amenewa? Polembela mpingo wa ku Atesalonika, Paulo anati m’kalata yake: “Tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwila nchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolelani mwa Ambuye ndi kukulangizani. Muwapatse ulemu waukulu mwacikondi cifukwa ca nchito yawo.” (1 Ates. 5:12, 13) Cifukwa ca kudzipeleka kwa oyang’anila mumpingo, utumiki wathu kwa Mulungu umakhala wosavuta komanso wokondweletsa. Paulo m’kalata yake yoyamba kwa Timoteyo, anachulanso mmene anthu mu mpingo ayenela kucitila kwa oyang’anila. Iye anati: “Akulu otsogolela bwino apatsidwe ulemu waukulu, makamaka amene amacita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.”—1 Tim. 5:17.
MAUDINDO ENA M’GULU LATHU
40 Nthawi zina, akulu ena amasankhidwa kuti atumikile mu Tumagulu Toyendela Odwala (PVG). Ena amatumikila m’Makomiti Okambilana ndi Acipatala (HLC), ndipo amayenda m’zipatala kukakambilana na madokotala za mmene angathandizile Mboni za Yehova mosaseŵenzetsa magazi. Akulu ena amapititsa patsogolo nchito ya Ufumu mwa kuthandiza kumanga na kukonza Nyumba za Ufumu, Mabwalo a Misonkhano, kapena kutumikila m’Makomiti a Msonkhano Wacigawo. Tonsefe timawayamikila kwambili abale amenewa pogwila nchito zimenezi molimbika komanso modzipeleka. Ndithudi, abale amenewo timawapatsa ulemu wowilikiza!—Afil. 2:29.
WOYANG’ANILA DELA
41 Bungwe Lolamulila linaika makonzedwe osankha akulu oyenelela kuti atumikile monga oyang’anila madela. Ofesi ya nthambi ndiyo imatumiza abale amenewa kuti aziyendela mipingo ya m’dela lawo, kaŵili pa caka. Amayendelanso apainiya a kumagawo akutali pa nthawi yake. Kukali nthawi yabwino, amalinganizilatu ndandanda yoyendela mipingo na kuidziŵitsilatu. Mipingo imapindula kwambili na maulendo amenewa.
42 Mgwilizanitsi wa bungwe la akulu ndiye amakhala patsogolo kulinganiza zinthu kuti ulendowo ukakhale wotsitsimula kwa onse. (Aroma 1:11, 12) Akalandila cidziŵitso ca kucezela kwa woyang’anila dela, mgwilizanitsi pamodzi na akulu anzake, amayamba kukonzekela zosamalila wadelayo na mkazi wake (ngati ni wokwatila), kuphatikizapo nyumba yokhalamo na zofunikila zina. Mgwilizanitsi amaonetsetsa kuti onse, kuphatikizapo wadelayo, adziŵitsidwa zimene zakonzedwa.
43 Woyang’anila dela amalumikizana na mgwilizanitsi wa bungwe la akulu kukambilana za misonkhano, na kukumana kotenga malangizo a ulaliki. Izi zimakonzedwa malinga na mmene wadela angalinganizile, komanso motsatila malangizo ocokela ku ofesi ya nthambi. Onse ayenela kudziŵitsidwa pasadakhale za nthawi na malo ocitila misonkhano ya mpingo, miting’i ya apainiya, miting’i ya akulu na atumiki othandiza, komanso nthawi na malo kokatengela malangizo a ulaliki.
44 Pa Ciŵili, woyang’anila dela amapenda Makhadi a Mpingo Olembapo Nchito za Ofalitsa, makhadi olembapo ciŵelengelo ca opezeka pamisonkhano, mafomu a magawo, komanso faelo ya maakaunti. Zimenezi zimam’thandiza kuona mbali zimene mpingo ufunikila cithandizo, na mmene angathandizile abale osamalila nchito zimenezi. Mgwilizanitsi wa bungwe la akulu amaonetsetsa kuti woyang’anila dela walandila faelo ya zimenezi pa nthawi yake.
45 Pocezela mpingo, woyang’anila dela amapatula nthawi yokambilana na abale na alongo aliyense payekha ngati angathe, ku misonkhano, mu ulaliki, pa nthawi ya cakudya, komanso pa nthawi ina iliyonse. Ndiponso amakumana na akulu pamodzi na atumiki othandiza kuti awapatse malangizo oyenelela a m’Malemba, malingalilo othandiza, na kulimbikitsa kuti azisamalila bwino maudindo awo poweta nkhosa zoikizidwa m’manja mwawo. (Miy. 27:23; Mac. 20:26-32; 1 Tim. 4:11-16) Amakumananso na apainiya kuti awalimbikitse pa nchito yawo, komanso kuwathandiza pa mavuto alionse amene angamakumane nawo okhudza utumiki wawo.
46 Ngati pali nkhani zina zofunikila cisamalilo, woyang’anila dela amathandizapo malinga na mpata umene ali nawo pocezela mpingo. Ngati nkhanizo sizinathe mkati mwa mlungu wake, adzalimbikitsa akulu kapena ena oloŵetsedwamo kuti akafufuze malangizo a m’Malemba amene angawathandize. Ngati n’zofunikila kuti ofesi ya nthambi ikacitepo kalondo-londo m’tsogolo, woyang’anila dela na akulu ayenela kutumiza ku ofesi lipoti la tsatane-tsatane wa nkhaniyo.
47 Pocezela mpingo, woyang’anila dela amacita nawo misonkhano ya nthawi zonse. Nthawi zina misonkhano ingasinthidwe malinga na malangizo ocokela ku ofesi ya nthambi. Iye amakamba nkhani zolimbikitsa, zophunzitsa, komanso zomangiliza mpingo. Amathandiza abale na alongo kukulitsa cikondi cawo pa Yehova, pa gulu lake, komanso pa Yesu Khristu.
48 Cimodzi mwa zolinga za woyang’anila dela akamacezela mpingo, ni kulimbikitsa ofalitsa kukhala okangalika mu ulaliki, komanso kuwapatsa malingalilo othandiza. Ambili mumpingo amakwanitsa kulinganiza zocita zawo kotelo kuti akatengeko mbali mokwanila mu ulaliki pa mlungu wapadela, ngakhalenso kucitako upainiya wothandiza mwezi umenewo. Aliyense wofuna kukayenda na woyang’anila dela kapena mkazi wake mu ulaliki ayenela kulembetselatu dzina lake. Pali mapindu ambili kutengelako wadela kapena mkazi wake ku maphunzilo a Baibo, na ku maulendo obwelelako. Khama lanu pocilikiza mlungu wapadela n’loyamikilika kwambili.—Miy. 27:17.
49 Caka ciliconse, pamakonzedwa misonkhano iŵili yadela m’dela lililonse. Woyang’anila dela ndiye amayang’anila kayendetsedwe ka misonkhano imeneyi. Wadelayo amasankha woyang’anila msonkhano wadela na wothandizila wake. Aŵiliwa amaseŵenzela pamodzi na woyang’anila dela polinganiza msonkhano. Zimenezi zimathandiza woyang’anila dela kuika kwambili maganizo ake pa pulogilamu ya msonkhano. Woyang’anila dela amasankhanso abale ena okhoza bwino kuti ayang’anile madipatimenti olekana-lekana. Amalinganizanso za kuŵelengetsela ndalama za dela pambuyo pa msonkhano wadela uliwonse. Msonkhano wadela umodzi caka ciliconse umakhala na woimilako nthambi monga mlendo wawo. Cifukwa ca kutalika kwa mitunda, kapena kucepa kwa malo ocitilako msonkhano, madela ena amagaŵidwa m’masekishoni, ndipo sekishoni iliyonse imakhala na msonkhano wawo wadela.
50 Woyang’anila dela amatumiza lipoti lake la utumiki wakumunda mwacindunji ku ofesi ya nthambi mwezi ukatha. Ngati waseŵenzetsa ndalama zake pa mayendedwe, kugula cakudya, kulipilila malo ogona, kapena zinthu zina zofunikila pa utumiki wake, koma mpingo umene akucezela sunakwanitse kum’bwezela, angatumize malisiti ku ofesi ya nthambi. Oyang’anila oyendela amakhala na cidalilo cakuti akaika zinthu za Ufumu wa Mulungu patsogolo, adzasamalidwanso pa zinthu zakuthupi, monga mmene Yesu analonjezela. (Luka 12:31) Poonetsa kuyamikila, mipingo iyenela kutengela mwayi wowaceleza akulu odzipeleka amenewa.—3 Yoh. 5-8.
KOMITI YA NTHAMBI
51 Pa ofesi ya nthambi iliyonse ya Mboni za Yehova zungulile dziko lapansi, pamakhala abale atatu kapena oposelapo oyenelela mwauzimu, amene amatumikila pa Komiti ya Nthambi. Komiti imeneyi imayang’anila nchito yolalikila m’dziko lawo kapenanso m’maiko ena ali pansi pa nthambi yawo. Mmodzi wa abale a m’komitiyi amatumikila monga mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi.
52 Abale a m’Komiti ya Nthambi amasamalila nkhani zokhudza mipingo yonse ya m’gawo la nthambi yawo. Komiti imeneyi imayang’anilanso nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu m’gawo lonse la nthambi yawo, na kukhazikitsa mipingo na madela kuti asamalile zosoŵa za munda wawo. Komiti ya Nthambi imayang’anilanso nchito za amishonale, apainiya apadela, apainiya a nthawi zonse, komanso apainiya othandiza. Kukakhala misonkhano yadela kapena yacigawo, komiti imeneyi imalinganiza zonse zofunikila, na kugaŵila nkhani zonse pofuna kuti “zinthu zonse zizicitika moyenela ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:40.
53 Maiko ena amakhala na Komiti ya Dziko, imene imayang’anilidwa na Komiti ya Nthambi ya dziko lina. Izi zimathandiza kuti nchito ya m’dzikolo iziyang’anilidwa bwino. Komiti ya Dziko imayang’anila Beteli, kusamalila makalata na malipoti, komanso nchito zonse za m’munda wawo. Komiti ya Dziko imatumikila m’cigwilizano na Komiti ya Nthambi popititsa patsogolo zinthu za Ufumu.
54 Bungwe Lolamulila ndilo limasankha abale otumikila pa Komiti ya Nthambi komanso pa Komiti ya Dziko.
OIMILAKO LIKULU
55 Nthawi na nthawi, Bungwe Lolamulila limatumiza abale oyenelezedwa kuti akayendele nthambi zosiyana-siyana padziko lonse lapansi. M’bale amene wapita pa ulendo umenewu amachedwa woimilako likulu. Nchito yake yaikulu ni kulimbikitsa mabanja a Beteli na kuthandiza abale a m’Komiti ya Nthambi pa zovuta kapena mafunso okhudza nchito yolalikila na kupanga ophunzila. M’baleyu amakumananso na oyang’anila madela osankhidwa, ndiponso nthawi na nthawi amakumananso na amishonale. Powacezela, amakambilana nawo mavuto na zosoŵa zawo, na kuwalimbikitsa pa nchito yawo yofunika kwambili yolalikila za Ufumu na kupanga ophunzila.
56 Woimilako likulu amafunitsitsa kudziŵa mmene nchito yolalikila za Ufumu ikuyendela, komanso mmene mipingo ikucitila. Ngati nthawi ilola, amayendelanso maofesi omasulila mabuku [ma RTO]. Pamene woimilako likulu ayendela nthambi, amatengakonso mbali m’nchito yolalikila za Ufumu.
Tikakhala ogonjelabe kwa oyang’anila amenewa, opatsidwa udindo woweta nkhosa, timakhala ogwilizana na Mutu wa mpingo, Khristu Yesu
OYANG’ANILA ACIKONDI
57 Kukamba zoona, timapindula zedi cifukwa ca khama na cisamalilo cacikondi ca amuna okhwima kuuzimu amenewa. Ngati tikhalabe ogonjela kwa oyang’anila amenewa, opatsidwa udindo woweta nkhosa, timakhala ogwilizana na Mutu wa mpingo, Khristu Yesu. (1 Akor. 16:15-18; Aef. 1:22, 23) Zotulukapo zake n’zakuti, mzimu wa Mulungu umagwila bwino nchito m’mipingo yonse padziko lapansi, ndipo Mawu a Mulungu amatiunikila pa nchito yathu zungulile dziko lapansi.—Sal. 119:105.