LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 11 masa. 116-122
  • Malo Olambilila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malo Olambilila
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NYUMBA YA UFUMU
  • KUMANGA NYUMBA ZA UFUMU
  • MABWALO A MISONKHANO
  • Awa Ndi Malo Athu Olambilila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 11 masa. 116-122

MUTU 11

Malo Olambilila

ALAMBILI oona a Yehova analamulidwa kuti azisonkhana pamodzi kuti azilandila malangizo na kulimbikitsana wina na mnzake. (Aheb. 10:23-25) Malo oyamba olambililapo anthu osankhidwa a Mulungu, Aisiraeli, anali “cihema copatulika, kapena kuti cihema cokumanako.” (Eks. 39:32, 40) Patapita zaka, Solomo mwana wa Davide anamanga nyumba kapena kuti kacisi, wopeleka ulemelelo kwa Mulungu. (1 Maf. 9:3) Kacisiyo anawonongedwa mu 607 B.C.E. Koma pambuyo pake, Ayuda anayamba kulambila Mulungu m’zimango zochedwa masunagoge. M’kupita kwa nthawi, kacisi uja anamangidwanso, ndipo anakhalanso malo apakati a kulambila koona, kapena kuti likulu lake. Yesu anali kuphunzitsa m’masunagoge komanso m’kacisi. (Luka 4:16; Yoh. 18:20) Ndipo anacitapo msonkhano ngakhale pa phili.—Mat. 5:1–7:29.

2 Pambuyo pa imfa ya Yesu, Akhristu anali kusonkhana m’malo apoyela komanso m’nyumba za abale, pophunzitsa Malemba komanso kusangalala na mayanjano pamodzi na Akhristu anzawo. (Mac. 19:8, 9; Aroma 16:3, 5; Akol. 4:15; Filim. 2) Nthawi zina, Akhristu oyambilila anali kusonkhana m’malo obisika kuti owazunza asadziŵe. Inde, atumiki a Mulungu okhulupilika akalewo anali kukondadi kukumana m’malo olambilila kuti ‘aphunzitsidwe na Yehova.’—Yes. 54:13.

3 Masiku anonso, timagwilitsila nchito malo apoyela na nyumba za abale pocita misonkhano yacikhristu. Kambili timakumana m’nyumba za abale potenga malangizo a ulaliki. Amene amapeleka nyumba zawo pa colinga cimeneci amaona kuti ni mwayi kwa iwo. Ambili aona kuti adalitsika mwauzimu potsegula nyumba zawo pa colinga cimeneci.

NYUMBA YA UFUMU

4 Malo odziŵika kwambili omwe Mboni za Yehova zimacitilako misonkhano ni ku Nyumba za Ufumu. Kambili, malo amagulidwa na kumangapo Nyumba ya Ufumu, kapena kukonzanso nyumba imene ilipo kale. Kuti pasawonongeke ndalama zambili, komanso kuti malo athu olambilila azigwila nchito mokwanila, nthawi zambili mipingo ingapo imasewenzetsa Nyumba ya Ufumu imodzi. Koma m’madela ena timacita lendi maholo osonkhanila. Pakamangidwa Nyumba ya Ufumu yatsopano, kapena ngati pacitika nchito yoikonzanso yaikulu, Nyumba ya Ufumuyo imapatulidwa. Koma ngati Nyumba ya Ufumu yangokonzedwa mbali zocepa cabe, palibe cifukwa coipatulilanso.

5 Nyumba ya Ufumu siifunika kumangidwa mwa maonekedwe adzaoneni ayi. Ngakhale kuti mamangidwe ake angakhale osiyana-siyana, colinga cake ni kukhala na malo osonkhanila oyenelela. (Mac. 17:24) Conco, imangofunika kukhala yooneka bwino komanso yoyenelela kucitilamo misonkhano yacikhristu.

6 Mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova umacita zopeleka zothandiza kukonza na kusamalila Nyumba ya Ufumu imene amasonkhanamo. Sipakhala kupititsamo mbale ya pelekani-pelekani, kapena kupemphetsa ndalama ayi. M’malomwake, pamaikidwa kabokosi ka zopeleka kuti aja obwela kudzasonkhana, mwa ufulu wawo, aziponyamo zopeleka zothandizila kusamalila Nyumba ya Ufumu. Amapeleka mwa kufuna kwawo komanso mocokela pansi pa mtima.—2 Akor. 9:7.

7 Onse mumpingo amaona kuti ni mwayi waukulu kucita zopeleka zothandiza kusamalila Nyumba ya Ufumu, kuti izikhala yaukhondo komanso yosamalidwa bwino. Cina, pamasankhidwa mkulu kapena mtumiki wothandiza kuti azikonza ndandanda yoyeletsa Nyumba ya Ufumu. Kaŵili-kaŵili, pulogilamu imeneyi imandandalika tumagulu twaulaliki, ndipo woyang’anila kagulu kapena wothandizila wake ndiye amatsogolela nchitoyo. Mkati na kunja komwe, maonekedwe a Nyumba ya Ufumu ayenela kupeleka ulemu kwa Yehova na gulu lake.

Onse mumpingo amauona kukhala mwayi waukulu kupanga zopeleka zothandizila pa zofunikila za Nyumba ya Ufumu yawo, kutinso izikhala yoyela komanso yosamalika bwino

8 Ngati pa Nyumba ya Ufumu pamasonkhana mipingo ingapo, akulu a mipingoyo amakhazikitsa Komiti Yosamalila Nyumba ya Ufumu. Ndiyo imayang’anila nchito zosamalila Nyumba ya Ufumuyo na malo ake. Mabungwe a akulu amasankha mkulu amene angatumikile monga mgwilizanitsi wa komitiyo. Pansi pa uyang’anilo wa mabungwe a akulu, komiti yosamalila nyumba ya ufumu imayang’anila nchito yoyeletsa holo, kuonetsetsa kuti zonse zili bwino, komanso kuti zofunikila zonse zilipo. Izi zimafuna mgwilizano wabwino wa mipingo yokhudzidwa.

9 Ngati mipingo ingapo imaseŵenzetsa Nyumba ya Ufumu imodzi, ikhoza kumasinthana nthawi yosonkhana. Akulu ayenela kukambilana na kukonza ndondomeko ya masonkhanidwe mwacikondi komanso moganizilana. (Afil. 2:2-4; 1 Pet. 3:8) Pasapezeke mpingo wokonzela anzawo pulogilamu ya kasonkhanidwe. Pamene woyang’anila dela acezela mpingo umodzi, mipingo inayo iyenela kusintha nthawi zosonkhana mlungu umenewo.

10 Nyumba ya Ufumu ingagwilitsilidwe nchito kukambilamo nkhani ya cikwati kapena ya malilo, mwa cilolezo ca Komiti ya Utumiki ya Mpingo. Akulu a m’komiti imeneyi akalandila pempholo, amaiganizila mosamala nkhaniyo na kupanga cigamulo motsatila malangizo a ofesi ya nthambi.

11 Amene amaloledwa kuseŵenzetsa Nyumba ya Ufumu pa zocitika ngati zimenezi, ayenela kucita zinthu mwa njila yolinga Akhristu. Pa Nyumba ya Ufumu pasacitike zinthu zimene zingakhumudwitse mpingo kapena kubweletsa citonzo pa dzina la Yehova, na kuwononga mbili yabwino ya mpingo. (Afil. 2:14, 15) Mwa citsogozo ca ofesi ya nthambi, Nyumba ya Ufumu ingagwilitsidwenso nchito pa zocitika zina zauzimu, monga Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, kapena Sukulu ya Apainiya.

12 Nthawi zonse mpingo uyenela kulemekeza malo olambilila. Mavalidwe, kudzikongoletsa, na zocita zathu ziyenela kukhala zaulemu woyenelela anthu olambila Yehova. (Mlal. 5:1; 1 Tim. 2:9, 10) Ngati ticita zimenezi, tidzaonetsa kuti timayamikiladi misonkhano yathu yacikhristu.

13 Misonkhano iyenela kucitika popanda zosokoneza. Ana ayenela kukhala pamodzi na makolo awo. Makolo omwe ali na ŵana aang’ono, ayenela kukhala pa malo amene sangasokoneze ena pofuna kutuluka kuti akadzudzule mwana wosokoneza, kapena kuthandiza mwana mwa njila zina.

14 Abale oyenelela amatumikila monga akalinde pa Nyumba ya Ufumu. Ayenela kukhala achelu, aubwenzi, komanso oganiza bwino. Udindo wawo umaphatikizapo kulandila bwino alendo na kuwathandiza kukhala omasuka, kuthandiza obwela mocedwa kupeza malo okhala, kutenga ciŵelengelo ca osonkhana, komanso kuonetsetsa kuti mu Nyumba ya Ufumu mukuloŵa mphepo yokwanila, kapena mukuthuma bwino. Kukakhala kofunikila, akalinde angapemphe makolo kusamalila bwino ana awo kuti asamacite mpishu-pishu kapena kuthamanga-thamanga misonkhano ili mkati kapena ikangotha, kapenanso kuseŵelela kupulatifomu. Mwaulemu komanso mosamala, akalinde angapemphe kholo la mwana amene akuvuta kuti atuluke naye panja kuti asasokoneze ena omvetsela. Nchito ya akalinde imathandiza kuti aliyense apindule na misonkhano. Akulu na atumiki othandiza ndiwo ali pamalo abwino kwambili kutumikila monga akalinde.

KUMANGA NYUMBA ZA UFUMU

15 M’zaka za zana loyamba, Akhristu ena anali opata bwino zakuthupi kuposa ena. Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo anawalembela kuti: “Ndikufuna kuti zoculuka zimene muli nazo zithandizile pa zimene iwowo akusoŵa, ndipo zoculuka zimene iwowo ali nazo zithandizile pa zimene inuyo mukusoŵa, kuti pakhale kufanana.” (2 Akor. 8:14) Masiku anonso, timayesetsa kuti “pakhale kufanana.” Ndalama zimene mipingo imapeleka padziko lonse, zimapita kuthumba limodzi kuti zizithandiza panchito yomanga na kukonza Nyumba za Ufumu. Gulu lathu komanso mipingo yonse imene imalandila thandizo la ndalama zimenezi, imayamikila kuwolowa manja kwa abale athu padziko lonse.

16 Ofesi ya nthambi ndiyo imagaŵila Nyumba za Ufumu ku mipingo. Ni imenenso imasankha malo omangapo Nyumba za Ufumu, kapena kuona zofunikila kukonzanso. Pakagwa ngozi zamwadzidzidzi, ofesi ya nthambi imapanga makonzedwe akuti Nyumba za Ufumu zikonzedwe, ngakhalenso nyumba za abale nthawi zina.

17 Ofesi ya nthambi ndiyo imayang’anila abale odzipeleka kuthandizila nchito monga kugula malo, kulemba mapulani a Nyumba za Ufumu, kutenga zilolezo ku boma, kumanga, na kukonza zowonongeka. Cifukwa ca kucepa kwa Nyumba za Ufumu m’maiko ambili, pakufunika anchito odzipeleka ambili. Ofalitsa onse obatizika oyenelela ofuna kuthandizako pa nchito imeneyi, akulimbikitsidwa kulemba fomu yofunsila utumiki umenewu, na kupatsila Komiti ya Utumiki ya Mpingo wawo. Ngakhale ofalitsa osabatizika angathandize pa nchito yomanga kapena kukonzanso Nyumba yawo ya Ufumu.

MABWALO A MISONKHANO

18 Akhristu a m’nthawi ya atumwi kambili anali kusonkhana m’magulu ang’ono-ang’ono. Koma nthawi zina anali kusonkhana “anthu ambili-mbili.” (Mac. 11:26) Masiku anonso, anthu a Yehova amasonkhana ambili pa misonkhano yadela kapena yacigawo. Nthawi zambili timacita lendi malo ocitilapo misonkhano imeneyi. Koma kumene kulibe malo otelo oyenelela, timadzimangila tekha malo athu olambilila ochedwa Mabwalo a Misonkhano.

19 Nthawi zina timagula cimango cimene cilipo kale, n’kucikonzanso kukhala Bwalo la Misonkhano. Koma nthawi zambili, timagula malo na kumangapo bwalo losonkhanamo. Mabwalo a Misonkhano amasiyana-siyana ukulu wake, potengela zofunikila kumaloko. Ofesi ya nthambi imapeleka cilolezo cogula cimango coteloco, kapena kudzimangila cathu, kokha pambuyo poŵelengela bwino-bwino ndalama zimene zingafunikile, komanso kuona ngati cimangoco cizigwilitsidwa nchito mokwanila.

20 Ofesi ya nthambi ndiyo imasankha m’bale woyang’anila Bwalo la Misonkhano. Pamakhalanso makonzedwe akuti mipingo ya m’delalo izikayeletsa malo amenewa nthawi na nthawi, komanso kukakonza zinthu zina. Cimakhala coyamikilika ngako ngati abale na alongo adzipeleka kukagwila nchito imeneyi. Conco, mipingo ikulimbikitsidwa kucilikiza makonzedwe amenewa na mtima wonse.—Sal. 110:3; Mal. 1:10.

21 Nthawi zina, Mabwalo a Misonkhano angagwilenso nchito pa zocitika zina zauzimu, monga Masukulu ophunzitsa Baibo, komanso mamiting’i a oyang’anila madela. Mofanana na Nyumba ya Ufumu, nawonso Mabwalo a Misonkhano ni malo olambilila opatulika. Tikasonkhana pa Bwalo la Misonkhano, zocita zathu, mavalidwe, na kudzikongoletsa kwathu, ziyenela kukhala zaulemu monga zimakhalila tikapita kukalambila ku Nyumba ya Ufumu.

22 M’ndime yothela ino ya masiku otsiliza, anthu ambili atsopano akufunitsitsa kubwela m’gulu la Mulungu. Uwu ni umboni wakuti Yehova akuikapodi dalitso lake. (Yes. 60:8, 10, 11, 22) Conco, tiyenela kucilikiza makonzedwe a kugula na kusamalila malo athu olambilila. Mwakutelo, timaonetsa ciyamiko cathu pokhala na malo amenewo, kumene timasonkhana kuti tilimbikitsane, maka-maka poona kuti tsiku la Yehova layandikila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani