LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 13 masa. 130-140
  • “Citani Zonse ku Ulemelelo wa Mulungu”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Citani Zonse ku Ulemelelo wa Mulungu”
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • TIKHALE OYELA KUUZIMU NA M’MAKHALIDWE
  • CIYELO CAKUTHUPI
  • ZOSANGULUTSA KAPENA ZOSANGALATSA
  • ZOCITIKA ZA KUSUKULU
  • NCHITO YAKUTHUPI NA MABWENZI
  • UMODZI WATHU WACIKHRISTU
  • Mulungu Amakonda Anthu Oyela
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Yehova Amafuna Anthu Ake Kukhala Oyela
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • “Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 13 masa. 130-140

MUTU 13

“Citani Zonse ku Ulemelelo wa Mulungu”

MONGA atumiki a Mulungu odzipatulila, tiyenela kuonetsa ulemelelo wa Yehova m’zokamba zathu na zocita zathu zonse. Mtumwi Paulo anapeleka malangizo otikumbutsa mfundo yofunika imeneyi. Anati: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukucita cina ciliconse, citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.” (1 Akor. 10:31) Izi ziphatikizapo kusunga miyezo ya Yehova yolungama, imene ni cisonyezelo ca makhalidwe ake. (Akol. 3:10) Inde, tiyenela kutengela makhalidwe ake a Mulungu kuti tikhale anthu oyela.—Aef. 5:1, 2.

2 Mtumwi Petulo nayenso anakumbutsa Akhristu mfundo yofunika imeneyi. Anawalembela kuti: “Monga ana omvela, lekani kukhala motsatila zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziŵa. Koma khalani motsanzila Woyela amene anakuitanani. Inunso khalani oyela m’makhalidwe anu onse, cifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.’” (1 Pet. 1:14-16) Monga zinalili kwa Aisiraeli akale, Akhristu onse ayenela kusunga ciyelo ca mpingo. Kutanthauza kuti ayenela kukhala opanda codetsa, osakhudzidwa na zocitika zaucimo za m’dzikoli. Inde, iwo anapatulidwa mwapadela kuti acite utumiki wopatulika.—Eks. 20:5.

3 Timasunga ciyelo potsatila malamulo na mfundo za Yehova, zofotokozedwa momveka bwino m’Malemba Oyela. (2 Tim. 3:16) Mwa kuphunzila Baibo, tinaphunzitsidwa za Yehova na njila zake, ndipo tinafika pomukonda kwambili. Tinaona kufunika kofuna-funa Ufumu wa Mulungu coyamba, na kucita cifunilo ca Yehova. Izi zinakhala zinthu zofunika kopambana mu umoyo wathu. (Mat. 6:33; Aroma 12:2) Kuti zimenezi zitheke, tinafunika kuvala umunthu watsopano.—Aef. 4:22-24.

TIKHALE OYELA KUUZIMU NA M’MAKHALIDWE

4 Kusunga miyezo ya Yehova yolungama kumakhala kovuta nthawi zina. Mdani wathu Satana Mdyelekezi, amakhala akufuna-funa njila zotipatutsila kucoka pa coonadi. Komanso cifukwa ca zokodola za dzikoli, kuphatikizapo kupanda ungwilo kwathu, zimakhala zotivuta nthawi zina. Kusunga lumbilo la kudzipatulila kwathu kumafuna kumenya nkhondo yauzimu. Malemba amatiuza kuti tisadabwe pokumana na citsutso kapena mayeso. N’zoona kuti tidzavutika cifukwa ca cilungamo. (2 Tim. 3:12) Koma tisataye cimwemwe cathu pokumana na mayeso, podziŵa kuti mayeso amenewo ni umboni wakuti tikucita cifunilo ca Mulungu.—1 Pet. 3:14-16; 4:12, 14-16.

5 Ngakhale Yesu amene, olo kuti anali wangwilo, anaphunzila kukhala womvela kupitila m’mavuto amene anakumana nawo. Ndipo iye sanagonjepo ku mayeselo a Satana, kapena kuyamba kukopeka na zokodola za dzikoli. (Mat. 4:1-11; Yoh. 6:15) Olo kungoganizilako cabe za kugonja, Yesu sanacitepo zimenezo. Ngakhale kuti dziko linadana naye cifukwa ca kukhulupilika kwake, iye anamamatilabe pa miyezo ya Yehova yolungama. Atatsala pang’ono kufa, Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti nawonso dziko lidzadana nawo. Kucokela panthawiyo, otsatila a Yesu akhala akukumana na masautso ambili-mbili, koma akhala olimba mtima podziŵa kuti Mwana wa Mulungu analigonjetsa dziko.—Yoh. 15:19; 16:33; 17:16.

6 Kuti tisakhale kumbali ya dziko, tiyenela kusungabe miyezo yolungama ya Yehova monga mmene Mbuye wathu anacitila. Cina, tisatengeko mbali m’ndale za dziko kapena m’nkhani za cikhalidwe ca dziko. Tipewenso kutengela makhalidwe onyansa a dzikoli. Tisautenge mopepuka uphungu wa pa Yakobo 1:21, wakuti: “Siyani khalidwe lililonse lonyansa ndiponso siyani khalidwe locita zoipa, lomwe ndi losafunika, ndipo vomelezani mofatsa mawu okhoza kupulumutsa miyoyo yanu, kuti abzalidwe mwa inu.” Kuphunzila Mawu a Mulungu na kupezeka kumisonkhano, kudzatithandiza ‘kuvomeleza mofatsa mawu’ a coonadi kukhala m’maganizo na m’mitima mwathu. Komanso sitidzakopeka na zokodola za dzikoli. Wophunzila wa Yesu, Yakobo, analemba kuti: “Kodi simukudziŵa kuti kucita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu? Conco, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.” (Yak. 4:4) Pa cifukwa ici, Baibo imatilangiza mwamphamvu za kufunika kosunga miyezo yolungama ya Yehova, na kukhalabe olekana nalo dzikoli.

7 Mawu a Mulungu amaticenjeza kuti tizipewa makhalidwe onyansa komanso ocititsa manyazi. Amati: “Dama ndi conyansa camtundu uliwonse kapena umbombo zisachulidwe n’komwe pakati panu, monga mmene anthu oyela amayenela kucitila.” (Aef. 5:3) Conco, tisalole maganizo athu kukhazikika pa zinthu zolaula, zamanyazi, kapena zonyansa. Ndipo poceza, tisalole ngakhale pang’ono kuti zinthu zotelozo ziloŵelele m’makambilano athu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti ndife ofunitsitsadi kusunga miyezo yolungama ya Yehova ya makhalidwe abwino.

CIYELO CAKUTHUPI

8 Kuwonjezela pa ciyelo cauzimu komanso ca makhalidwe, Akhristu ayenelanso kukhala oyela kuthupi. M’nthawi ya Aisiraeli, Mulungu wa ciyelo anafuna kuti mu msasa muzikhala mwaukhondo. Conco ifenso tiyenela kukhala aukhondo kuti Yehova “asaone coipa ciliconse” mwa ife. —Deut. 23:14.

9 Baibo imaonetsa kuti pali mgwilizano kwambili pakati pa ciyelo cauzimu na ukhondo. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Okondedwanu tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwanilitsa kukhala oyela poopa Mulungu.” (2 Akor. 7:1) Conco, amuna na akazi acikhristu ayenela kuyesetsa kusunga matupi awo ali oyela, mwa kusamba nthawi zonse na kucapa zovala zawo. Ngakhale kuti mikhalidwe imasiyana m’maiko osiyana-siyana, tiyenela kuyesetsa kupeza sopo yokwanila na madzi kuti tizisunga matupi athu ali oyela, na kuonetsetsa kuti ana athu naonso ni aukhondo.

10 Cifukwa ca nchito yathu yolalikila, ambili amatidziŵa ku madela akwathu. Nyumba zathu zikamakhala zaukhondo komanso zaudongo mkati na kunja komwe, zimapeleka umboni wabwino kwa anansi athu. Ndipo aliyense m’banja ayenela kutengapo gawo pambali imeneyi. Abalenso maka-maka afunika kuonetsetsa kuti nyumba zawo na pabwalo pomwe pazikhala polozeka. Inde, pazioneka paukhondo komanso posamalika bwino, cifukwa zimapeleka cithunzi cabwino kwa ena. Akamacita zimenezi, kuwonjezela pa kutsogolela mabanja awo pa zinthu zauzimu, amaonetsa kuti akuyang’anila bwino mabanja awo. (1 Tim. 3:4, 12) Alongo nawonso ali na udindo wosamalila panyumba, maka-makanso mkati. (Tito 2:4, 5) Ana ophunzitsidwa bwino nawonso amatengapo gawo lawo posamalila zipinda zawo kukhala zaudongo. Mwakutelo, banja lonse capamodzi limakonzekela makhalidwe aukhondo oyenelela m’dziko latsopano pansi pa Ufumu wa Mulungu.

11 Anthu a Yehova ambili masiku ano amaseŵenzetsa mamotoka popita ku misonkhano. Ndipo m’madela ena n’zosatheka kupita muulaliki popanda motoka. Conco, motoka nayonso iyenela kukhala yaukhondo komanso yokonzedwa bwino. Nyumba zathu na mamotoka athu ayenela kupeleka umboni wakuti tili mu gulu la Yehova la anthu aukhondo, komanso oyela. N’cimodzimodzinso na cola cathu ca ulaliki, komanso Baibo yathu.

12 Mavalidwe na kudzikongoletsa kwathu ziyenelanso kuyendelana na mfundo za m’Baibo. Kodi pokaonekela pamaso pa munthu wolemekezeka, tingavale mosasamala kapena motayilila? Kutali-tali! Koposa kotani nanga poimilako Yehova mu ulaliki kapena papulatifomu! Inde, mavalidwe athu na mmene timadzikonzela zingakhudze kwambili mmene anthu angaonele kulambila kwathu Yehova. Mmene timazikongoletsela komanso mavalidwe athu zimaonetsa ena mmene timaonela kulambila kwathu Yehova. Mwa ici, si cinthu canzelu kuvala motayilila kapena mosaganizila ena. (Mika 6:8; 1 Akor. 10:31-33; 1 Tim. 2:9, 10) Conco, kaya tikukonzekela kupita mu ulaliki, ku misonkhano ya mpingo, ku msonkhano wadela kapena wacigawo, tiyenela kuganizila zimene Malemba amakamba za ciyelo capathupi na kudzikongoletsa mwaulemu. Nthawi zonse ticite zinthu mopeleka ulemu na ulemelelo kwa Yehova.

Monga atumiki a Mulungu odzipatulila, timayembekezeka kuonetsa ulemelelo wa Yehova m’zokamba zathu, na zocita zathu zonse

13 N’cimodzimodzinso tikapita kukayendela likulu lathu la padziko lonse, kapena ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova. Tizikumbukila kuti dzina lakuti Beteli limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Conco, mavalidwe na makhalidwe athu azikhala monga tikupita ku misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu.

14 Ngakhale pa zocitika za cisangalalo, tiyenela kusamalabe na mavalidwe komanso kudzikongoletsa kwathu. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi mavalidwe aya siningacite nawo manyazi polalikila mwamwayi?’

ZOSANGULUTSA KAPENA ZOSANGALATSA

15 Umoyo wabwino ndiponso wathanzi umafuna kumapumulako na kusangulukako. Panthawi ina, Yesu anatenga ophunzila ake n’kupita nawo kumalo a kwa okha kuti ‘[akapumuleko] pang’ono’. (Maliko 6:31) Conco, kupumula na kucitako zosangulutsa kapena zosangalatsa kumatsitsimula. Kungatipatse nyonga zatsopano kuti tipitilize kugwila bwino nchito zathu za tsiku na tsiku.

16 Masiku ano kuli zosangulutsa zambili za mitundu-mitundu. Conco Akhristu ayenela kusankha mosamala pogwilitsila nchito nzelu zaumulungu. N’zoona kuti kusanguluka n’kofunika, koma kusakhale cinthu cacikulu paumoyo wathu. Timacenjezedwa kuti ‘m’masiku otsiliza’ anthu adzakhala “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Tim. 3:1, 4) Zambili zimene anthu amati zosangulutsa kapena zosangalatsa, zimakhala zosayenela kwa ife ofuna kusunga miyezo ya Yehova yolungama.

17 Akristu oyambilila anali kupewelatu zosangalatsa zoipa zimene anthu apanthawiyo anali kukonda. M’mabwalo a zamaseŵela ku Roma, anthu anali kusangalala kutamba anthu akuzunzidwa, akumenyana, kuphana, kukhadzulidwa na zilombo zolusa, komanso kucita ciwelewele pamaso pa openyelela. Koma Akhristu oyambilila anali kupewelatu zinthu zimenezi. Masiku anonso, zosangalatsa zambili zimaphatikizamo zinthu zimene anthu a makhalidwe oipa amakonda. Conco, tiyenela kukhala ‘osamala kwambili’ kuti tipewe zosangalatsa zoipa.(Aef. 5:15, 16; Sal. 11:5) Ndipo ngakhale zosangalatsazo zingakhale zabwino-bwino pa izo zokha, zingakhalebe zosayenelela kwa Mkhristu cifukwa ca malo ake, zinthu zina zophatikizidwamo, ngakhalenso anthu oloŵetsedwamo.—1 Pet. 4:1-4.

18 Zilipo zosangulutsa komanso zosangalatsa zimene Akhristu angakondwele nazo. Cathandiza Akhristu ambili ni kutsatila uphungu wa m’Malemba na malangizo a m’zofalitsa othandiza kusankha bwino, na kucita zinthu mwacikatikati.

19 Nthawi zina, mabanja angapo angaitanidwe kupita kumaceza kunyumba kwa Mkhristu. Kapenanso abale na alongo angaitanidwe ku phwando la ukwati, kapenanso ku zocitika zina za cisangalalo. (Yoh. 2:2) Oceleza alendo pazisangalalo zimenezo ndiwo ali na udindo woonetsetsa kuti zonse zikucitika moyenelela. Conco, m’pofunika kukhala osamala kwambili pamene tiitana anthu oculuka ku zocitika zimenezi. N’zacisoni kuti ena atayilila n’kuyamba kuonetsa makhalidwe osayenela kwa Akhristu, monga kudya na kumwa mopitilila muyeso. Ngakhalenso kugwela m’zolakwa zazikulu. Pa cifukwa cimeneci, Akhristu ozindikila aona kuti n’cinthu canzelu kucepetsako anthu owaitanila, komanso utali wa nthawi ya zisangalalo zimenezo. Ngati padzakhala moŵa, amene amwamwako akamwe mwacikatikati, osati mopitilila malile. (Afil. 4:5) Kuti maceza anu akakhale olimbikitsa komanso otsitsimula mwauzimu, musaike maganizo anu onse pa kukonzekela zakudya na zakumwa.

20 Kuceleza alendo ni cinthu cabwino ngako. (1 Pet. 4:9) Koma poitanila Akhristu anzathu kunyumba kwathu ku cakudya, zakumwa, zosangulutsa, kapena maceza cabe, tisaiŵale kuphatikizapo aja osaukilapo. (Luka 14:12-14) Ndipo ngati ndife oitanidwa ku zocitika zimenezo, tisamale kuti khalidwe lathu lisasemphane na uphungu wa pa Maliko 12:31. Ni bwino nthawi zonse kumayamikila cisomo cimene anthu ationetsa.

21 Akhristufe timakondwela na mphatso zocokela kwa Mulungu podziŵa kuti tingadye, kumwa, na kusangalala na zinthu zabwino, cifukwa cogwila nchito molimbika. (Mlal. 3:12, 13) Ngati ticita “zonse ku ulemelelo wa Mulungu,” ife oceleza pamodzi na alendo athu, tonse tingayang’ane kumbuyo na cikumbumtima coyela ku maceza omwe tinali nawo otsitsimula mwauzimu.

ZOCITIKA ZA KUSUKULU

22 Ana a Mboni za Yehova amapindula na maphunzilo a kusukulu. Pamene apita kusukulu, amakhala na cidwi cofuna kuphunzila kuŵelenga na kulemba bwino. Maphunzilo ena a kusukulu amawathandiza acicepele ngakhale pa zolinga zawo zauzimu. Pamene ali kusukulu, iwo amayesetsa ‘kukumbukila Mlengi wawo Wamkulu’ mwa kuika zinthu zauzimu patsogolo.—Mlal. 12:1.

23 Ngati ndimwe Mkhristu wacinyamata amene muli pasukulu, samalani kuti musamayanjane kwambili na acinyamata akudziko. (2 Tim. 3:1, 2) Yehova wapeleka zocita zambili zokutetezani ku zokodola za dzikoli. (Sal. 23:4; 91:1, 2) Conco, kuti mukhale wotetezeka, tengelani mwayi wocita zimene Yehova wakupatsani.—Sal. 23:5.

24 Pofuna kukhala olekana nalo dziko pamene ali kusukulu, acinyamata a Mboni amapewa kutengako mbali m’zocitika zina zimene si mbali ya maphunzilo. Izi zingakhale zovuta kwa anzawo a m’kalasi kumvetsa, ngakhale kwa aphunzitsi amene. Koma cacikulu n’kukondweletsa Mulungu. Conco, cikumbumtima canu cophunzitsidwa Baibo ciyenela kukuthandizani kupewa mzimu wa dziko wa mpikisano, komanso uja wa ‘konda dziko lako.’ (Agal. 5:19, 26) Ndipo pomvela uphungu wa m’Malemba wa makolo anu oopa Mulungu, na kupeza mabwenzi abwino mumpingo, acinyamatanu mungakwanitse ndithu kusunga miyezo ya Yehova yolungama.

NCHITO YAKUTHUPI NA MABWENZI

25 Mitu ya mabanja ili na udindo wa m’Malemba wosamalila a m’banja lawo. (1 Tim. 5:8) Ngakhale n’telo, pokhala atumiki a Mulungu, iwo amadziŵa kuti ayenela kutsogoza Ufumu wa Mulungu m’malo mwa nchito yawo yakuthupi. (Mat. 6:33; Aroma 11:13) Iwo angapewe nkhawa za moyo na msampha wokonda cuma ngati aika patsogolo kupembedza Mulungu, ndiponso kukhala okhutila na cakudya komanso zovala zimene ali nazo.—1 Tim. 6:6-10.

26 Akhristu odzipatulila onse ogwila nchito zakuthupi ayenela kukumbukila mfundo za m’Malemba. Popezela mabanja athu zofunikila, tiyenela kucita zinthu mwacilungamo, na kupewa njila zophwanya malamulo a Mulungu kapena a boma. (Aroma 13:1, 2; 1 Akor. 6:9, 10) Tiyenela kukumbukila kuwopsa kwa mayanjano oipa. Monga asilikali a Khristu, timapewa malonda osemphana na miyezo ya Mulungu, kapena okhudzana n’zandale. (Yes. 2:4; 2 Tim. 2:4) Timapewanso ciliconse cogwilizana na mdani winanso wa Mulungu, “Babulo Wamkulu.”—Chiv. 18:2, 4; 2 Akor. 6:14-17.

27 Kutsatila miyezo ya Mulungu yolungama, kudzatithandiza kupewa kutengela mwayi misonkhano yathu kutsatsilapo malonda kapena zinthu zina za phindu laumwini. Colinga cacikulu cokumanila pamodzi kumisonkhano ya mpingo, yadela komanso yacigawo, si cina ayi koma kulambila Yehova. Timakhala tikulandila cakudya pathebulo lauzimu, na ‘kulimbikitsana’ wina na mnzake.’ (Aroma 1:11, 12; Aheb. 10:24, 25) Conco, pamayanjano otelowo payenela kucitika zinthu zauzimu zokha-zokha.

UMODZI WATHU WACIKHRISTU

28 Kutsatila miyezo ya Yehova yolungama kumathandizanso anthu ake ‘kusunga umodzi wawo mwa mzimu, na mtendele monga comangila coŵagwilizanitsa.’ (Aef. 4:1-3) Aliyense amayesetsa kucitila anthu ena zabwino, m’malo modzikondweletsa yekha. (1 Ates. 5:15) Mosakaika konse, ndiwo mzimu umene munapeza mumpingo mwanu. Kaya tikhale a fuko lanji, mtundu uti, dziko liti, olemela kapena osauka, ophunzila kapena osaphunzila, tonsefe timayendela mfundo zolungama zimodzimodzi. Ngakhale anthu akunja amadzionela okha mgwilizano umenewu pakati pa anthu a Yehova.—1 Pet. 2:12.

29 Pofotokoza maziko a mgwilizano wa Akhristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pali thupi limodzi ndi mzimu umodzi, mogwilizana ndi ciyembekezo cimodzi cimene munaitanidwila. Palinso Ambuye mmodzi, cikhulupililo cimodzi, ubatizo umodzi, ndi Mulungu mmodzi amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse ndipo amacita zinthu kudzela mwa onse ndiponso mphamvu yake imagwila nchito mwa onse.” (Aef. 4:4-6) Kuti umodzi umenewu utheke, m’pofunikanso kugwilizana pa kamvedwe ka ziphunzitso zikulu-zikulu zoyambilila za m’Baibo, komanso mfundo zina zozamilapo zotithandiza kuzindikila ulamulilo wa Yehova. Inde, Yehova wapatsa anthu ake cinenelo coyela ca coonadi kuti am’tumikile mogwilizana.—Zef. 3:9.

30 Mgwilizano komanso mtendele wa mpingo wacikhristu umapeleka citsitsimulo kwa alambili onse a Yehova. Taona kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti: “Ndidzawabweletsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola.” (Mika 2:12) Colinga cathu n’cakuti titeteze mgwilizano wathu wamtendele mwa kusunga miyezo ya Yehova yolungama.

31 Alidi odala awo amene alandilidwa mumpingo woyela wa Yehova! Kudziŵika na dzina la Yehova ni mwayi umene timakhala okonzeka kutailapo cililconse. Pofuna kusunga ubale wathu wamtengo wapatali na Yehova, tidzacita zonse zotheka kuti tisungebe miyezo yake yolungama, na kuuzakonso ena miyezo imeneyo.—2 Akor. 3:18.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani