LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 14 masa. 141-156
  • Kusunga Mtendele na Ciyelo ca Mpingo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kusunga Mtendele na Ciyelo ca Mpingo
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUTHETSA NKHANI ZING’ONO-ZING’ONO
  • KUPELEKA UPHUNGU WA M’MALEMBA
  • KUIKA CIZINDIKILO ANTHU OYENDA MOSALONGOSOKA
  • KUSAMALILA ZOLAKWA ZAZIKULU
  • KUSAMALILA ZOLAKWA ZIKULU-ZIKULU
  • KULENGEZA CIDZUDZULO
  • NGATI CIGAMULO N’CAKUTI ACOTSEDWE
  • CILENGEZO CA KUCOTSEDWA
  • KUDZILEKANITSA
  • KUBWEZELETSA MUNTHU MUMPINGO
  • CILENGEZO CA KUBWEZELETSA
  • NKHANI ZOKHUDZA ANA OBATIZIKA
  • WOFALITSA WOSABATIZIKA AKAGWELA M’CHIMO
  • YEHOVA AMADALITSA ANTHU OMULAMBILA MWAMTENDELE KOMANSO MWACIYELO
  • Mmene Akulu Amaonetsela Cikondi na Cifundo Kwa Munthu Wocita Chimo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Mmene Akulu Angathandizile Amene Anacotsedwa Mumpingo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 14 masa. 141-156

MUTU 14

Kusunga Mtendele na Ciyelo ca Mpingo

CAKA NA CAKA, anthu masauzande amakhamukila kunyumba ya Yehova ya kulambila koyela, pokwanilitsa ulosi wa m’Baibo. (Mika 4:1, 2) Ndipo timakhala okondwa kuwalandila na manja aŵili mu “mpingo wa Mulungu”! (Mac. 20:28) Iwo amayamikila mwayi wotumikila Yehova pamodzi nafe, ndiponso amasangalala na paradaiso wathu wauzimu woyela komanso wamtendele. Mzimu woyela wa Mulungu, na malangizo anzelu opezeka m’Mawu ake, zimatithandiza kusungabe mtendele na ciyelo mumpingo.—Sal. 119:105; Zek. 4:6.

2 Timavala “umunthu watsopano” mwa kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo. (Akol. 3:10) Sitilola kuti nkhani zing’ono-zing’ono, kapena kusemphana maganizo kusokoneze mgwilizano wathu. Potengela citsanzo ca Yehova copanda tsankho, tidzapewa mzimu wa dziko wa magaŵano. M’malomwake, tidzatumikila Mulungu wathu mogwilizana paubale wathu wa padziko lonse.—Mac. 10:34, 35.

3 Ngakhale n’telo, mavuto amabukabe nthawi zina amene angasokoneze mtendele na mgwilizano wa mpingo. Kodi cimapangitsa n’ciani? Kambili, kumakhala kulephela kuseŵenzetsa uphungu wa m’Baibo. Cina, tonse tili na zifooko zathu cifukwa copanda ungwilo. Palibe aliyense amene ni wangwilo. (1 Yoh. 1:10) Wina angagwele m’colakwa na kusokoneza ciyelo ca mpingo. Mwinanso tingakhumudwitse munthu wina polankhula kapena kucita zinthu mosaganiza bwino. Kapenanso ife amene tingakhumudwe na zimene munthu wina wakamba kapena kucita. (Aroma 3:23) Kodi zimenezi zikacitika, tiyenela kutani kuti tisungitse mtendele?

4 Yehova mwa cikondi cake, anapeleka njila zothetsela mavuto onsewa. M’Mawu ake Baibo, muli uphungu wabwino woyanjanitsa anthu pakabuka mavuto. Komanso akulu monga abusa acikondi, amathanso kupeleka thandizo kwa aliyense. Mwa kuseŵenzetsa uphungu wawo wa m’Malemba, timatha kukhalanso paubale wabwino na ŵena, n’kukhalabe na kaimidwe kabwino pamaso pa Yehova. Ngati tapatsidwa cilango kapena cidzudzulo pa colakwa cimene tinacita, tidziŵe kuti ni Atate wathu wakumwamba amene akutiwongolela cifukwa cotikonda.—Miy. 3:11, 12; Aheb. 12:6.

KUTHETSA NKHANI ZING’ONO-ZING’ONO

5 Nthawi zina mumpingo mungabuke mavuto ang’ono-ang’ono kapena kusemphana maganizo pakati pa Akhristu. Zimenezi ziyenela kuthetsedwa m’mangu-m’mangu mwa cikondi capaubale. (Aef. 4:26; Afil. 2:2-4; Akol. 3:12-14) Mudzapeza kuti mavuto amene angabuke pakati pa imwe na Mkhristu mnzanu, kambili angathetsedwe pogwilitsila nchito uphungu wa mtumwi Petulo wakuti, “khalani okondana kwambili, pakuti cikondi cimakwilila macimo oculuka.” (1 Pet. 4:8) Baibo imanena kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambili.” (Yak. 3:2) Potsatila mfundo yopambana imeneyi, yocitila ena zonse zimene tingafune kuti iwo aticitile, nthawi zambili tikhoza kungokhululukilana zolakwa zing’ono-zing’ono na kuziiŵala.—Mat. 6:14, 15; 7:12.

6 Ngati mwazindikila kuti wina anakhumudwa na zimene munakamba kapena kucita, musacedwe kucitapo kanthu kuti mukhazikitse mtendele. Kumbukilani kuti zimenezi zimakhudzanso ubale wanu na Yehova. Yesu anapatsa ophunzila ake uphungu wakuti: “Ngati wabweletsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba, ndipo ukabwelako, peleka mphatso yako.” (Mat. 5:23, 24) N’kutheka kuti munangomvana molakwa. Conco, si cinthu canzelu kuleka kukambitsana, cifukwa sindiwo mankhwala. Ndipo ngati tonse timakambilana momasuka mumpingo, zimatithandiza kuti pasakhale kuganizilana molakwa. Ndiponso, sicidzakhala covuta kwambili kuthetsa mavuto amene amabuka cifukwa ca kupanda ungwilo kwathu.

KUPELEKA UPHUNGU WA M’MALEMBA

7 Nthawi zina, oyang’anila angaone kuti m’pofunikila kupeleka uphungu kuti athandize munthu pa maganizo ake olakwika. Koma nthawi zina zimakhala zovuta. Mtumwi Paulo analembela Akhristu a ku Galatiya kuti: “Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowela njila yolakwika mosazindikila, inu oyenelela mwauzimu, yesani kumuthandiza munthu woteloyo ndi mzimu wofatsa.”—Agal. 6:1.

8 Mwa kuweta nkhosa, oyang’anila angateteze mpingo ku zoopsa zambili zauzimu, na kuthandiza kuti pasamabuke mavuto aakulu. Akulu amayesetsa kuti utumiki wawo mumpingo uzikwanilitsa lonjezo la Yehova kupitila mwa Yesaya lakuti: “Aliyense adzakhala ngati malo obisalilapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.”—Yes. 32:2.

KUIKA CIZINDIKILO ANTHU OYENDA MOSALONGOSOKA

9 Mtumwi Paulo anacenjeza za anthu ena amene angakhale cisonkhezelo coipa mumpingo. Analemba kuti: “Tsopano tikukulangizani abale . . . kuti mupewe m’bale aliyense woyenda mosalongosoka komanso mosagwilizana ndi mwambo umene tinakupatsani.” Kenako anamveketsa bwino mfundoyi ponena kuti: “Ngati wina sakumvela mawu athu a m’kalatayi, muikeni cizindikilo ndipo lekani kucitila naye zinthu limodzi, kuti acite manyazi. Komabe musamuone monga mdani, koma pitilizani kumulangiza monga m’bale.”—2 Ates. 3:6, 14, 15.

10 Nthawi zina, munthu angakhale kuti sanacite chimo limene lingamucotsetse mu mpingo, koma akuonetsa makhalidwe onyozela miyezo ya Mulungu yotsogolela umoyo wacikhristu. Zingaphatikizepo ulesi wocita kunyanya nawo, mzimu wokonda kusuliza, komanso uve kapena kuti ucisi. Angakhalenso wokonda ‘kuloŵelela nkhani zimene sizikum’khudza.’ (2 Ates. 3:11) Mwinanso angakhale wokonda kudyela ena masuku pa mutu, kapena wokonda zosangalatsa zodziŵikilatu kuti n’zosayenela Akhristu. Kuyenda mosalongosoka ni kuja kumene kungaipitse dzina la mpingo, ndipo kukhoza kuyambukila Akhristu ena.

11 Coyamba, akulu adzayesa kum’thandiza munthu woyenda mosalongosokayo mwa kum’patsa uphungu wocokela m’Baibo. Koma ngati iye apitiliza kunyozela mfundo za m’Baibo, pambuyo pothandizidwa mobweleza-bweleza, akulu angagamule kuti papelekedwe nkhani yocenjeza mpingo. Koma kuti nkhaniyo ikambidwe, coyamba akuluwo ayenela kugwilitsila nchito luntha la kuzindikila, pofuna kuona ngati khalidwelo lafikadi pokula msinkhu cakuti ena akukhumudwa nalo. Wokamba nkhaniyo apeleke uphungu woyenelela wodzudzula khalidwelo, koma asachule dzina la munthu woyenda mosalongosokayo. Zikatelo, aja oidziŵa nkhaniyo adzayamba kupewa kuceza naye munthu wa khalidwe limenelo, ngakhale kuti adzapitiliza kuyanjana naye mwauzimu, ndiko “kumulangiza monga m’bale.”

12 Pamakhala ciyembekezo cakuti ngati Akhristu okhulupilika acita zimenezi kwa munthu woyenda mosalongosoka, iye angacite manyazi ndipo angasinthe khalidwe lakelo. Koma ngati zacita kuonekelatu kuti iye wasankha ndithu kuleka kuyenda molongosoka, palibe cifukwa comuonelanso monga woikidwa cizindikilo cabe.

KUSAMALILA ZOLAKWA ZAZIKULU

13 Ngakhale kuti tiyenela kunyalanyaza na kukhululuka zolakwa, sizitanthauza kuti timazilekelela kapena kuzivomeleza. Si zolakwa zonse zimene zimacitika cifukwa ca kupanda ungwilo; ndipo sitinganyalanyale zolakwa zikulu-zikulu. (Lev. 19:17; Sal. 141:5) Pangano la Cilamulo linaonetsa kuti macimo ena ni aakulu kuposa ena. N’cimodzi-modzinso mumpingo wacikhristu.—1 Yoh. 5:16, 17.

14 Yesu anapeleka ndondomeko yothetsela mavuto aakulu akabuka pakati pa Akhristu. Taonani masitepu amene anapeleka: “Ngati m’bale wako wacimwa, [1] upite kukam’fotokozela colakwaco panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvela, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo. Koma akapanda kukumvela, [2] upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena aŵili, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziŵili kapena zitatu. Akapanda kuwamvela amenewanso, [3] uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvela mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wocokela mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.”—Mat 18:15-17.

15 Poona citsanzo cimene Yesu anapeleka pa Mateyu 18:23-35, zikuoneka kuti macimo otanthauzidwa pa Mateyu 18:15-17, amaphatikizapo nkhani zokhudza ndalama kapena katundu wa munthu, monga kulephela kubweza nkhongole, kapena kucita cinyengo. Komanso ingakhale misece, imene imawononga mbili ya munthu.

16 Ngakhale mutakhala na umboni wakuti wina mumpingo wakucimwilani mwa iliyonse ya njila zimenezi, musathamangile kupempha akulu kuti aloŵelelepo ayi. Monga mwa malangizo a Yesu, coyamba kambilanani na munthu amene muli naye cifukwayo. Yesani kuithetsa nkhaniyo pakati pa inu aŵili popanda kuloŵetsapo wina aliyense. Kumbukilani, Yesu sanakambe kuti ‘upite kamodzi kokha kukam’fotokozela colakwaco’ ayi. Conco, ngati munthuyo sanavomeleze colakwa cake na kupempha cikhululuko paulendo woyamba, zingakhale bwino kukapitakonso ulendo wina. Ngati nkhaniyo ingathetsedwe mwa njila imeneyi, wocimwayo angayamikile kwambili mukapanda kuuzako ena za colakwa cake posafuna kumuipitsa mbili mumpingo.” Mukatelo, ndiye kuti ‘mwabweza m’bale wanu.’

17 Ngati wolakayo wavomeleza kulakwa kwake, ndipo wapempha cikhululukilo, na akucitapo kanthu kuti awongolele, palibe cifukwa coipitilizila nkhaniyo. Ngakhale kuti colakwaco n’cacikulu, colakwa ca mtundu umenewu cingathetsedwe pakati pa okhudzidwawo.

18 Ngati zalepheleka kum’bweza m’bale wanu pom’fotokozela colakwaco ‘panokha inu ndi iye,’ pamenepo mungacite zimene Yesu anakamba, ‘mukapiteko na munthu wina mmodzi kapena aŵili,’ kuti mukakambenso na m’bale wanuyo. Nawonso amene mwapita nawo azikhala na colinga cobweza m’baleyo. Zimakhala bwino kutenga amene ali mboni pa colakwaco. Koma ngati palibe mboni zoona na maso, mungapemphe munthu mmodzi kapena aŵili kuti akakhale mboni za makambilano anu. Iwo angakhalepo na cidziŵitso pankhani zotelo, moti mwina angathandize kutsimikizila ngati zimene zinacitikazo zinalidi zolakwika. Ngati amene apemphedwa kukakhala mboni ni akulu, iwo sakuimilako mpingo pankhaniyo, cifukwa sanatumidwe na bungwe la akulu kukasamalila mbali imeneyo.

19 Ngati nkhaniyo siikuthabe pambuyo poyesetsa mobweleza-bweleza—munayesetsa kukambilana naye panokha, kenako munatengelako munthu mmodzi kapena aŵili—ndipo muona kuti nkhaniyo simungangoiiŵala, pamenepo kaituleni kwa akulu a mpingo. Kumbukilani kuti colinga cawo ni kusungitsa mtendele na ciyelo ca mpingo. Conco mukawatulila akulu nkhaniyo, isiyeni m’manja mwawo na kuika cidalilo mwa Yehova. Musalole kuti zocita za munthu wina zikupunthwitseni, kapena kukulandani cimwemwe canu mu utumiki wanu kwa Yehova.—Sal. 119:165.

20 Abusa oyang’anila nkhosa adzaifufuza nkhaniyo. Zikatsimikizika kuti munthuyo anakucimwilanidi kwakukulu, ndipo ni wosalapa posafuna kucitapo kanthu kuti awongole zinthu, komiti ya oyang’anila ingaone kuti palibe kucitila mwina koma kum’cotsa mu mpingo munthuyo. Angacite zimenezo pofuna kuteteza nkhosa na kusungitsa ciyelo ca mpingo—Mat. 18:17.

KUSAMALILA ZOLAKWA ZIKULU-ZIKULU

21 Milandu ikulu-ikulu, monga ciwelewele, cigololo, mathanyula, kunyozela Mulungu, mpatuko, kupembedza mafano, na macimo ena akulu-akulu, si nkhani zimene munthu mmodzi akhoza kungozikhululuka basi zatha ayi. (1 Akor. 6:9, 10; Agal. 5:19-21) Popeza macimo aakulu otelewa angawononge ciyelo ca mpingo, afunika kuwacitila lipoti kwa akulu, cifukwa ndiwo oyenelezedwa kuwasamalila. (1 Akor. 5:6; Yak. 5:14, 15) Anthu ena angapite kwa akulu kukaulula okha chimo lawo, kapena kukamang’ala zimene akudziŵa pa zolakwa za ena. (Lev. 5:1; Yak. 5:16) Mulimonse mmene akulu angalandilile malipoti a colakwa cacikulu ca Mboni yobatizika, akulu aŵili ayenela kuifufuza nkhaniyo coyamba. Ngati kwapezeka kuti chimolo linacitikadi ndipo umboni ulipo wotsimikizila nkhaniyo, bungwe la akulu lidzasankha komiti yaciweluzo ya akulu osacepela atatu kuti aisamalile.

22 Abusa amayang’anila nkhosa mwachelu kwambili, pofuna kuziteteza kwa anthu amene angaziwononge mwauzimu. Amaseŵenzetsanso Mawu a Mulungu mwaluso kudzudzula olakwa, pofuna kuwathandiza kuti abwezeletse thanzi lawo lauzimu. (Yuda 21-23) Ndiwo malangizo amene mtumwi Paulo anapatsa Timoteyo polemba kuti: “Pamaso pa Mulungu ndi pa Khristu Yesu, amene anaikidwilatu kudzaweluza amoyo ndi akufa, . . . Dzudzula, tsutsa, dandaulila. Cita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambili.” (2 Tim. 4:1, 2) Kucita zimenezi kungatenge nthawi yaikulu, koma ni mbali imodzi mwa nchito zovuta zimene akulu amagwila. Ndipo mpingo umayamikila kudzipeleka kwawo, n’cifukwa cake amawaona kukhala oyenela ‘kupatsidwa ulemu waukulu.’—1 Tim. 5:17.

23 Nthawi zonse munthu akapezeka kuti ni wolakwa, colinga ca akulu cimakhala kubwezeletsa wolakwayo ku thanzi lauzimu. Ngati ni wolapadi ndipo angathe kum’thandiza, cidzudzulo cimene angam’patse, kaya camseli kapena capoyela, kutanthauza pamaso pa mboni zimene zinapelekapo umboni pamene mlanduwo unali kuzengedwa, cidzathandiza kuwongolela wolakwayo, komanso kupeleka cenjezo kwa openyelelawo. (2 Sam. 12:13; 1 Tim. 5:20) Pa milandu yonse ya cidzudzulo, ziletso ziyenela kupelekedwa. Zimathandiza kuti wolakwayo ‘awongole njila zake.’ (Aheb. 12:13) M’kupita kwa nthawi, ziletsozo zimacotsedwa pang’ono-pang’ono akamaonetsa kuti akucila kuuzimu.

KULENGEZA CIDZUDZULO

24 Komiti yaciweluzo ikaona kuti munthuyo ni wolapa, koma n’zacionekele kuti nkhaniyo idzadziŵika mumpingo komanso kudelalo, kapenanso pofuna kucenjeza mpingo kuti uzisamala naye wolakwayo, cilengezo cacidule ciyenela kupelekedwa pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Ciziŵelengedwa mwacidule motele: “M’bale (mlongo) [Dzina lake] anadzudzulidwa.”

NGATI CIGAMULO N’CAKUTI ACOTSEDWE

25 Nthawi zina wolakwa amakhala wouma khosi panjila ya kulakwa kwake moti salabadila zoyesa-yesa zonse zofuna kum’thandiza. Panthawi imene komiti yaciweluzo ikuzenga mlandu wake, iye saonetsa mokhutilitsa “nchito zosonyeza kulapa.” (Mac. 26:20) Zikakhala conco, palibe kucitila mwina koma kum’cotsa munthuyo mumpingo, kuti asakhalenso na mwayi womayanjana na anthu oyela a Yehova. Kucotsa munthu wotelo kumakhala kucotsa cisonkhezelo coipa mumpingo, pofuna kuteteza ciyelo ca mpingo komanso dzina lake labwino. (Deut. 21:20, 21; 22:23, 24) Pamene mtumwi Paulo anamva za khalidwe lonyazitsa la wina wake mumpingo wa ku Korinto, analangiza akulu kuti ‘apeleke munthu ameneyo kwa Satana . . . , kuti mzimu [wa mpingo] upulumutsidwe.’ (1 Akor. 5:5, 11-13) Paulo anachulanso za ena omwe anacotsedwa mumpingo m’nthawi ya Akhristu oyambilila cifukwa copandukila coonadi.—1 Tim. 1:20.

26 Komiti yaciweluzo ikagamula kuti munthu wosalapayo ayenela kucotsedwa, imuuze za cigamuloco, na kumuunikila momveka bwino cifukwa kapena zifukwa za m’Malemba zomucotsela. Akamudziŵitsa za cigamuloco, amuuzenso kuti ngati akuona kuti cigamulo ca komiti calakwika kwambili penapake, ndipo akufuna kucita apilu, acite zimenezo mwa kulemba kalata, na kuchula momveka bwino zifukwa zake zocitila apilu. Apatsidwe masiku 7 ocita apilu kucokela patsiku limene wauzidwa za cigamulo ca komiti. Kalata ya apilu ikabwela, akuluwo adzadziŵitsa woyang’anila dela amene adzasankha akulu oyenelela kutumikila pakomiti ya apilu kuti akamvenso mlanduwo. Akuluwo adzayesetsa kusamalila nkhaniyo mkati mwa mlungu umodzi kucokela pamene kalatayo inalandilidwa. Ngati munthu wacita apilu, musalengeze kuti wacotsedwa mumpingo. Koma panthawi imeneyi, munthuyo sadzaloledwa kuyankha pamisonkhano, kupelekapo pemphelo, kapena kutumikila pambali ina iliyonse.

27 Colinga ca apilu ni kukomela mtima munthu wonenezedwayo pom’patsa mwayi wakuti madandaulo ake akamvedwe. Mwa ici, ngati wolakwayo mwadala sakubwela kudzaonekela ku komiti ya apilu, ndipo mwayesetsa kulumikizana naye koma osaphula kathu, lengezani za kucotsedwa kwake.

28 Ngati wolakwayo safuna kucita apilu, komiti yaciweluzo imufotokozele kufunika kolapa, komanso zimene ayenela kucita kuti m’kupita kwa nthawi akabwezeletsedwe. Kucita zimenezi n’kumuthandiza komanso kum’komela mtima. Pocita izi, maganizo athu azikhala a ciyembekezo cakuti adzawongolela njila zake na kubwelela m’gulu la Yehova.—2 Akor. 2:6, 7.

CILENGEZO CA KUCOTSEDWA

29 Ngati kwakhala kofunikila kucotsa mumpingo munthu wosalapa, palekani cilengezo cacidule. Ciziŵelengedwa mwacidule motele: “[Dzina lake] salinso Mboni ya Yehova.” Izi zimathandiza okhulupilika mumpingo kuti aleke kuyanjana naye munthuyo.—1 Akor. 5:11.

KUDZILEKANITSA

30 Liwu lakuti “kudzilekanitsa” limatanthauza mcitidwe wa munthu amene ni Mboni yobatizika, koma mosankha yekha wadzilekanitsa na mpingo wacikhristu, mwa kucita kukamba yekha kuti safunanso kudziŵika monga Mboni ya Yehova. Kapenanso angadzilekanitse na mpingo wacikhristu mwa zocita zake, monga kugwilizana na gulu kapena bungwe limene zolinga zake n’zosemphana na ziphunzitso za m’Baibo, amene mwakutelo amadziika pa ciweluzo ca Yehova Mulungu.—Yes. 2:4; Chiv. 19:17-21.

31 M’nthawi ya mtumwi Yohane, analiponso amene anakana cikhulupililo cawo. Iye anati za iwo: “Amenewo anacoka pakati pathu, koma sanali m’gulu lathu, cifukwa akanakhala a m’gulu lathu, akanakhalabe ndi ife”.—1 Yoh. 2:19.

32 Munthu akadzilekanitsa, pamaso pa Yehova amasiyana kwambili na Mkhristu wozilala, amene anangoleka kutengako mbali mu ulaliki. Munthu angazilale cabe cifukwa analeka kuŵelenga Mawu a mulungu nthawi zonse. Kapenanso mwina pokumana na mavuto ena ake kapena cizunzo, anazilala pa kutumikila Yehova. Zikatelo, akulu komanso ena onse mumpingo ayenela kupitiliza kuthandizila Mkhristu wozilala ameneyo.—Aroma 15:1; 1 Ates. 5:14; Aheb. 12:12.

33 Koma ngati munthu wasankha kudzilekanitsa na mpingo, mpingo udziŵitsidwe mwa cilengezo cacidule cakuti: “[Dzina la munthuyo] salinso Mboni ya Yehova.” Munthu woteloyo tiyenela kucita naye mofanana na munthu wocotsedwa.

KUBWEZELETSA MUNTHU MUMPINGO

34 Munthu wocotsedwa mumpingo kapena wodzilekanitsa yekha akhoza kubwezeletsedwa ngati waonetsa umboni wotsimikizika wakuti analapadi, ndipo kwa nthawi yaitali bwino waonetsa kuti anasiilatu njila yake yaucimo. Akatelo, amaonetsa kuti akufunadi kukhalanso paubale na Yehova. Ngakhale n’telo, akulu amacita naye mosamala. Amalola kuti papite nthawi yokwanila—miyezi yambili, caka, ngakhale kuposapo, malinga na zocitikazo—kuti munthuyo aonetse kuti kulapa kwake n’kweni-kwenidi. Akulu akalandila kalata yopempha kubwezeletsedwa, komiti yobwezeletsa ikambilane naye munthuyo. Komitiyo ipende mosamala ngati palidi umboni woonetsa “nchito za kulapa,” na kugamula kuti abwezeletsedwe panthawiyo kapena ayi.—Mac. 26:20.

35 Ngati munthu wopempha kubwezeletsedwa anacotsedwela kumpingo wina, komiti yobwezeletsa ya mpingo kumene ali panthawiyo akumane naye kuti amvele pempho lake. Komitiyo ikakhutila kuti munthuyo ayeneladi kubwezeletsedwa, itumize civomelezo cawo ku bungwe la akulu kumpingo umene unasamalila nkhaniyo. Makomiti aŵiliwo adzaseŵenzela pamodzi kuti aunikilane mfundo zonse zofunikila kuti nkhaniyo isamalidwe mwacilungamo. Koma cigamulo cobwezeletsa munthu ciyenela kupangidwa na komiti yobwezeletsa ya mpingo umene unasamalila nkhaniyo poyamba.

CILENGEZO CA KUBWEZELETSA

36 Komiti yobwezeletsa ikakhutila kuti munthu wocotsedwa kapena wodzilekanitsa ni wolapadi, ndipo m’pake kuti abwezeletsedwe, cilengezo cipelekedwe kumpingo umene unasamalila nkhaniyo poyamba. Ngati munthuyo anasamukila ku mpingo wina, kumenekonso cilengezo cipelekedwe. Ciyenela kukhala cacidule motele: “[Dzina la munthuyo] wabwezeletsedwa kukhalanso Mboni ya Yehova.”

NKHANI ZOKHUDZA ANA OBATIZIKA

37 Ngati mwana wamng’ono wobatizika wacita colakwa cacikulu, nkhaniyo ikatulidwebe kwa akulu. Akulu posamalila chimo lalikulu lokhudza mwana wamng’ono, ni bwino kuti makolo ake obatizika azikhalapo. N’cinthu canzelu kuti makolowo athandizane bwino na komiti yaciweluzo, m’malo moyesa kuikila kumbuyo mwana wolakwayo kuti asalandile cilango. Monga zimakhalila posamalila nkhani ya munthu wamkulu, komiti yaciweluzo iyenela kuyesetsa kupeleka cidzudzulo kwa mwana wolakwayo n’colinga cakuti am’bweze. Koma ngati wacicepeleyo saonetsa kulapa, ayenela kucotsedwa mumpingo.

WOFALITSA WOSABATIZIKA AKAGWELA M’CHIMO

38 Kodi ciyenela kucitika n’ciani pamene wofalitsa wosabatizika wacita colakwa cacikulu? Popeza kuti iye si Mboni yobatizika, sangacotsedwe mumpingo. Kweni-kweni amakhala alibe cidziŵitso cokwanila ca miyezo ya m’Baibo. Conco, uphungu wokoma mtima ungam’thandize ‘kuwongola njila za mapazi ake.’—Aheb. 12:13.

39 Koma ngati wofalitsa wosabatizikayo ni wosalapa, ngakhale akulu aŵili atakumana naye na kuyesa kum’thandiza, m’pofunikila kuudziŵitsa mpingo. Pelekani cilengezo cacidule cakuti: “[Dzina la munthuyo] salinso wofalitsa wosabatizika.” Zikatelo, mpingo uziona munthuyo ngati wakunja. Ngakhale kuti iye wasiyanako na munthu wocotsedwa, Akhristu ayenela kusamalabe naye pa nkhani ya mayanjano. (1 Akor. 15:33) Munthu ameneyo sayenela kupelekanso malipoti a utumiki.

40 M’kupita kwa nthawi, munthu amene anacotsedwa pamalo ake monga wofalitsa wosabatizika, angapemphe kuti akhalanso wofalitsa. Akatelo, akulu aŵili akumane naye kuti aone mmene wawongolela umoyo wake wauzimu. Ngati apeza kuti ni woyenelela, cilengezo cacidule cikapelekedwe kumpingo, cakuti: “[Dzina la munthuyo] wakhalanso wofalitsa wosabatizika.”

YEHOVA AMADALITSA ANTHU OMULAMBILA MWAMTENDELE KOMANSO MWACIYELO

41 Onse amene ali mumpingo wa Mulungu masiku ano, amasangalala kukhala m’malo auzimu amene Yehova wapeleka kwa anthu ake. M’malo amenewo, tili na cakudya cauzimu ca mwana alilenji, komanso madzi otsitsimula ambili-mbili a coonadi. Tilinso na citetezo ca Yehova kupitila m’makonzedwe a umulungu pansi pa Khristu monga mutu wa mpingo. (Sal. 23; Yes. 32:1, 2)

42 Ngati tisungabe mtendele na ciyelo mumpingo, kuwala kwathu kwa coonadi ca Ufumu kuzipita kuwalila-walilabe. (Mat. 5:16; Yak. 3:18) Mwa dalitso la Mulungu, tidzapitiliza kuona anthu oculukila-culukilabe akukhamukila kwa Yehova kudzatumikila nafe pamodzi pokwanilitsa cifunilo cake.

Ngati tisungabe mtendele na ciyelo mumpingo, kuwala kwathu kwa coonadi ca Ufumu kuzipita kuwalila-walilabe

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani