LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 17 masa. 169-178
  • Khalanibe Pafupi na Gulu la Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khalanibe Pafupi na Gulu la Yehova
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIANI MAYESO AKUCULUKILA-CULUKILABE?
  • KULITSANI CIPILILO
  • KUPILILA MAYESO OSIYANA-SIYANA
  • KUKHALABE OKHULUPILIKA ZIVUTE ZITANI
  • “Mulole Kuti Kupilila Kumalize Kugwila Nchito Yake”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Tengelani Citsanzo ca Yehova pa Kupilila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mmene Tingakhalilebe Acimwemwe Popilila Mayeso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 17 masa. 169-178

MUTU 17

Khalanibe Pafupi na Gulu la Yehova

MTUMWI Yakobo analemba kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yak. 4:8) Inde, ngakhale kuti ndife anthu opanda ungwilo, Yehova sali kutali koti n’kulephela kumva mapemphelo athu. (Mac. 17:27) Nanga tingamuyandikile bwanji Mulungu? Tingatelo mwa kupalana naye ubwenzi wolimba, kumene kuphatikizapo kumakamba naye m’pemphelo mocokela pansi pa mtima. (Sal. 39:12) Tingalimbitsenso ubwenzi wathu na Mulungu mwa kuphunzila Mawu ake Baibo nthawi zonse. Mwa kutelo, timafika pom’dziŵa bwino Yehova Mulungu, zolinga zake, na cifunilo cake kwa ife. (2 Tim. 3:16, 17) Pocita zimenezi, timaphunzila kumukonda, na kukulitsa mantha oopa kucita zinthu zomukhumudwitsa.—Sal. 25:14.

2 Komabe, kuyandikana naye Yehova kumangotheka kupyolela mwa Yesu Mwana wake. (Yoh. 17:3; Aroma 5:10) Palibe munthu aliyense angatiunikile bwino za maganizo a Yehova kuposa mmene Yesu amacitila. Iye anafika pomudziŵa bwino kwambili Atate wake. N’cifukwa cake ananena kuti: “Palibe amene akum’dziŵa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso Atatewo palibe amene akuwadziŵa bwino koma Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululila za Atatewo.” (Luka 10:22) Conco, tikamaphunzila m’mabuku a Uthenga Wabwino za kaganizidwe ka Yesu na mmene anali kuonela zinthu, kweni-kweni timakhala tikuphunzila za kaganizidwe ka Yehova na mmene amaonela zinthu. Cidziŵitso cimeneco n’cimene cimatiyandikizitsa kwa Mulungu wathu.

3 Pansi pa umutu wa Mwana wake, timakulitsa cikondi cacikulu pa Yehova poyandikana kwambili na gulu lake looneka na maso, limene limatithandiza kucita cifunilo ca Mulungu. Monga zinanenedwelatu pa Mateyu 24:45-47, Mbuye ameneyo, Yesu Khristu, anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azigaŵila “cakudya pa nthawi yoyenela” ku banja la cikhulupililo. Lelo lino, kapolo wokhulupilika ameneyo amatigaŵiladi cakudya cauzimu ca mwana alilenji. Kudzela m’makonzedwe amenewa, Yehova amatilangiza kuti tiziŵelenga Mawu ake tsiku na tsiku, tizipezeka kumisonkhano nthawi zonse, na kutengako gawo panchito yolalikila “uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mat. 24:14; 28:19, 20; Yos. 1:8; Sal. 1:1-3) Ngakhale kuti kapolo wokhulupilika ni anthu opanda ungwilo, tikhale na cidalilo conse cakuti Yehova ndiye amawatsogolela. Tikatelo, tidzamuyandikila kwambili Mulungu wathu Yehova, ndipo tidzakhala olimba komanso otetezeka ngakhale pamayeso.

N’CIFUKWA CIANI MAYESO AKUCULUKILA-CULUKILABE?

4 Mwina inu mwakhala m’coonadi kwa zaka zambili. Ngati n’conco, nkhani yopilila mayeso mumaidziŵa bwino. Koma ngakhale kuti Yehova munam’dziŵa posacedwa ndipo mumagwilizana na anthu ake, mumadziŵa zakuti Satana Mdyelekezi amatsutsa aliyense amene amagonjela ulamulilo wa Yehova. (2 Tim. 3:12) Cotelo, kaya mwapilila zambili kapena zocepa, musakhale na mantha kapena kulefulidwa. Yehova akulonjeza kuti adzakucilikizani, adzakupulumutsani, ndipo pothela pake adzakupatsani moyo wosatha.—Aheb. 13:5, 6; Chiv. 2:10.

5 M’masiku otsalawa a dongosolo la Satana, tonsefe tingakumanebe na mayeso ena. Ciukhazikitsileni Ufumu wa Mulungu mu 1914, Satana sanaloledwe kukaloŵa kumwamba kwa Yehova. Anaponyedwa ku dziko lapansi, kumene iye na angelo ake oipa alili. Kuculuka kwa matsoka padziko lapansi, ngakhalenso kuzunzidwa kwa atumiki a Yehova, ni kaamba ka mkwiyo wa Satana. Ndipo umenewu ni umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiliza a ulamulilo wake woipa pa anthu.—Chiv. 12:1-12.

6 Satana ali na mkwiyo waukulu cifukwa ca kutsitsidwa pamalo ake, ndipo amadziŵa kuti nthawi yam’tsalila ni yocepa. Poona conco, iye na ziŵanda zake amayesa kucita zonse zotheka kuti asokoneze nchito yolalikila, na mgwilizano wa atumiki a Yehova. Pa cifukwa cimeneci, ife tili pankhondo yauzimu yofotokozedwa kuti “sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma, maulamulilo, olamulila dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” Conco, “musasunthike polimbana ndi zocita zacinyengo za Mdyelekezi.” (Aef. 6:10-17) Kuti izi zitheke, pamafunika cipililo kumbali yathu.

KULITSANI CIPILILO

7 Cipililo cimatanthauza “kukwanitsa kulimbika pa zovuta.” M’lingalilo lauzimu, cipililo ni khalidwe la kucilimika pa kucita cabwino poyang’anizana na mavuto, kutsutsidwa, kuzunzidwa, kapena cina ciliconse cofuna kutitayitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu. Tiyenela kukulitsa cipililo cacikhristu cimeneci. Koma zimatenga nthawi. Khalidwe la kupilila limakula pamene tikupita patsogolo kuuzimu. Pamene tipilila mayeso ang’ono-ang’ono kumayambililo kwa umoyo wathu wacikhristu, timapita tilimbila-limbila. Ndipo m’kupita kwa nthawi, timatha kupilila mayeso akulu-akulu. (Luka 16:10) Mayeso akulu-akulu asanatipeze, tiyenela kukonzeka pasadakhale kuti tikapilile zilizonse zimene zingayese cikhulupililo cathu. Poonetsa kufunika kokulitsa cipililo pamodzi na makhalidwe ena aumulungu, mtumwi Petulo analemba kuti: “Yesetsani mwakhama kuwonjezela pa cikhulupililo canu makhalidwe abwino, pa makhalidwe anu abwino muwonjezelepo kudziŵa zinthu, pa kudziŵa zinthu kudziletsa, pa kudziletsa kupilila, pa kupilila kudzipeleka kwa Mulungu, pa kudzipeleka kwa Mulungu kukonda abale, pa kukonda abale, cikondi.”—2 Pet. 1:5-7; 1 Tim. 6:11.

Cipililo cathu cimakula tsiku na tsiku pamene tigonjetsa mayeso

8 Yakobo nayenso anakambapo za kufunika kokulitsa cipililo. Iye anati m’kalata yake: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayeselo osiyanasiyana, monga mukudziŵila kuti cikhulupililo canu cikayesedwa, cimabala kupilila. Koma mulole kuti kupilila kumalize kugwila nchito yake, kuti mukhale okwanila ndi opanda cilema m’mbali zonse, osapeleŵela kalikonse.” (Yak. 1:2-4) Yakobo anati Akhristu ayenela kulandila mayeso na manja aŵili na kusangalala nawo, cifukwa amatithandiza kukulitsa cipililo. Kodi munawaonapo motelo mayeso? Kenako Yakobo anaonetsa kuti cipililo cimagwila nchito youmba bwino umunthu wathu wacikhristu, kuti tikhale olandilika kwa Mulungu. Inde, cipililo cathu cimakula tsiku na tsiku pokumana na mayeso na kuwagonjetsa. Naconso cipililo cimabala makhalidwe enanso abwino amene timafunikila.

9 Yehova amakondwela nako kupilila kwathu. Ndipo tikakhalabe opilila, adzatipatsa mphoto ya moyo wosatha. Yakobo anawonjezelanso kuti: “Wodala ndi munthu wopilila mayeselo, cifukwa akadzavomelezedwa, adzalandila mphoto ya moyo, umene Yehova analonjeza onse omukonda.” (Yak. 1:12) Zoonadi, timapilila kuti tikapeze moyo wosatha. Ndipo popanda kupilila, palibe angakhalemo m’coonadi. Conco tisagonje ku zopanikiza kapena zokodola za dzikoli, cifukwa zingatibwezenso kudziko. Popanda kupilila, mzimu wa Yehova sungapitilize pa ife, kutanthauza kuti sitingabalenso zipatso za mzimu mu umoyo wathu.

10 Kuti tikhalebe okhoza kupilila panthawi zovuta, tiyenela kukhala na maganizo oyenelela pa nkhani ya kuzunzidwa. Kumbukilani zimene Yakobo analemba. Iye anati: “Sangalalani” pokumana na mayeselo. N’zoona kuti si cinthu cokondweletsa kumva zoŵaŵa kapena kusautsika m’maganizo. Koma tikumbukile kuti moyo wam’tsogolo uli paciswe. Zimene zinacitikila atumwi zingatithandize kuona mmene tingakhalile osangalala pamene tikuvutitsidwa. Buku la Macitidwe limanena kuti: “Ndipo anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno anangowakwapula ndi kuwalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu, kenako anawamasula. Conco atumwiwo anacoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu.” (Mac. 5:40, 41) Atumwiwo anali ozindikila kuti kuzunzidwa kwawo kunali umboni wa kulabadila lamulo la Yesu, na ciyanjo ca Yehova. Patapita zaka, pamene Petulo anali kulemba kalata yake yoyamba youzilidwa, anakambapo za phindu la kuzunzidwa pa cifukwa ca cilungamo.—1 Pet. 4:12-16.

11 Cocitika cina cinali cokhudza Paulo na Sila. Ali pautumiki wawo waumishonale ku Filipi, anamangidwa na kupatsidwa mlandu wobweletsa cisokonezo mumzindawo, komanso kulalikila miyambo yacilendo. Mwa ici, anawamenya kwambili na kuwaponya m’ndende. Baibo imatiuza kuti ali m’ndende muja na zilonda zawo, “capakati pa usiku, Paulo ndi Sila anali kupemphela ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo, ndipo akaidi ena anali kuwamva.” (Mac. 16:16-25) Paulo na mnzakeyo anaona kuti kuvutikila kawo Khristu kunali umboni wa cikhulupilolo cawo mwa Mulungu na anthu, ndiponso unali ulaliki kwa anthu a maganizo abwino kuti amvetsele uthenga wabwino. Komanso miyoyo ya anthu ena inali paciswe. Usiku umenewo, woyang’anila ndende pamodzi na banja lake analabadila uthenga wabwino na kukhala ophunzila. (Mac. 16:26-34) Paulo na Sila anadalila Yehova na mphamvu zake. Inde, anadziŵa kuti zivute zitani, Mulungu anali wokonzeka kuwacilikiza m’masautso awo.

12 Masiku anonso, Yehova watipatsa zonse zofunikila kuticilikiza pokumana na mayeso. Ndipo amafuna kuti tizipilila. Watipatsa Mawu ake ouzilidwa kuti tikhale na cidziŵitso colondola pa colinga cake. Zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo cathu. Timakhalanso na mwayi wosonkhana pamodzi na okhulupilila anzathu, ndiponso kucita utumiki wopatulika. Tilinso na mwayi woyandikana naye Yehova pokambilana naye m’pemphelo. Iye amamvetsela mawu athu omutamanda, komanso mapempho athu akuti atithandize kukhala na makhalidwe abwino pamaso pake. (Afil. 4:13) Komanso, ciyembekezo cimene tili naco cimatipatsa mphamvu kwambili.—Mat. 24:13; Aheb. 6:18; Chiv. 21:1-4.

KUPILILA MAYESO OSIYANA-SIYANA

13 Mayeso amene timakumana nawo masiku ano sasiyana na amene ophunzila oyambilila a Yesu Khristu anali kukumana nawo. M’nthawi zamakono, anthu onamizidwa akhala akuvutitsa a Mboni za Yehova mwa kuwanyoza na kuwazunza. Monga zinalili m’nthawi ya atumwi, kambili amene amakhala kumbuyo kwa nkhanza zimenezo ni atsogoleli acipembedzo. Kumakhala kupsa mtima cifukwa cakuti Mawu a Mulungu amavumbula zocita zawo. (Mac. 17:5-9, 13) Nthawi zina, anthu a Yehova amafunsila maufulu awo ku maboma andale, ndipo amapatsidwa maufulu amenewo. (Mac. 22:25; 25:11) Komabe, nthawi zina olamulila aika ziletso pa nchito yathu kuti utumiki wathu ulekeke. (Sal. 2:1-3) Zimenezi zikacitika, molimba mtima timatengela citsanzo ca atumwi okhulupilika, amene anakamba kuti: “Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Mac. 5:29.

14 Pamene mzimu wa ‘konda dziko lako’ ukukulila-kulila zungulile dziko lapansi, pakucitika zinthu zambili zoyesa kukakamiza alaliki a uthenga wabwino kuti aleke utumiki umene Mulungu anawapatsa. Pa cifukwa ici, atumiki a Mulungu onse safuna kuiŵala cenjezo la pa Chiv. 14:9-12, lonena za kulambila “cilombo ndi cifanizilo cake.” Timaona kufunika kwa mawu a Yohane akuti: “Kwa oyelawo, amene akusunga malamulo a Mulungu ndi kutsatila cikhulupililo ca Yesu, apa ndiye pofunika kupilila.”

15 Cifukwa ca nkhondo, kusintha kwa maboma, mazunzo, kapena ziletso za boma, nthawi zina kungakhale kosatheka kulambila poyela. Zingakhale zosatheka ngakhale kusonkhana monga mpingo. Njila zolumikizilana na ofesi yanthambi zingaduke. Maulendo a woyang’anila dela angalekeke. Ngakhalenso zofalitsa zingaleke kubwela. Kodi pakagwa zotelezi, muyenela kucita ciani?

16 Citani ciliconse cothekela malinga na mikhalidweyo. Limbikilani kumacita phunzilo laumwini. Mwinanso zingakhale zotheka kumakumana m’tumagulu m’nyumba za abale. Pamisonkhano mungamaseŵenzetse zofalitsa zakale na Baibo. Musade nkhawa kwambili kapena kucita mantha. Nthawi zambili, Bungwe Lolamulila limatha kupeza njila mwamsanga yolumikizana na abale apaudindo.

17 Ngakhale mutalekanitsidwa kwa abale anu onse acikhristu, kumbukilani kuti palibe angakulekanitseni kwa Yehova na Mwana wake Yesu Khristu. Ciyembekezo canu cingakhalebe colimba. Yehova adzamvabe mapemphelo anu, na kukulimbitsani na mzimu wake. Yang’anani kwa iye kuti akutsogoleleni njila. Musaiŵale kuti ndimwe mtumiki wa Yehova komanso wophunzila wa Yesu Khristu. Conco, tengelani mwayi mipata yocitila umboni. Yehova adzadalitsa zoyesa-yesa zanu. Ndipo mwakutelo, ena angagwilizane namwe pa kulambila koona.—Mac. 4:13-31; 5:27-42; Afil. 1:27-30; 4:6, 7; 2 Tim. 4:16-18.

18 Koma ngati zimene zinacitikila atumwi komanso anthu ena zingakugweleni, zoyang’anizana na imfa yeni-yeni, ikani cidalilo conse mwa “Mulungu amene amaukitsa akufa.” (2 Akor. 1:8-10) Cikhulupililo canu cakuti Mulungu adzaukitsa akufa cingakuthandizeni kupilila masautso alionse, olo akhale oopsa cotani. (Luka 21:19) Khristu anatisiyila citsanzo. Iye anadziŵa kuti kukhulupilika kwake pamayeso kudzalimbikitsa ena kuti azipilila. Inde, inunso mungalimbikitsenso abale na alongo m’njila yofananayo.—Yoh. 16:33; Aheb. 12:2, 3; 1 Pet. 2:21.

19 Kupatulapo kuzunzidwa na kutsutsidwa, palinso zovuta zina zofunikila kupilila. Mwacitsanzo, ena alefuka cifukwa ca kuculuka kwa anthu osafuna kuwalalikila m’gawo lawo. Ena n’cifukwa ca matenda, kupsinjika maganizo, kapena zifooko zina zaumunthu. Mtumwi Paulo nayenso anapilila mayeso amene anajejemetsa utumiki wake nthawi zina. (2 Akor. 12:7) Komanso Epafurodito, Mkhristu wa ku Filipi wa m’nthawi ya atumwi, ‘anavutika maganizo cifukwa [anzake] anamva kuti iye anali kudwala.’ (Afil. 2:25-27) Ndiponso, zifooko zathu kapena za abale athu zingakhale zovuta kuzipilila. Mwinanso pangakhale kusamvana cifukwa cosiyana maumunthu na Akhristu ena, ngakhale m’banja mwathu mweni-mwenimo. Koma ngati tilabadila uphungu wa m’Mawu a Yehova, zopinga zimenezi tikhoza kuzipilila na kuzigonjetsa.—Ezek. 2:3-5; 1 Akor. 9:27; 13:8; Akol. 3:12-14; 1 Pet. 4:8.

KUKHALABE OKHULUPILIKA ZIVUTE ZITANI

20 Tiyenela kukhalabe nga nga nga kwa amene Yehova anamuika kukhala Mutu wa mpingo, Yesu Khristu. (Akol. 2:18, 19) Tiyeni tigwile nchito mogonjela “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” komanso aja oikidwa kukhala oyang’anila. (Aheb. 13:7, 17) Pocilikiza makonzedwe a umulungu na kulabadila abale otsogolela, tidzaonetsa kuti ndifedi gulu lokhazikitsidwa kucita cifunilo ca Yehova. Tiyenelanso kutengela mwayi wa pemphelo. Kumbukilani, kaya zipupa za ndende, kapena kutitsekela m’cipinda catokha, palibe cingapinge kukambilana kwathu na Atate wathu wacikondi wakumwamba, kapena kupasula umodzi umene tili nawo na olambila anzathu.

21 Pokhala okonzekela kupilila zilizonse, tiyeni ticite zonse zotheka kuti tigwile nchito yathu yolalikila, inde nchito imene Yesu Khristu woukitsidwayo analamula otsatila ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.” (Mat. 28:19, 20) Mofanana na Yesu, tiyeni tipilile. Tiikebe patsogolo pathu ciyembekezo ca Ufumu wa Mulungu na moyo wamuyaya. (Aheb. 12:2) Monga ophunzila a Yesu obatizika, tili na mwayi wotengapo gawo pa kukwanilitsa ulosi wonena za “nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:3, 14) Ngati panthawi ino tidzipeleka na mtima wonse pa nchito imeneyi, tidzadalitsika pokalandila moyo wamuyaya m’dziko latsopano lolungama limene Yehova analonjeza!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani