NKHANI 15
Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
1. N’ndani yekha angatiuze njila yoyenela yolambilila Mulungu?
ZIPEMBEDZO zambili zimakamba kuti zimaphunzitsa coonadi ponena za Mulungu. Koma zimenezo n’zosatheka, cifukwa zipembedzo zonse zimaphunzitsa zinthu zosiyana-siyana pa nkhani yakuti Mulungu n’ndani, ndi mmene tiyenela kum’lambilila. Conco, tingadziŵe bwanji kulambila kumene Mulungu amavomeleza? Yehova yekha ndiye angatiuze mmene tiyenela kum’lambilila.
2. Mungadziŵe bwanji kulambila kumene Mulungu amavomeleza?
2 Yehova anatipatsa Baibulo kuti tidziŵe mmene tiyenela kum’lambilila. Conco phunzilani Baibulo, ndipo Yehova adzakuthandizani kuti mupindule ndi malangizo ake cifukwa amakukondani kwambili.—Yesaya 48:17.
3. N’ciani cimene Mulungu amafuna kuti tizicita?
3 Anthu ena amakamba kuti Mulungu amavomeleza zipembedzo zonse. Koma Yesu sanaphunzitse zimenezo. Iye anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzaloŵa Ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akucita cifunilo ca Atate wanga.” Conco, tiyenela kucidziŵa cifunilo ca Mulungu ndi kucicita. Iyi ni nkhani ikulu kwambili. Ndiye cifukwa cake Yesu anayelekezela anthu osamvela Mulungu ndi apandu, “anthu osamvela malamulo.”—Mateyu 7:21-23.
4. Kodi Yesu anati ciani pa nkhani yocita cifunilo ca Mulungu?
4 Yesu anaticenjezelatu kuti pocita cifunilo ca Mulungu tidzakumana ndi mavuto. Iye anati: “Loŵani pacipata copapatiza. Pakuti mseu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuciwonongeko, ndipo anthu ambili akuyenda mmenemo. Koma cipata coloŵela ku moyo n’copapatiza komanso mseu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi oŵelengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Mseu wopanikiza, kapena kuti njila yabwino yolambilila Mulungu imatsogolela ku moyo wosatha. Mseu wotakasuka, kapena kuti njila yolakwika yolambilila Mulungu imatsogolela ku imfa. Koma Yehova safuna kuti munthu aliyense akafe. Amapeleka mwayi kwa munthu aliyense kuti aphunzile za iye.—2 Petulo 3:9.
KULAMBILA KUMENE MULUNGU AMAVOMELEZA
5. Tingawadziŵe bwanji anthu amene amalambila Mulungu m’njila yoyenela?
5 Yesu anakamba kuti tikhoza kuwadziŵa anthu amene amalambila Mulungu m’njila yoyenela. Tingawadziŵe mwa kuona zimene amakhulupilila ndi zimene amacita. Iye anati: “Mudzawazindikila ndi zipatso zawo.” Ndiponso anati: “Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino.” (Mateyu 7:16, 17) Ici sicitanthauza kuti amene amalambila Mulungu ni angwilo iyai. Koma atumiki a Mulungu amayesetsa kucita zoyenela nthawi zonse. Lomba tiyeni tikambilane mmene tingadziŵile anthu amene amalambila Mulungu m’njila yoyenela.
6, 7. N’cifukwa ciani cipembedzo coona ciyenela kudalila Baibulo? Nanga citsanzo ca Yesu cikutiphunzitsa ciani?
6 Kulambila kwathu kuyenela kuzikidwa pa Baibulo. Baibulo imati: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’cilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenelela bwino ndi wokonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Mtumwi Paulo analembela Akhiristu kuti: “Pakuti pamene munalandila mau a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandile monga mau a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mau a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Inde, kulambila koona kuyenela kuzikidwa pa Mau a Mulungu, Baibulo, osati pa nzelu za anthu, miyambo, kapena cina ciliconse.
7 Ciliconse cimene Yesu anaphunzitsa cinacokela m’Mau a Mulungu. (Ŵelengani Yohane 17:17.) Ndipo anali kugwila mau Malemba. (Mateyu 4:4, 7, 10) Atumiki oona a Mulungu amatengela citsanzo ca Yesu, ndipo zonse zimene amaphunzitsa zimacokela m’Baibulo.
8. Kodi Yesu anatiphunzitsanji za nkhani yolambila Yehova?
8 Tiyenela kulambila Yehova yekha. Salimo 83:18 ikamba kuti: “Kuti anthu adziŵe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba.” Yesu anafuna kuti anthu adziŵe kuti Mulungu woona n’ndani, ndi kuwaphunzitsa dzina la Mulungu. (Ŵelengani Yohane 17:6.) Yesu anati: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.” (Mateyu 4:10) Conco ife pokhala atumiki a Mulungu, timatengela citsanzo ca Yesu. Timalambila Yehova yekha, timagwilitsila nchito dzina lake, ndi kuphunzitsa ena dzina la Mulungu ndi zimene adzaticitila.
9, 10. Timaonetsa bwanji cikondi kwa wina ndi mnzake?
9 Tiyenela kukonda anthu anzathu ndi mtima wonse. Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuti azikondana wina ndi mnzake. (Ŵelengani Yohane 13:35.) Zilibe kanthu kuti ticokela kuti, cikhalidwe cathu, kaya ndife olemela kapena osauka. Cikondi cathu kwa wina ndi mnzake cimatigwilizanitsa monga abale ndi alongo. (Akolose 3:14) Ndiye cifukwa cake siticitako nkhondo kapena kupha anthu. Baibulo imakamba kuti: “Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyelekezi amaonekela bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sacita zolungama sanacokele kwa Mulungu, cimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake.” Imakambanso kuti: “Tizikondana, osati ngati Kaini, amene anacokela kwa woipayo n’kupha m’bale wake.”—1 Yohane 3:10-12; 4:20, 21.
10 Timaseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, ndi cuma cathu kuti tithandize ndi kulimbikitsa anzathu. (Aheberi 10:24, 25) ‘Timacitila anthu onse zabwino.’—Agalatiya 6:10.
11. N’cifukwa ciani timavomeleza Yesu kukhala njila yofikila kwa Mulungu?
11 Tiyenela kumvela Yesu cifukwa ndiye njila yofikila kwa Mulungu. Baibulo imati: “Cipulumutso sicipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, limene lapelekedwa kwa anthu, limene tiyenela kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Mu Nkhani 5 ya buku ino, tinaphunzila kuti Yehova anatumiza Yesu pa dziko lapansi kuti adzapeleke moyo wake monga dipo loombola anthu omvela. (Mateyu 20:28) Ndiyeno Yehova anasankha Yesu ameneyo kuti akalamulile dziko lonse lapansi monga Mfumu. Ndiye cifukwa cake Baibulo imatiuza kuti tiyenela kumvela Yesu ngati tifuna kuti tikapeze moyo wosatha.—Ŵelengani Yohane 3:36.
12. N’cifukwa ciani sitiloŵa m’ndale?
12 Sitiyenela kuloŵa m’ndale. Yesu sanatengeko mbali m’ndale. Pamene anali kuzengedwa mlandu, iye anauza Pilato, wolamulila waciroma, kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Ŵelengani Yohane 18:36.) Mofanana ndi Yesu, ndife okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu, ndipo sitiloŵa m’zandale kulikonse kumene timakhala. Ngakhale n’conco, Baibulo imatilamula kuti tizimvela “olamulila akuluakulu,” kutanthauza akulu-akulu a boma. (Aroma 13:1) Timamvela malamulo a dziko limene tikhalamo. Koma ngati malamulo a boma awombana ndi malamulo a Mulungu, timatengela citsanzo ca atumwi amene anati: “Tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Machitidwe 5:29; Maliko 12:17.
13. Timalalikila ciani ponena za Ufumu wa Mulungu?
13 Timakhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu ndiye boma cabe limene lidzatsiliza mavuto pa dziko lapansi. Yesu anakamba kuti “uthenga wabwino wa Ufumu” udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi. (Ŵelengani Mateyu 24:14.) Palibe boma la anthu limene lingacite zimene Ufumu wa Mulungu udzaticitila. (Salimo 146:3) Yesu anatiphunzitsa kupemphelela Ufumu wa Mulungu pamene anati: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Baibulo imatiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzaphwanya maboma onse a anthu, ndipo udzakhalapo kwamuyaya.—Danieli 2:44.
14. N’ndani amene muganiza kuti amalambila m’njila imene Mulungu amavomeleza?
14 Pamene mwaphunzila mfundo zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Ni a cipembedzo citi amene amatenga ziphunzitso zawo m’Baibulo? N’ndani amene amakonda kulalikila za dzina la Mulungu? Ni a mpingo uti amene amadziŵika kuti amakondana ndi kugwilizana kwambili, amenenso amakhulupilila kuti Mulungu anatuma Yesu kudzatipulumutsa? Ni a cipembedzo canji amene saloŵa m’zandale? N’ndani amene amalalikila kuti Ufumu wa Mulungu cabe ndiye udzacotsa mavuto pa dziko lapansi? Kukamba zoona, ni Mboni za Yehova cabe.—Yesaya 43:10-12.
KODI INU MUDZACITA CIANI?
15. Tiyenela kucita ciani kuti Mulungu avomeleze kulambila kwathu?
15 Kungokhulupilila cabe kuti Mulungu aliko sikokwanila. Ngakhale viŵanda vimakhulupilila kuti kuli Mulungu, koma sivimumvela. (Yakobo 2:19) Ngati tifuna kuti Mulungu avomeleze kulambila kwathu, tifunikilanso kucita zimene amatiuza.
16. N’cifukwa ciani tiyenela kukana cipembedzo conama?
16 Kuti Mulungu avomeleze kulambila kwathu, tiyenela kukana cipembedzo conama. Mneneli Yesaya analemba kuti: “Tulukani mmenemo! Musakhudze cinthu ciliconse codetsedwa.” (Yesaya 52:11; 2 Akorinto 6:17) Ndiye cifukwa cake tiyenela kukana ciliconse cokhudzana ndi kulambila kwabodza
17, 18. Kodi “Babulo Wamkulu” n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kucokamo mwamsanga?
17 Kodi cipembedzo conama ni citi? Ni cipembedzo ciliconse cimene cimaphunzitsa anthu zosagwilizana ndi Mau ake opatulika. Baibulo imaphatikiza zipembedzo zonse zonama ndi kuzicha “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 17:5) Cifukwa ciani? Cifukwa ziphunzitso zonama zambili zinayambila mu mzinda wa Babulo, pambuyo pa Cigumula ca Nowa. Ziphunzitso zabodza zimenezo zinafalikila pa dziko lonse. Mwacitsanzo, anthu a ku Babulo anali kulambila milungu yokhala itatu-itatu. Ngakhale masiku ano, zipembedzo zambili zimaphunzitsa kuti pali Milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Koma Baibulo imaphunzitsa momveka bwino kuti pali Mulungu woona mmodzi yekha, Yehova, ndi kuti Yesu ni Mwana wake. (Yohane 17:3) Anthu a ku Babulo analinso kukhulupilila kuti munthu akafa, mzimu wake umapitiliza kukhala ndi moyo, ndipo ukhoza kukazunzidwa m’moto ku helo. Koma zonse izi ni mabodza cabe.—Onani Zakumapeto 14, 17, ndi 18.
18 Mulungu anakambilatu kuti posacedwa adzawononga zipembedzo zonse zonama. (Chivumbulutso 18:8) Kodi mwaona lomba cifukwa cake mufunika kucoka mwamsanga m’cipembedzo conama? Yehova Mulungu afuna kuti mucokemo mwamsanga madzi akali m’nkhongono.—Chivumbulutso 18:4.
Mukayamba kutumikila Yehova, mudzakhala m’banja la pa dziko lonse
19. Kodi Yehova adzakusamalilani bwanji mukasankha kum’tumikila?
19 Koma dziŵani kuti mukacoka m’cipembedzo conama ndi kuyamba kutumikila Yehova, anzanu ena, kapena abululu ŵanu, sangamvetse cifukwa cake mwacita zimenezo. Ndipo ena angayambe kukuvutitsani. Koma Yehova sadzakusiyani. Mudzakhala m’banja la padziko lonse la anthu amene amakondana ndi mtima wonse. Cina, mudzakhalanso ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. (Maliko 10:28-30) Mudziŵa bwanji, mwina anzanu ena, kapena abululu ŵanu amene pali pano safuna kuti mutumikile Yehova, nawonso angadzayambe kuphunzila Baibulo.
20. N’cifukwa ciani n’kofunika kulambila m’njila ya Mulungu?
20 Lomba apa, Mulungu adzacotsapo zoipa zonse, ndipo Ufumu wake udzalamulila dziko lonse lapansi. (2 Petulo 3:9, 13) Ndipo idzakhala nthawi yokondweletsa ngako! Aliyense adzalambila m’njila imene Yehova amavomeleza. Conco, ino ndiye nthawi yakuti mucitepo kanthu mwamsanga, kuti muyambe kulambila m’njila ya Mulungu.