LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ypq funso 5 masa. 15-17
  • Ningacite Bwanji Ngati Ena Amanivutitsa Kusukulu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ningacite Bwanji Ngati Ena Amanivutitsa Kusukulu?
  • Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa
  • Nkhani Zofanana
  • Muzidalila Yehova Pamene Mukuvutitsidwa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa
ypq funso 5 masa. 15-17
Mnyamata avutitsa mnzake pamaso pa anzake a kusukulu

FUNSO 5

Ningacite Bwanji Ngati Ena Amanivutitsa Kusukulu?

CIFUKWA CAKE UFUNIKA KUDZIŴA

Zimene ungacite zingapangitse zinthu kukhalako bwino kapena kuipilatu.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Ganizila cocitika ici: Thomas safuna kuyenda kusukulu lelo, mailo, kapena tsiku lililonse. Papita miyezi itatu pamene vuto iyi inayamba, pamene anzake kusukulu anafalitsa mabodza oipa onena za iye. Ndiyeno, anzake anayamba kum’patsa maina onyoza. Komanso, zinali kucitika kuti wina anamizila kum’guda mwangozi n’kugwetsela mabuku ake pansi. Nthawi zinanso wina m’gulu anali kumukankha, koma akaceuka osaona kuti n’ndani. Mailo zomuvutitsa zinafika poipa kwambili, wina anam’tumizila meseji yomuopseza kuti akam’menya kusukulu.

Ukanakhala Thomas ukanacita bwanji?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

Sikuti palibiletu zimene ungacite! Ndipo kukamba zoona, ungagonjetse munthu wokuvutitsa popanda kumenyana naye. Motani?

  • OSAYANKHA MOKALIPA. Baibo imakamba kuti: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzelu amakhala wodekha mpaka pamapeto.” (Miyambo 29:11) Ngati uonetsa kuti sunakalipe, ngakhale kuti mumtima cakuŵaŵa, amene akuvutitsa angamvele ulesi na kukuleka.

  • OSABWEZELA. Baibo imakamba kuti: “Musabwezele coipa pa coipa.” (Aroma 12:17) Kubwezela kudzangoipitsilatu zinthu.

  • OSADZINGENETSA DALA M’MAVUTO. Baibo imanena kuti: “Wocenjela ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Ngati zingatheke, uzipewa anthu ovutitsa anzawo, na malo kumene angapezeke.

  • YESA KUCITA ZIMENE SAYEMBEKEZELA. Baibo imakamba kuti: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Nthabwala nazo zimathandiza. Mwacitsanzo, ngati munthu wokuvutitsa akamba kuti ndiwe dugude, kapena dumbo, ukhoza kungoseka n’kunena kuti, “Owo, mwina nifunika kuyondako pang’ono!”

  • COKAPO. “Nora wa zaka 19 anakamba kuti: “Kusayankha na kucokapo kumaonetsa kuti una nzelu ndipo ndiwe wolimba kuposa munthu amene akuvutitsa.” Anatinso: “Kumaonetsa kuti ndiwe wodziletsa—khalidwe limene munthu wokuvutitsa alibe.”—2 Timoteyo 2:24.

  • KHALA NA CIDALILO. Anthu ovutitsa anzawo amadziŵa kuti uyu munthu ni wosadzidalila ndipo ni wamantha. Koma akaona kuti sucita mantha ndipo suwaikako nzelu, ambili amakusiya.

  • UZAKO MUNTHU WINA. Munthu wina amene anakhalapo tica pa sukulu anakamba kuti: “N’nali kulimbikitsa ana a sukulu kuti wina akawavutitsa azimunenela. Ndiye zofunika kucita kuti ena aziopa kuvutitsa anzawo.”

Mnyamata ayang’anizana ndi wom’vutitsa mwacidalilo

Kudzidalila kudzakupatsa mphamvu zimene wokuvutitsa alibe

KODI UDZIŴA?

Kuwonjezela pa kumenya, kuvutitsa munthu kungaphatikizeponso izi:

  • Mau ocoka pakamwa pa munthu wovutitsa anzake angakhale monga moto

    Mau onyoza. Celine wa zaka 20 anati: “Sin’dzaiŵala maina oipa amene ananipatsa, na mmene anali kuninyozela. Ananipangitsa kudzimvela monga wopanda pake, wosafunika, wacabe-cabe. N’nali kumvela kuipa cakuti olo kunimenya kunaliko bwino.”

  • Mnyamata wakhala yekha-yekha cifukwa anzake safuna kukhala naye

    Kupatuliwa. Haley wa zaka 18 anati: “Anzanga kusukulu anayamba kunipatula. Pa nthawi ya cakudya ca masana, anali kuniuza kuti malo asila pathebulo, kuti cabe nisakhale nawo. Caka conse cinathelamo nikudya nekha, uku nikulila.”

  • Mtsikana acokapo pa kompyuta cifukwa anzake amutumizila zomunyoza

    Kuipitsa mbili ya munthu pa Intaneti. Daniel wa zaka 14 anati: “Kameseji kang’ono cabe kamene ungatumize pa intaneti, kangawononge mbili yonse ya munthu—ngakhale moyo wake. Zingamveke monga uku n’kuwonjezela nkhani, koma zimacitika ndithu!”

MAFUNSO PA ZOVUTITSANA

ZOONA KAPENA BODZA

MAYANKHO

1 Kuvutitsana kwakhala kukucitika kucokela kale-kale.

1 Zoona. Mwacitsanzo, Baibo imakamba za Anefili—dzina lotanthauza kuti “Ogwetsa Anzawo.”—Genesis 6:4.

2 Kuvutitsana kulibe vuto. N’kuceza cabe.

2 Bodza. Acicepele ambili adzipha cifukwa covutitsiwa.

3 Njila yabwino yocitila na munthu wokuvutitsa ni kum’bwezela.

3 Bodza. Nthawi zambili, anthu ovutitsa anzawo amakhala amphamvu kuposa amene amawavutitsa. Conco kubwezela kungakupweteketse.

4 Ukaona wina avutitsiwa, osacitapo kanthu si nkhani yako.

4 Bodza. Kusacitapo kanthu n’kulakwa. Ngati suulula nkhaniyo, umathandizila kuti vutolo lipitilize.

5 Olo kuti ovutitsa anzawo amakamba moopseza, kweni-kweni ni amantha.

5 Zoona. Ngakhale kuti ovutitsa anzawo amadzitukumula, ambili ni amantha. Akacititsa anzawo kuwaopa amamvelako bwino.

6 Anthu ovutitsa anzawo angasinthe.

6 Zoona. Ovutitsa anzawo akhoza kusintha ngati angathandizidwe.

ZOFUNIKA KUCITA

  • Ngati wina anivutitsa, n’dzacita kapena n’dzakamba izi:

KUTI UDZIŴE ZAMBILI!

Ukhoza Kugonjetsa Munthu Wokuvutitsa Popanda Kumenyana Naye

Ukatambe vidiyo ya tukadoli yakuti Kugonjetsa Munthu Amene Akukuvutitsani Popanda Kumenyana Naye pa www.jw.org. (Yang’ana pa BIBLE TEACHINGS > TEENAGERS) Sankha Cinyanja.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani