LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 2 tsa. 10-tsa. 11 pala. 1
  • Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mwamuna Ndi Mkazi Oyamba
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • N’cifukwa Ciani Timakalamba Na Kufa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Yesu Kodi Zili ndi Tanthauzo Lotani kwa Inu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 2 tsa. 10-tsa. 11 pala. 1
Adamu na Hava m’munda wa Edeni

PHUNZILO 2

Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Oyamba

Yehova anakonza malo okongola, na kuwacha kuti munda wa Edeni. M’mundamo munali maluŵa ambili, mitengo, na vinyama. Ndiyeno Mulungu anapanga munthu woyamba, Adamu, kucokela ku dothi, na kufuzilila mpweya m’mphuno mwake. Udziŵa cimene cinacitika? Munthu uja anakhala wamoyo! Kenako, Yehova anapatsa Adamu nchito yoyang’anila munda uja, na kumuuza kuti apatse vinyama vonse maina.

Ndiyeno Yehova anapatsa Adamu lamulo lofunika kwambili. Anamuuza kuti: ‘Ungadye zipatso za m’mitengo yonse kusiyapo cabe mtengo umodzi wapadela. Ukadzadya cipatso ca mu mtengo umenewo, udzafa.’

M’kupita kwa nthawi, Yehova anati: ‘Adamu nidzamupangila womuthandiza.’ Pamenepo Mulungu anagoneka Adamu tulo tofa nato. Ndiyeno anatengako nthiti imodzi kwa Adamu na kumupangila mkazi. Dzina lake anali Hava. Adamu na Hava anakhala banja loyamba. Kodi Adamu anamvela bwanji ataona mkazi wake? Anakondwela ngako, cakuti anakamba kuti: ‘Ha, Yehova wanipangila mkazi kucokela ku nthiti yanga! Uyu lomba, ndiye wofanana na ine.’

Yehova anauza Adamu na Hava kuti abale ana na kudzaza dziko lapansi. Anali kufuna kuti iwo azikondwela pogwila nchito pamodzi yokonza dziko lonse kukhala lokongola. Inde, kuti dziko lonse likhale monga munda wa Edeni. Koma zinthu sizinayende bwino. Cifukwa ciani? Tidzaphunzila m’nkhani yotsatila.

“Amene analenga anthu pa ciyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi.”—Mateyu 19:4

Mafunso: Kodi Yehova anam’patsa nchito yanji Adamu? Kodi Mulungu anati cidzacitika n’ciani kwa Adamu na Hava akadya zipatso za mtengo umene anaŵaletsa?

Genesis 1:27-31; 2:7-9, 15-23; Salimo 115:16; Mateyu 19:4-6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani