LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 42 tsa. 102-tsa. 103 pala. 3
  • Yonatani, Munthu Wolimba Mtima Komanso Wokhulupilika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yonatani, Munthu Wolimba Mtima Komanso Wokhulupilika
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Khalani Wokhulupilika kwa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Pitilizani Kuonetsana Cikondi Ceni-ceni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kondani Anthu Amene Mulungu Amakonda
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 42 tsa. 102-tsa. 103 pala. 3
Yonatani na mtumiki wake womunyamulila zida

PHUNZILO 42

Yonatani, Munthu Wolimba Mtima Komanso Wokhulupilika

Yonatani, mwana woyamba wa Sauli, anali msilikali wolimba mtima. Davide anati Yonatani anali wa liŵilo kuposa ciwombankhanga, komanso wamphamvu kuposa mkango. Tsiku lina, Yonatani anaona asilikali 20 acifilisiti ali pa phili. Anauza womunyamulila zida kuti: ‘Tidzamenyana nawo kokha ngati Yehova watipatsa cizindikilo. Ngati Afilisiti atiuza kuti tipite, ndiye kuti tiyenela kumenyana nawo.’ Kenako Afilisiti anafuula kuti: ‘Bwelani timenyane!’ Conco, amuna aŵiliwo anakwela phili na kugonjetsa asilikaliwo.

Yonatani apeleka zinthu zake zina kwa Davide

Cifukwa Yonatani anali mwana woyamba wa Sauli, ndiye akanatenga ufumu kwa atate ake. Yonatani anali kudziŵa kuti Yehova anasankha Davide kukhala mfumu yotsatila ya Aisiraeli. Koma sanam’citile nsanje. Yonatani na Davide anakhala mabwenzi apamtima. Iwo analonjezana kuti adzatetezana. Yonatani anapatsa Davide covala cake, lupanga, uta, na lamba monga cizindikilo ca ubwenzi wawo.

Pamene Davide anali kuthaŵa Sauli, Yonatani anapita kwa Davide n’kumuuza kuti: ‘Khala wamphamvu ndipo limba mtima. Yehova anakusankha kukhala mfumu. Ngakhale atate anga adziŵa bwino zimenezi.’ Kodi ungakonde kukhala na bwenzi labwino monga Yonatani?

Kangapo konse, Yonatani anaika moyo wake paciswe kuti athandize bwenzi lake. Anadziŵa kuti Mfumu Sauli anali kufuna kupha Davide. Conco, anauza atate ake kuti: ‘Mukapha Davide mudzacimwa. Iye sanacite colakwa ciliconse.’ Koma Sauli anamukwiila kwambili Yonatani. Patapita zaka, Sauli na Yonatani onse anafa pa nkhondo.

Yonatani atamwalila, Davide anapita kukafuna-funa Mefiboseti, mwana wa Yonatani. Atam’peza anamuuza kuti: ‘Cifukwa atate ako anali bwenzi langa lapamtima, nidzakusamalila moyo wako wonse. Udzakhala m’nyumba yanga yacifumu ndi kudya pa thebulo langa.’ Davide sanamuiŵale bwenzi lake Yonatani.

“Mukondane monga mmene inenso ndakukondelani. Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake.”—Yohane 15:12, 13

Mafunso: Kodi Yonatani anaonetsa bwanji kuti anali wolimba mtima? Nanga anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika?

1 Samueli 14:1-23; 18:1-4; 19:1-6; 20:32-42; 23:16-18; 31:1-7; 2 Samueli 1:23; 9:1-13

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani