PHUNZILO 44
Kacisi wa Yehova
Solomo atakhala mfumu ya Isiraeli, Yehova anam’funsa kuti: ‘Kodi ufuna nikupatse ciani?’ Solomo anayankha kuti: ‘Ndine mwana ndipo sinidziŵa zimene nicita. Conde, nipatseni nzelu kuti nisamalile bwino anthu anu.’ Mwa ici, Yehova anamuuza kuti: ‘Cifukwa wapempha nzelu, udzakhala munthu wanzelu kuposa aliyense pa dziko lapansi. Nidzakupatsanso cuma cambili. Ndipo ngati udzamvela malamulo anga, udzakhala na moyo wautali.’
Solomo anayamba nchito yomanga kacisi. Anaseŵenzetsa golide na siliva woyenga bwino, komanso mitengo na miyala ina ya mtengo wapatali. Amuna ndi akazi ambili amaluso awo anagwila nchito yomanga kacisi. Nchito yonse inatenga zaka 7. Lomba nthawi inafika yopatulila kacisiyo kwa Yehova. Panali guwa la nsembe, na nsembe zake. Solomo anagwada patsogolo pa guwalo na kuyamba kupemphela kuti: ‘Mbuyanga Yehova, ukulu wa kacisiyu, na kukongola kwake, sizifikapo pa muyezo wanu. Koma conde, kulambila kwathu kukomele mtima wanu, ndipo mvelani mapemphelo athu.’ Kodi Yehova anamuona bwanji kacisiyo, na pemphelo la Solomo? Solomo atangotsiliza kupemphela, moto unatsika kucokela kumwamba, ndipo unanyeketsa kothelatu nsembe zinali pa guwapo. Unali umboni wakuti Yehova walandila kacisiyo. Aisiraeli poona zimenezi, anasangalala kwambili.
Cifukwa ca nzelu zake, mfumu Solomo anali wochuka kwambili mu Isiraeli na kumadela akutali. Anthu anali kupita kwa Solomo kukapempha nzelu pa mavuto awo. Ngakhale mfumukazi ya ku Seba, inapita kukamuyesa na mafunso ovuta. Mfumukazi imeneyo itamva mayankho ake, inati: ‘Sin’nali kukhulupilila zimene anthu anali kuniuza za imwe, koma lomba nakhulupilila kuti ndimwe anzelu kuposa mmene anthu ananiuzila. Mulungu wanu Yehova, wakudalitsanidi.’ Umoyo kwa Aisiraeli unali wokondweletsa kwambili, ndipo anali kukhala acimwemwe. Koma zinthu zinali pafupi kusintha.
“Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.”—Mateyu 12:42