LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 50 tsa. 120-tsa. 121 pala. 5
  • Yehova Anateteza Yehosafati

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Anateteza Yehosafati
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yehosafati Adalila Yehova
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Mudzatengelapo Phunzilo pa Zimene Zinalembedwa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Muziona Ena Mmene Yehova Amawaonela
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Tumikilani Yehova ndi Mtima Wathunthu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 50 tsa. 120-tsa. 121 pala. 5
Mfumu Yehosafati na Alevi oimba atsogolela asilikali potuluka mu Yerusalemu

PHUNZILO 50

Yehova Ateteza Yehosafati

Yehosafati mfumu ya Yuda, anawononga maguwa ansembe a Baala na mafano ake onse. Anafuna kuti anthu adziŵe malamulo a Yehova. Conco anatuma zinduna komanso Alevi ku madela onse a ufumu wa Yuda, kuti akaphunzitse anthu cilamulo ca Yehova.

Mitundu yapafupi inali kuyopa kuukila Ayuda, cifukwa inali kudziŵa kuti Yehova ali kumbali yawo. Anali kucita kubweletsa mphatso kwa Mfumu Yehosafati. Koma Amoabu, Aamoni na ena ocokela ku cigawo ca Seiri anabwela kudzacita nkhondo na Ayuda. Yehosafati anadziŵa kuti anafunikila thandizo la Yehova. Iye anasonkhanitsa amuna, akazi, ndi ana ku Yerusalemu. Ataimilila pamaso pa onse, anapemphela kuti: ‘Yehova, popanda imwe sitingapambane. Conde tiuzeni zocita.’

Yehova anayankha pemphelo limeneli. Iye anati: ‘Musacite mantha. Nidzakuthandizani. Khalani m’malo anu, imani cilili na kuona mmene nikupulumutsileni.’ Kodi Yehova anawapulumutsa bwanji?

M’mawa mwake, Yehosafati anasankha anthu oimba, na kuwauza kuti aziimba kutsogolo kwa asilikali. Iwo anayenda kucokela ku Yerusalemu mpaka kumalo omenyela nkhondo ochedwa Tekowa.

Pamene oimba anali kutamanda Yehova mosangalala komanso mokweza mawu, Yehova anamenyela nkhondo anthu ake. Anapangitsa Aamoni na Amoabu kusokonezeka, cakuti anayamba kuphana okha-okha, ndipo sipanapulumuke olo mmodzi. Koma Yehova anateteza Ayuda, asilikali, komanso ansembe. Anthu onse m’maiko ozungulila anamvela zimene Yehova anacita. Ndipo anadziŵa kuti Yehova ndiye anali kuteteza anthu ake. Kodi Yehova amapulumutsa bwanji anthu ake? M’njila zambili. Ndipo iye safunikila thandizo la munthu.

“Ulendo uno simufunikila kumenya nkhondo. Khalani m’malo anu, imani cilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.”—2 Mbiri 20:17

Mafunso: Kodi Yehosafati anali mfumu yotani? Kodi Yehova anaŵateteza bwanji Ayuda?

2 Mbiri 17:1-19; 20:1-30

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani