LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 55 tsa. 132
  • Mngelo wa Yehova Ateteza Hezekiya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mngelo wa Yehova Ateteza Hezekiya
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Abusa 7 Ndi Atsogoleli 8 Ndani Masiku Ano?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • ezekiya Anafupidwa Cifukwa ca Cikhulupililo Cake
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 55 tsa. 132
Mngelo akupha asilikali pa msasa wa Asuri

PHUNZILO 55

Mngelo wa Yehova Ateteza Hezekiya

Ufumu wa Asuri unalanda ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10. Lomba, Senakeribu mfumu ya Asuri, inali kufuna kulandanso ufumu wa Yuda wa mafuko aŵili. Anayamba kulanda mizinda ya Yuda umodzi-umodzi. Koma umene anali kuufuna kwambili ni mzinda wa Yerusalemu. Cimene Senakeribu sanadziŵe n’cakuti Yehova anali kuuteteza mzinda wa Yerusalemu.

Hezekiya anacita kupeleka ndalama zambili kwa Senakeribu kuti asalande Yerusalemu. Senakeribu analandila ndalamazo, koma anatumizabe asilikali ake amphamvu kuti akalande Yerusalemu. Asuri atafika pafupi kwambili, anthu mu mzinda anacita mantha. Ndiyeno Hezekiya anauza anthuwo kuti: ‘Musayope. N’zoona kuti Asuri ni amphamvu, koma Yehova adzatithandiza kukhala amphamvu kuposa iwo.’

Senakeribu anatumiza mthenga wake Rabisake ku Yerusalemu, kuti akaopseze anthu. Rabisake anaimilila kunja kwa mzinda na kufuula kuti: ‘Yehova sadzakuthandizani. Musalole kuti Hezekiya akupusitseni. Palibe mulungu amene adzakutetezani kwa ife.’

Hezekiya anapempha Yehova kuti amuuze zocita. Yehova anamuuza kuti: ‘Usacite mantha na zimene Rabisake wakamba. Senakeribu sadzalanda Yerusalemu.’ Kenako, Hezekiya analandila makalata ocokela kwa Senakeribu. Makalatawo anati: ‘Ugonje cabe. Yehova sadzakupulumutsa.’ Hezekiya anapemphela kuti: ‘Conde Yehova, tipulumutseni, kuti onse adziŵe kuti inu nokha ndinu Mulungu woona.’ Yehova anamuyankha kuti: ‘Mfumu ya Asuri siidzaloŵa mu Yerusalemu. Nidzauteteza mzinda wanga.’

Senakeribu anali na cidalilo conse kuti Yerusalemu adzakhala mzinda wake. Koma tsiku lina usiku, Yehova anatuma mngelo ku msasa wa asilikali kunja kwa mzinda. Mngeloyo anapha asilikali 185,000! usikuwo. Asilikali onse amphamvu a Senakeribu anaphedwa. Koma kwa iye kunalibe mwina mocitila, anangobwelela kwawo atagonja. Yehova anateteza Hezekiya komanso Yerusalemu, monga mmene analonjezela. Sembe unaliko ku Yerusalemu, kodi ukanam’dalila Yehova?

“Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulila onse oopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.”—Salimo 34:7

Mafunso: Kodi Yehova anateteza bwanji Yerusalemu? Kodi uganiza kuti na iwe Yehova angakuteteze?

2 Mafumu 17:1-6; 18:13-37; 19:1-37; 2 Mbiri 32:1-23

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani