LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 69 tsa. 164-tsa. 165 pala. 2
  • Gabirieli Aonekela kwa Mariya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Gabirieli Aonekela kwa Mariya
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mngelo Acezela Mariya
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 69 tsa. 164-tsa. 165 pala. 2
Mngelo Gabirieli aonekela kwa Mariya

PHUNZILO 69

Gabirieli Aonekela kwa Mariya

Mngelo aonekela kwa Yosefe m’maloto

Elizabeti anali na m’bululu wake wacitsikana, Mariya, amene anali kukhala mu mzinda wa Nazareti ku Galileya. Mariya anali wotomeledwa kwa Yosefe kalipentala. M’mwezi wa 6 wa mimba ya Elizabeti, mngelo Gabirieli anaonekelanso kwa Mariya. Ndipo anati kwa iye: ‘Mtendele ukhale nawe Mariya. Yehova wakukomela mtima kwambili.’ Koma Mariya sanamvetsetse zimene Gabirieli anali kutanthauza. Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Udzakhala na mimba, na kubala mwana wamwamuna, ndipo udzam’patse dzina lakuti Yesu. Iye adzalamulila monga Mfumu. Ufumu wake udzakhalapo mpaka kale-kale.’

Koma Mariya anati: ‘Ine ndine namwali. Nanga ningakhale bwanji na mwana?’ Gabirieli anati: ‘Palibe cosatheka kwa Yehova. Mzimu woyela udzafika pa iwe, ndipo udzakhala na mwana wamwamuna. Nayenso m’bale wako Elizabeti ali na mimba.’ Pamenepo Mariya anati: ‘Ndine kapolo wa Yehova. Zimene mwakamba zicitike kwa ine.’

Yosefe atenga mariya monga mkazi wake

Kenako Mariya anapita kukacezela Elizabeti ku mzinda wa ku mapili. Mariya atapeleka moni, mwana amene anali m’mimba mwa Elizabeti analumpha. Podzazidwa na mzimu woyela, Elizabeti anati: ‘Mariya, Yehova wakudalitsadi. Ni mwayi wapadela kukhala na mayi wa Ambuye anga m’nyumba muno.’ Mariya anati: ‘Nitamanda Yehova na mtima wanga wonse.’ Mariya anakhala na Elizabeti kwa miyezi itatu, kenako anabwelela kwawo ku Nazareti.

Yosefe atadziŵa kuti Mariya ali na mimba, anafuna kutsiliza citomelo cawo. Koma mngelo anaonekela kwa Yosefe m’maloto na kumuuza kuti: ‘Usacite mantha kum’kwatila. Sanacite colakwa ciliconse.’ Conco, Yosefe anakwatila Mariya, na kumubweletsa ku nyumba kwake.

‘Ciliconse cimene Yehova wafuna kucita amacita, kumwamba ndi pa dziko lapansi.’—Salimo 135:6

Mafunso: Kodi Gabirieli anamuuza ciani Mariya za mwana wake? Nanga Elizabeti na Mariya anamvela bwanji pa zimene zinawacitikila?

Mateyu 1:18-25; Luka 1:26-56; Yesaya 7:14; 9:7; Danieli 2:44; Agalatiya 4:4

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani