LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 92 tsa. 214-tsa. 215 pala. 1
  • Yesu Aonekela kwa Ophunzila Ake Asodzi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Aonekela kwa Ophunzila Ake Asodzi
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 92 tsa. 214-tsa. 215 pala. 1
Yesu akamba na ophunzila ake pamene nsomba zili pa moto

PHUNZILO 92

Yesu Aonekela kwa Ophunzila Ake Asodzi

M’kupita kwa nthawi Yesu ataonekela kwa atumwi, Petulo anaganiza zopita kukapha nsomba ku Nyanja ya Galileya. Tomasi, Yakobo, Yohane, na ophunzila ena anam’konkha. Usiku wonse anaponya maukonde awo koma osagwilako olo imodzi.

M’mawa kutaca, anangoona munthu ataimilila m’mbali mwa nyanja. Munthuyo mofuula anawafunsa kuti: ‘Kodi mwagwilako nsomba iliyonse?’ Iwo anayankha kuti: “Iyai!” Ndiyeno munthuyo anati: “Ponyani ukonde wanu kulamanja kwa boti yanu.” Atacita zimenezo, nsomba zinadzala phamu-phamu mu ukonde wawo, cakuti analephela kuukokela m’boti. Pamenepo Yohane anazindikila kuti munthuyo anali Yesu. Ndipo anati: ‘Ni Ambuye!’ Petulo kungomvela zimenezo anangoti joo m’madzi cubwi! n’kuyamba kunyaila kumtunda kwa Yesu. Ophunzila ena analondola na boti.

Atafika ku mtunda, anapeza mkate na nsomba zili pa moto. Yesu anawauza kuti abweletseko nsomba zimene anaphazo kuti awonjezele cakudya cimene anali naco. Kenako anati: ‘Bwelani mudye cakudya cam’maŵa.’

Petulo afika kumene kuli Yesu, ndipo ophunzila ena atsatila m’boti

Atatsiliza kudya, Yesu anafunsa Petulo kuti: ‘Kodi umanikonda kuposa usodzi?’ Petulo anati: ‘Inde Ambuye, imwe mudziŵa kuti nimakukondani.’ Yesu anati: ‘Kansi dyetsa ana a nkhosa anga.’ Yesu anam’funsanso kuti: ‘Petulo, kodi umanikonda?’ Petulo anati: ‘Ambuye, mudziŵa kuti nikukondani.’ Yesu anamuuza kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” Pamene Yesu anam’funsa kacitatu, Petulo anamvela cisoni. Iye anati: ‘Ambuye, inu mudziŵa zonse. Mudziŵa kuti nikukondani.’ Yesu anati: “Dyetsa ana a nkhosa anga.” Ndiyeno anauza Petulo kuti: ‘Pitiliza kunitsatila.’

“[Yesu] anawauza kuti: ‘Nditsatileni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.’ Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatila.”—Mateyu 4:19, 20

Mafunso: Kodi Yesu anawacitila cozizwitsa cotani ophunzila ake? Uganiza n’cifukwa ciani Yesu anafunsa Petulo katatu konse kuti: “Kodi umanikonda?”

Yohane 21:1-19, 25; Machitidwe 1:1-3

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani