LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 97 tsa. 226-tsa. 227 pala. 2
  • Koneliyo Alandila Mzimu Woyela

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Koneliyo Alandila Mzimu Woyela
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Petulo Acezela Korneliyo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Limbikilani Monga Anacitila Petulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 97 tsa. 226-tsa. 227 pala. 2
Koneliyo alandila Petulo m’nyumba yake

PHUNZILO 97

Koneliyo Alandila Mzimu Woyela

Ku Kaisareya kunali kukhala munthu wina waudindo waukulu, dzina lake Koneliyo. Analinso mkulu wa asilikali m’boma la Roma. Ngakhale sanali Myuda, Ayuda anali kum’lemekeza kwambili. Iye anali kuthandiza kwambili anthu ovutika. Koneliyo anali kukhulupilila mwa Yehova, ndipo anali kupemphela kwa iye nthawi zonse. Tsiku lina, mngelo anaonekela kwa Koneliyo. Mngeloyo anamuuza kuti: ‘Mulungu wamvela mapemphelo ako. Tumiza anthu apite ku mzinda wa Yopa, kumene amakhala Petulo. Akam’pemphe kuti abwele kwa iwe.’ Nthawi yomweyo, Koneliyo anatuma amuna atatu kupita ku Yopa, pa mtunda wa makilomita pafupi-fupi 50, kuloŵela kum’mwela.

Ku Yopa kumeneko, Petulo anaona masomphenya. M’masomphenyawo, anaona nyama zimene Ayuda sanali kuloledwa kudya. Ndiyeno anamvela mawu omuuza kuti adye nyama zimenezo. Petulo anakana, amvekele: ‘Cibadwile, nikalibe kudyapo nyama zodetsedwa.’ Koma mawuwo anamuuza kuti: ‘Usakambe kuti nyama izi n’zodetsedwa. Mulungu waziyeletsa.’ Petulo anauzidwanso kuti: ‘Pita ukakumane ndi amuna atatu amene ali pa khomo la nyumba yako.’ Petulo anapita kukakumana ndi anthuwo. Iye atawafunsa cifukwa cimene anabwelela, iwo anati: ‘Tatumiwa na Koneliyo mkulu wa asilikali m’boma la Roma. Iye akamba kuti tikutengeni tipite ku nyumba kwake ku Kaisareya.’ Pamenepo Petulo anapempha alendowo kuti aloŵe m’nyumba agone. Tsiku lotsatila, iye anapita nawo anthuwo ku Kaisareya, pamodzinso na abale ena a ku Yopa.

Pamene Koneliyo anaona Petulo, anagwada pansi. Koma Petulo anati: ‘Nyamukani! Ine ndine munthu monga imwe. Mulungu wanituma kuti nibwele kuno ku nyumba kwanu, ngakhale kuti Ayuda saloŵa m’nyumba za anthu a mitundu. Conde, niuzeni lomba cimene mwaniitanila.’

Koneliyo anauza Petulo kuti: ‘Papita masiku anayi, n’nali kupemphela kwa Mulungu. Ndipo mngelo ananiuza kuti nikuitaneni. Conde, tiphunzitseni mawu a Yehova.’ Petulo anati: ‘Nadziŵa kuti Mulungu alibe tsankho. Amalandila aliyense amene afuna kum’lambila.’ Petulo anaŵaphunzitsa zinthu zambili zokhudza Yesu. Kenako mzimu woyela unabwela pa Koneliyo, komanso pa anthu ena amene anali naye, ndipo onse anabatizidwa.

“[Mulungu] amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—Machitidwe 10:35

Mafunso: N’cifukwa ciani Petulo anakana kudya nyama zodetsedwa? N’cifukwa ciani Yehova anauza Petulo kupita ku nyumba ya munthu wa mitundu?

Machitidwe 10:1-48

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani