LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 99 tsa. 230-tsa. 231 pala. 4
  • Woyang’anila Ndende Aphunzila Coonadi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Woyang’anila Ndende Aphunzila Coonadi
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • “Mtendele wa Mulungu ... Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 99 tsa. 230-tsa. 231 pala. 4
Woyang’anila ndende ku Filipi apeza zitseko za ndende n’zotseguka koma akaidi onse alimo

PHUNZILO 99

Woyang’anila Ndende Aphunzila Coonadi

Ku Filipi, kunali mtsikana wina wanchito amene anali na ciŵanda. Ciŵandaco cinali kum’pangitsa kulosela zakutsogolo. Mwanjila imeneyo, anali kupangila mabwana ake ndalama zambili. Paulo na Sila atafika ku Filipi, mtsikana uja anawalondola kulikonse kwa masiku ambili. Ndipo ciŵandaco cinam’pangitsa kumafuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wam’mwambamwamba!” Paulo atalema nazo, anauza ciŵandaco kuti: ‘M’dzina la Yesu, tuluka mwa mtsikanayu!’ Pamenepo, ciŵanda cija cinacoka mwa mtsikanayo.

Mabwana a mtsikanayo ataona kuti Paulo wacotsapo njila yawo yopangila ndalama kupitila mwa mtsikana uja, anakalipa kwambili. Anagwila Paulo na Sila na kuŵapeleka kwa oweluza milandu. Atafika kumeneko iwo anati: ‘Anthu awa akuphwanya malamulo, ndipo akusokoneza mzinda wonse!’ Oweluzawo analamula kuti am’kwapule Paulo na Sila, na kuwaponya m’ndende. Woyang’anila ndende anawaika m’cipinda ca mkati-kati ca ndende, kumene kunali mdima wa ndiwe yani, na kuwamanga m’matangadza.

Ali m’ndendemo, Paulo na Sila anali kuimbila Yehova zitamando, ndipo akaidi ena anali kumvetsela. Ndiyeno pakati pa usiku, mwadzidzidzi panacitika civomezi camphamvu cimene cinagwedeza ndende yonseyo. Zitseko za ndendeyo zinatseguka, ndipo unyolo na matangadza anamasuka. Pamenepo woyang’anila ndendeyo anathamanga kuloŵa mkati-kati mwa ndendeyo. Anangoona kuti zitseko zonse n’zotseguka. Poganiza kuti akaidi onse athaŵa, iye anasolola lupanga kuti adziphe.

Koma Paulo anafuula kuti: ‘Usadzivulaze! Tonse tilimo!’ Woyang’anila ndendeyo anathamanga kukagwada pamaso pa Paulo na Sila. Iye anaŵafunsa kuti: “Ndicite ciyani kuti ndipulumuke?” Iwo anamuyankha kuti: ‘Iweyo, komanso onse a m’banja mwako mufunika kukhulupilila mwa Yesu.’ Kenako Paulo na Sila anaŵaphunzitsa mawu a Yehova, ndipo woyang’anila ndendeyo na onse a m’banja lake anabatizika.

“Anthu adzakugwilani ndi kukuzunzani, adzakupelekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakutengelani kwa mafumu ndi abwanamkubwa cifukwa ca dzina langa. Umenewu udzakhala mpata wanu wocitila umboni.”—Luka 21:12, 13

Mafunso: N’cifukwa ciani Paulo na Sila anaponyedwa m’ndende? Kodi woyang’anila ndende uja anaphunzila bwanji coonadi?

Machitidwe 16:16-34

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani