PHUNZILO 102
Masomphenya a Yohane
Pamene mtumwi Yohane anali m’ndende pa cisumbu ca Patimo, Yesu anamuonetsa masomphenya kapena kuti zithunzi zokwanila 16, zoonetsa zinthu zakutsogolo. Masomphenyawo anaonetsa mmene dzina la Yehova lidzayeletsedwela, mmene Ufumu wake udzabwelela, na mmene cifunilo cake cidzacitikila pa dziko lapansi monga kumwamba.
M’masomphenya ena, Yohane akuona Yehova ali kumwamba pa mpando wake wacifumu waulemelelo. Akulu 24 ovala zisoti zacifumu azungulila mpando wacifumu wa Yehova. Ndipo ku mpando wacifumuwo kukucokela kuwala kong’anima na mabingu amphamvu. Akulu 24 aja akuŵelama pamaso pa Yehova na kum’lambila. M’masomphenya enanso, Yohane akuona khamu lalikulu la anthu olambila Yehova, ocokela m’dziko lililonse, mtundu uliwonse, na citundu ciliconse. Mwanawankhosa amene ni Yesu, awasamalila na kuŵatsogolela ku madzi a moyo. M’masomphenya enanso, Yohane akuona Yesu akuyamba kulamulila monga Mfumu kumwamba, pamodzi na akulu 24. M’masomphenya okonkhapo, Yohane aona Yesu akumenyana na cinjoka, amene ni Satana na ziŵanda zake. Koma Yesu awacotsa kumwambako na kuwaponyela pa dziko lapansi.
Ndiyeno Yohane aona cithunzi cokongola ca Mwanawankhosa, ataimilila pa Phili la Ziyoni kumwamba pamodzi ndi a 144,000. Akuonanso mngelo akuuluka uku na uku pa dziko lapansi, akuuza anthu kuti aziyopa Mulungu na kum’patsa ulemelelo.
M’masomphenya otsatilapo, pabuka nkhondo ya Aramagedo. Pa nkhondo imeneyo, Yesu na asilikali ake agonjetsa dziko la Satana. M’masomphenya othela, Yohane aona mgwilizano wamtendele kumwamba na pa dziko lapansi. Satana pamodzi na onse omutsatila awonongedwa kothelatu. Aliyense kumwamba na pa dziko lapansi akulemekeza dzina la Yehova, na kulambila iye yekha basi.
“Ndidzaika cidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza cidendene.”—Genesis 3:15