Mawu Oyamba a Cigawo 6
Pamene Aisiraeli anafika ku Dziko Lolonjezedwa, cihema cinakhala likulu lolambililako Yehova m’dzikolo. Ansembe anali kuphunzitsa Cilamulo, ndipo oweluza anali kutsogolela mtundu. Cigawo cino cionetsa mmene zosankha na zocita za munthu zimakhudzila anthu ena. Mwisiraeli aliyense anali na udindo kwa Yehova, komanso kwa munthu mnzake. Onetsani mmene zocita za Debora, Naomi, Yoswa, Hana, mwana wamkazi wa Yefita, na Samueli zinakhudzila anthu ambili. Onetsani kuti ngakhale anthu amene sanali Aisiraeli, monga Rahabi, Rute, Yaeli, komanso Agibeoni, anasankha kukhala kumbali ya Aisiraeli cifukwa anadziŵa kuti Mulungu anali nawo.