Mawu Oyamba a Cigawo 10
Yehova ni Mfumu ya cilengedwe conse. Iye nthawi zonse wakhala akulamulila, ndipo adzalamulilabe kwamuyaya. Mwacitsanzo, anapulumutsa Yeremiya m’citsime cozama. Anapulumutsa Sadirake, Mesake na Abedinego m’ng’anjo ya moto, komanso Danieli m’dzenje la mikango. Yehova anateteza Esitere kuti apulumutse anthu onse a mtundu wake. Iye sadzalola kuti zoipa zipitilize kwamuyaya. Maulosi okhudza fano lalikulu komanso mtengo waukulu, amatitsimikizila kuti Ufumu wa Yehova posacedwa udzacotsapo zoipa zonse na kuyamba kulamulila pa dziko lapansi.