NYIMBO 41
Mvelani Pemphelo Langa Conde
Yopulinta
(Salimo 54)
1. Nidzakutamandani M’lungu.
Imwe ndimwe Atate wanga.
Dzina lanu ni lalikulu.
(KOLASI)
Conde Yehova, nimveleni.
2. Nikuyamikani Yehova.
Mwanipatsa mphatso ya moyo.
Imwe mumanisamalila.
(KOLASI)
Conde Yehova, nimveleni.
3. M’lungu wanga nithandizeni,
Nipilile mavuto onse.
Nifuna kucita zabwino.
(KOLASI)
Conde Yehova, nimveleni.
(Onaninso Eks. 22:27; Sal. 106:4; Yak. 5:11)