NYIMBO 105
“Mulungu Ndiye Cikondi”
Yopulinta
(1 Yohane 4:7, 8)
1. Mulungu ndiye cikondi,
Tikhale monga iye.
Tikakhala na cikondi
Iye adzatiyanja.
Tidzapeza madalitso,
Tidzapeza cimwemwe.
Monga otsatila Khristu
Tionetse cikondi.
2. Ngati tikonda Yehova
Tidzacita zabwino.
Iye adzatiphunzitsa
Kukhala acikondi.
Cikondi citilimbitsa
Potumikila M’lungu.
Tikakhala na cikondi,
Sitidzacita nsanje.
3. Tisabwezele coipa,
Tikhale acifundo.
Tikonde abale athu,
Tikhale monga M’lungu.
Ngati ena ‘tilakwila
Tiŵakhululukile.
Mu zocita zathu zonse
Tikhale acikondi.
(Onaninso Maliko 12:30, 31; 1 Akor. 12:31–13:8; 1 Yoh. 3:23.)