LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 25
  • Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kodi Mulungu Woona Ndani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 25
Phunzilo 25. Dziko lapansi kuliona kucokela kuthambo.

PHUNZILO 25

Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Baibo imavomeleza kuti “anthu amakhala na moyo waufupi komanso wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Kodi ici ndiye cinali cifunilo ca Mulungu kwa ife? Yankho ni lakuti iyayi. Koma kodi colinga cake kwa ife n’ciyani? Kodi colingaco cidzakwanilitsikadi? Onani mayankho olimbikitsa a m’Baibo.

1. Kodi Yehova amatifunila moyo wotani?

Yehova amatifunila moyo wabwino kopambana. Pamene Yehova analenga anthu oyamba, Adamu na Hava, anawaika m’malo okongola a paradaiso, ochedwa Munda wa Edeni. Ndiyeno “Mulungu anawadalitsa ndi kuwauza kuti: ‘mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi ndipo muliyang’anile.’” (Genesis 1:28) Yehova anafuna kuti iwo akhale na ŵana, kuti apange dziko lapansi kukhala paradaiso, komanso kuti azisamalila zinyama. Colinga cake cinali cakuti anthu onse akhale na thanzi langwilo na moyo wamuyaya.

Ngakhale kuti zinthu sizinacitike mwa njila imeneyo,a colinga ca Mulungu sicinasinthe ayi. (Yesaya 46:10, 11) Iye akufunabe kuti anthu omvela akakhale na moyo wangwilo wopanda mavuto alionse.—Ŵelengani Chivumbulutso 21:3, 4.

2. Kodi tingakhale bwanji na moyo waphindu pali pano?

Yehova anatilenga na ‘zosowa zauzimu,’ kutanthauza cikumbumtima cofuna kumulambila. (Ŵelengani Mateyu 5:3-6.) Amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wa thi-thi-thi, kuti ‘tiziyenda m’njila zake zonse, kuti tizim’konda,’ komanso kuti tizim’tumikila na “mtima . . . wonse.” (Deuteronomo 10:12; Salimo 25:14) Tikamacita zimenezi, tidzapeza cimwemwe ceniceni ngakhale timakumana na mavuto. Kulambila Yehova kumatipatsa moyo waphindu wocita cifunilo ca Mulungu.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani za cikondi cacikulu cimene Yehova anaonetsa potikonzela dziko lapansi, komanso colinga cake cabwino cimene amatiphuzitsa m’Mawu ake.

Adamu na Hava akuyang’ana malo awo okongola a munda wa Edeni, odzala na zomela zobiliŵila bwino na zinyama.

3. Yehova ali na colinga cabwino kwambili pa anthu

Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

VIDIYO: N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?—Kachigawo Kake (1:41)

  • Kodi Mulungu anali na colinga cotani polenga dziko lapansi lokongola?

Ŵelengani Mlaliki 3:11, kenako kambilanani funso ili:

  • Kodi zimenezi zikuuzani ciyani za Yehova?

4. Colinga ca Yehova sicinasinthe

Ŵelengani Salimo 37:11, 29, komanso Yesaya 55:11, kenako kambilanani funso ili:

  • Kodi timadziŵa bwanji kuti colinga ca Yehova pa ife sicinasinthe?

A. Nyumba yowonongeka. Mtenje wake ni wopasuka, mawindo ake ni ophwanyika, ndipo pabwalo pake zinyalala zili bwee paliponse. B. Nyumba imodzi-modziyo, tsopano inakonzedwa, ikuoneka yokongola, pabwalo pakenso m’pokonzedwa bwino.

Nyumba yowonongeka cifukwa cosasamalidwa ingakozedwenso. Mofananamo, dziko lapansi limene anthu aliwononga, Mulungu adzalikonzanso kaamba ka anthu omukonda

5. Kulambila Yehova kumapangitsa moyo wathu kukhala waphindu

Kudziŵa colinga ca moyo kumatipatsa cimwemwe. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

VIDIYO: N’naphunzila za Colinga ca Moyo (5:03)

  • Kodi Terumi anapindula motani atadziŵa colinga ca moyo?

Ŵelengani Mlaliki 12:13, na kukambilana funso ili:

  • Poona zambili zimene Yehova waticitila, kodi ifenso tiyenela kucita ciyani poonetsa kuyamikila kwathu?

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “Kodi Mulungu anatilengelanji pamene anali kudziŵa kuti tidzafa?”

  • Inu mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Yehova amafuna kuti tikapeze moyo wosatha wopanda mavuto pano padziko lapansi. Ngati timulambila na mtima wathu wonse, umoyo wathu udzakhala waphindu ngakhale pali pano.

Mafunso Obweleza

  • Kodi poyamba, colinga ca Yehova kwa Adamu na Hava cinali ciyani?

  • Kodi timadziŵa bwanji kuti colinga ca Mulungu kwa anthu sicinasinthe?

  • Kodi moyo weniweni waphindu tingaupeze bwanji?

Colinga

FUFUZANI

Onani umboni woonetsa kuti munda wa Eden unalikodi.

“Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?” (Nsanja ya Mlonda, January 1, 2011)

Dziŵani cifukwa cake tiyenela kutsimikiza kuti dziko lapansi lidzakhalapobe kwamuyaya.

“Kodi Dzikoli Lidzatha?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Dziŵani mmene Baibo ingakuthandizileni kupeza moyo waphindu.

“Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani mmene munthu amene anali kuganiza kuti zonse anazipeza pa umoyo anazindikilila cimene anali kusoŵeka.

Moyo Wanga Tsopano Uli na Colinga (3:55)

a M’phunzilo lotsatila, mudzamva kuti cinalakwika n’ciyani.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani