PHUNZILO 52
Cifukwa Cake Tiyenela Kusamala na Mavalidwe Komanso Maonekedwe Athu
Tonsefe tili na makonda athu pa nkhani ya mavalidwe na maonekedwe. Tikangotsatila mfundo zocepa za m’Baibo komanso zosavuta, tingapeze mavalidwe a kumtima kwathu komanso okondweletsa Yehova. Tiyeni tikambilaneko zina mwa mfundo za m’Baibo zimenezo.
1. Kodi ni mfundo ziti zingatithandize posankha mavalidwe na kudzikongoletsa?
Tiyenela kusankha “zovala zoyenela, povala mwaulemu ndi mwanzelu,” komanso mwa maonekedwe aukhondo ‘olemekeza Mulungu.’ (1 Timoteyo 2:9, 10) Ganizilani mfundo zinayi izi: (1) Mavalidwe athu azikhala ‘oyenela.’ Monga mumaonela ku misonkhano ya mpingo, anthu a Yehova ali na makonda osiyana-siyana pa mavalidwe. Ngakhale n’conco, mavalidwe athu komanso kakonzedwe kathu ka tsitsi, kamaonetsa ulemu kwa Mulungu amene timamulambila. (2) Kuvala “mwaulemu” kumatanthauza kuti mavalidwe athu sayenela kutenthetsa thupi anthu ena, komanso safunika kukhala odzionetsela. (3) Timakhala ‘anzelu’ tikamapewa kutengela mafasho alionse obwela a mavalidwe, komanso a makonzedwe a tsitsi. (4) Maonekedwe athu azionetsa nthawi zonse kuti ‘timalemekeza Mulungu.’ Mwa kutelo, ena adzaona kuti ndife olambila oona.—1 Akorinto 10:31.
2. Kodi maonekedwe athu angawakhudze bwanji olambila anzathu?
Ngakhale kuti tili na ufulu wosankha zimene tingakonde kuvala, tiyenela kuganizila mmene maonekedwe athu angakhudzile anthu ena. Conco tiyenela kusamala kuti tisakhumudwitse aliyense. M’malo mwake, ‘tizikondweletsa anzathu pa zinthu zabwino zowalimbikitsa.’—Ŵelengani Aroma 15:1, 2.
3. Kodi anthu ena angakopeke bwanji na kulambila koona cifukwa ca maonekedwe athu?
Ngakhale kuti timayesetsa kuvala moyenela panthawi iliyonse, tiyenela kusamala kwambili maka-maka pokasonkhana ku mpingo, kapena polalikila. Sitifuna kunyozetsa uthenga wofunika kwambili umene timatengela anthu. M’malo mwake, timafuna kuti maonekedwe athu azikokela anthu ku coonadi, kotelo kuti “akometsele ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu.”—Tito 2:10.
KUMBANI MOZAMILAPO
Onani zimene zingatithandize kutsimikiza kuti tavala moyenela, komanso tikuoneka bwino monga Akhristu.
Maonekedwe athu amaonetsa ngati anthu audindo timawalemekeza kapena ayi. Ngakhale kuti Yehova amayang’ana za mumtima mwa munthu, maonekedwe athu nawonso ayenela kupeleka ulemu kwa iye
4. Maonekedwe abwino amapeleka ulemu kwa Yehova
Kodi cifukwa cacikulu cosamalila maonekedwe athu n’ciyani? Ŵelengani Chivumbulutso 4:11, na kukambilana mafunso aya:
Pokhala atumiki a Yehova, n’cifukwa ciyani tiyenela kusamala na mavalidwe athu?
Kodi muganiza n’zofunikiladi kusamala za maonekedwe athu, pamene tili ku misonkhano kapena mu ulaliki? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?
5. Mmene tingasankhile mwanzelu mavalidwe komanso maonekedwe
Kaya zovala zathu n’zodula kapena n’zochipa, zizikhala zaukhondo komanso zogwilizana na cocitika cimene tazivalila. Ŵelengani 1 Akorinto 10:24, komanso 1 Timoteyo 2:9, 10. Ndiyeno, kambilanani cifukwa cake tiyenela kupewa kuvala zovala . . .
zotayilila kapena zocotsa ulemu.
zothina, zoonetsa thupi, kapena zotenthetsa thupi anthu ena.
Ngakhale kuti Akhristu sali pansi pa Cilamulo ca Mose, cilamuloco cimaonetsa maganizo a Yehova. Ŵelengani Deuteronomo 22:5, na kukambilana funso ili:
N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa mavalidwe kapena makonzedwe a tsitsi opangitsa amuna kuoneka monga akazi, kapena akazi kuoneka monga amuna?
Ŵelengani 1 Akorinto 10:32, 33, komanso 1 Yohane 2:15, 16, na kukambilana mafunso aya:
N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala kuti maonekedwe athu asamakhumudwitse ena, kumene tikukhala kapena mu mpingo?
Kodi ni mavalidwe otani kapena makonzedwe a tsitsi ofala kumene mukukhala?
Kodi muganiza kuti ena mwa mafasho amenewo si oyenelela kwa Mkhristu? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?
ikhoza kuvala kapena kukonza tsitsi lathu m’njila zosiyana-siyana, koma zokondweletsabe Yehova
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nili na ufulu wovala mulimonse mmene nifunila.”
Kodi mukuvomeleza zimenezi? Cifukwa ciyani?
CIDULE CAKE
Tikapanga zisankho zabwino pa nkhani ya maonekedwe, timalemekeza Yehova komanso anthu ena.
Mafunso Obweleza
N’cifukwa ciyani mavalidwe athu, komanso kakonzedwe kathu ka tsitsi, ni nkhani yofunika kwa Yehova?
Ni mfundo ziti zingatithandize kupanga zisankho zabwino pa nkhani ya maonekedwe?
Kodi maonekedwe athu angakhudze bwanji mmene anthu amaonela kulambila koona?
FUFUZANI
Onani uthenga umene mavalidwe anu angapeleke.
“Kodi Ndimakonda Kuvala Zovala Zotani?” (Nkhani ya pawebusaiti)
Dziŵani cifukwa cake n’kwanzelu kuyamba mwaganiza bwino musanadzilembe-lembe matatuu pathupi panu.
“Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yodzilemba Matatuu?” (Nkhani ya pawebusaiti)
Onani mfundo zinanso zimene zingakuthandizeni popanga zisankho.
“Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?” (Nsanja ya Mlonda, September 2016)