LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 10
  • Kudzipeleka pa Nchitoyi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kudzipeleka pa Nchitoyi
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anacitila Zimenezi
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kusankha Kutumikila Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzila Anga’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 10

KUPANGA OPHUNZILA

Yesu na Nikodemo akukambilana usiku m’bwalo.

Yohane 3:1, 2

PHUNZILO 10

Kudzipeleka pa Nchitoyi

Mfundo Yaikulu: “Tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeniyeniyo, cifukwa tinakukondani kwambili.”—1 Ates. 2:8.

Mmene Yesu Anacitila Zimenezi

Yesu na Nikodemo akukambilana usiku m’bwalo.

VIDIYO: Yesu Aphunzitsa Nikodemo

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Yohane 3:1, 2. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Muganiza n’cifukwa ciyani Nikodemo anasankha kupita kwa Yesu usiku?—Onani Yoh. 12:42, 43.

  2. Kodi Yesu polola kukumana na Nikodemo usiku, anaonetsa bwanji kuti anali wodzipeleka pa nchito yopanga ophunzila?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Cifukwa timakonda anthu, timadzipeleka kuti tiwathandize kukhala ophunzila.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Muziphunzila pa nthawi na malo okomela wophunzila Baibo wanu. Iye angasankhe tsiku lakuti-lakuti pa mlungu, kapenanso nthawi yakuti-yakuti. Kodi angakonde kumaphunzilila ku nchito kwake, ku nyumba kwake, kapena pa malo a anthu onse? Monga kungathekele, sinthilani ku nthawi, tsiku, na malo omwe angam’komele.

4. Musamalumphe-lumphe kuphunzila. Ngati simudzakhalapo, musalumphe mlungu umenewo. Ganizilani izi m’malo mwake:

  1. Kodi mungaphunzilebe naye pa tsiku lina mlungu umenewo?

  2. Kodi mungatsogozebe phunzilolo pa foni, kapena pa vidiyokomfalensi?

  3. Kodi mungapemphe wofalitsa wina kuti akutsogozeleni?

5. Pemphani thandizo kwa Yehova. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukhalabe wodzipeleka pa kuthandiza wophunzila wanu, ngakhale kuti amaphonya-phonya kuphunzila, kapena amacedwa kugwilitsa nchito zimene mukuphunzila. (Afil. 2:13) N’kutheka kuti wophunzila wanu ali na makhalidwe abwino ambili; muzim’pemphelela kuti awakulitse makhalidwe amenewo.

ONANINSO MALEMBA AWA

Miy. 3:27; Mac. 20:35; 2 Akor. 12:15

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani