LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 11
  • Kuphunzitsa M’njila Yosavuta Kumva

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuphunzitsa M’njila Yosavuta Kumva
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anacitila Zimenezi
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kuti Akakhale Ophunzila Obatizika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Motsogozela Phunzilo la Baibo Poseŵenzetsa Buku la “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!”
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 11

KUPANGA OPHUNZILA

Yesu akuphunzitsa gulu la anthu kufupi na nyanja. Mbalame zikuuluka m’mwamba, komanso pali maluŵa a m’chile.

Mat. 6:25-27

PHUNZILO 11

Kuphunzitsa M’njila Yosavuta Kumva

Mfundo Yaikulu: ‘Muzilankhula zomveka.’—1 Akor. 14:9.

Mmene Yesu Anacitila Zimenezi

Yesu akuphunzitsa gulu la anthu kufupi na nyanja. Mbalame zikuuluka m’mwamba, komanso pali maluŵa a m’chile.

VIDIYO: Yesu Apeleka Fanizo la Mmene Atate Wathu Amatisamalila

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Mateyu 6:25-27. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Kodi Yesu anafanizila motani mmene Yehova amatisamalila?

  2. Ngakhale kuti Yesu anali kudziŵa zambili zokhudza mbalame, kodi anasankha mfundo iti yosavuta kumva imene anaphunzitsilapo? N’cifukwa ciyani njila imeneyi ili yothandiza ngako?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Tikamaphunzitsa mosavuta kumva, anthu adzakumbukila zimene tawaphunzitsa, komanso zidzawafika pa mtima.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Musamafotokoze zambili. M’malo mofotokoza zonse zimene mudziŵa pa nkhani imene mukuphunzitsa, kambani maka-maka mfundo zili m’buku limene mukuphunzila. Mukafunsa funso, yembekezelani moleza mtima kuti wophunzila wanu ayankhe. Ngati yankho salidziŵa kapena wayankha zosemphana ni zimene Baibo imaphunzitsa, funsani mafunso oonjezela omuthandiza kuimvetsa nkhaniyo. Akaimvetsa mfundo yaikulu, pitani patsogolo.

4. Gwilitsani nchito zimene akudziŵa kale kuti amvetse mfundo zatsopano. Mwacitsanzo, musanayambe kuphunzila za ciukitso ca akufa, mungamufunseko zimene anaphunzila kale za mkhalidwe wa akufa.

5. Seŵenzetsani mafanizo, koma mosamala. Musanapeleke fanizo dzifunseni kuti:

  1. ‘Kodi fanizo ili n’losavuta kumva?’

  2. ‘Kodi wophunzila wanga adzalimva mosavuta?’

  3. ‘Kodi lidzamuthandiza kukumbukila mfundo yaikulu—m’malo mwa fanizo lokhalo?’

ONANINSO MALEMBA AWA

Mat. 11:25; Yoh. 16:12; 1 Akor. 2:1

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani