LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 9/1 tsa. 32
  • Kuyankha Mafunso a M’baibo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyankha Mafunso a M’baibo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Mungacite Ciani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
  • Tetezani Cikwati Canu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Cikwati Ni Mphatso Yocokela Kwa Mulungu
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Khalani ndi Banja Lolimba ndi Lacimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 9/1 tsa. 32

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO

N’ciani cingathandize kuti banja likhale lacimwemwe?

Malangizo a m’Baibo amathandiza kuti banja likhale lacimwemwe cifukwa cakuti ndi ocokela kwa Yehova Mulungu amene anayambitsa banja. Baibo imatiphunzitsa makhalidwe abwino amene amathandiza kuti banja likhale lacimwemwe. Ndiponso imaticenjeza kuti tipewe makhalidwe amene angaononge cikwati. Imatiphunzitsanso kalankhulidwe kabwino kamene kamapangitsa banja kukhala lacimwemwe.—Ŵelengani Akolose 3:8-10, 12-14.

Mwamuna ndi mkazi ayenela kulemekezana. Ngati io acita mbali yao imene Mulungu anawapatsa, angakhale acimwemwe.—Ŵelengani Akolose 3:18, 19.

N’ciani cimapangitsa banja kukhala lolimba?

Mwamuna ndi mkazi angakhale limodzi kwa nthawi yaitali ngati amakondana. Mulungu amatiphunzitsa kuti tizikondana. Iye ndi Mwana wake Yesu, anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tingakhalile ndi cikondi codzimana.—Ŵelengani 1 Yohane 4:7, 8, 19.

Ngati mwamuna ndi mkazi amalemekeza cikwati monga makonzedwe a Mulungu, io amakhala ndi banja lolimba. Mulungu analinganiza kuti cikwati cikhale m’gwilizano wokhalitsa pakati pa mwamuna ndi mkazi ndi colinga cakuti mabanja akhale otetezeka. N’zotheka cikwati kukhalitsa cifukwa cakuti Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi m’njila yakuti azigwilizana. Iye anawalenganso m’cifanizilo cake, conco angathe kusonyezana cikondi.—Ŵelengani Genesis 1:27; 2:18, 24.

Kuti mudziŵe zambili onani nkhani 14 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Mungatenge buku limeneli pa www.jw.org

[Cithunzi papeji 32]

Kodi ndi kalankhulidwe kotani kamene kamapangitsa kuti banja likhale lacimwemwe?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani