Upainiya Umalimbitsa Unansi Wathu Ndi Mulungu
“Kuimbila Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.”—SAL. 147:1.
MAFUNSO OBWELELAMO
Kodi kucita upainiya kungalimbitse bwanji ubwenzi wanu ndi Yehova?
Ngati ndinu mpainiya, n’ciani cingakuthandizeni kuti mupitilize utumiki wopindulitsa umenewu?
Ngati sindinu mpainiya tsopano, n’ciani cingakuthandizeni kuti muyambe utumiki umenewu?
1, 2. (a) Kodi kuganizila ndi kulankhula za munthu amene timakonda kungakhale ndi zotsatilapo zotani? (Onani cithunzi-thunzi cimene cili kuciyambi kwa nkhani ino) (b) Kodi tidzakambilana mafunso ati?
KUGANIZILA ndi kulankhula za munthu amene timakonda kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi munthuyo. N’cimodzi-modzi ndi ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Pamene Davide anali m’busa, nthawi zambili usiku anali kuyang’ana nyenyezi mwacidwi kumwamba ndi kusinkha-sinkha za amene anazilenga. Iye analemba kuti: “Ndikayang’ana kumwamba, nchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizila, ndipo mwana wa munthu wocokela kufumbi ndani kuti muzimusamalila?” (Sal. 8:3, 4) Pamene mtumwi Paulo anaganizila za mmene Yehova anali kukwanilitsila colinga cake pa Isiraeli wakuuzimu, iye anafuula kuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapeleka ndi oculuka kwambili.”—Aroma 11:17-26, 33.
2 Tikamatenga mbali pa nchito yolalikila, timaganizila ndi kulankhula za Yehova, ndipo zimenezi zimatilimbikitsa. Akristu ambili amene ndi atumiki a nthawi zonse amanena kuti kucita zambili pa nchito ya Ufumu kwawathandiza kukulitsa cikondi cao pa Mulungu. Kaya mukucita utumiki wa nthawi zonse kapena muli ndi colinga cakuti muyambe, dzifunseni kuti: ‘Kodi utumiki wa nthawi zonse ungalimbitse bwanji unansi wanga ndi Yehova?’ Ngati ndinu mpainiya dzifunseni kuti, ‘Kodi n’ciani cingandithandize kupitiliza utumiki wopindulitsa umenewu?’ Ngati simunayambe upainiya, kodi mungasinthe zinthu ziti pa umoyo wanu kuti muyambe? Tiyeni tikambilane mmene utumiki wa nthawi zonse ungalimbitsile unansi wathu ndi Mulungu.
MMENE UPAINIYA UMALIMBITSILA UNANSI WATHU NDI MULUNGU
3. Kodi timamva bwanji pamene tikambilana ndi ena mu utumiki za madalitso a Ufumu a mtsogolo?
3 Tikamauza ena za madalitso a Ufumu a mtsogolo timayandikila Yehova kwambili. Kodi ndi lemba liti limene mumakonda kugwilitsila nchito mukamalalikila ku nyumba ndi nyumba? Kodi mumagwilitsila nchito Salimo 37:10, 11; Danieli 2:44; Yohane 5:28, 29 kapena Chivumbulutso 21:3, 4? Nthawi zonse tikamakambilana ndi anthu ena za malonjezo amene ali pa Malemba amenewa, ifeyo timakumbukila kuti Mulungu woolowa manja ndiye amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” Zimenezi zimatipangitsa kumuyandikila kwambili.—Yak. 1:17.
4. Kodi kulalikila anthu osauka mwa kuuzimu kumatithandiza bwanji kuyamikila ubwino wa Mulungu?
4 Tikaona anthu osauka mwa kuuzimu amene timawalalikila, timayamikila kwambili kuti tinaphunzila coonadi. Anthu m’dzikoli amasowa malangizo amene angawathandize kuti akhale ndi moyo wopindulitsa ndi wacimwemwe. Ambili ali ndi nkhawa kaamba ka tsogolo lao ndipo alibe ciyembekezo. Iwo amafuna kudziŵa colinga ca moyo. Ngakhale anthu ambili amene amapembedza sadziŵa zambili zimene Malemba amanena. Ali ngati anthu a mumzinda wakale wa Nineve. (Ŵelengani Yona 4:11.) Ngati titenga mbali mokwanila pa nchito yolalikila, timaona kusiyana kwakukulu pakati pa anthu amene timawalalikila ndi anthu a Yehova. (Yes. 65:13) Timaona kuti Yehova ndi wabwino cifukwa amatipatsa cakudya ca kuuzimu ndi kuitananso anthu onse kuti atsitsimulidwe mwa kuuzimu ndi kukhala ndi ciyembekezo ceni-ceni.—Chiv. 22:17.
5. Kodi timawaona bwanji mavuto athu tikamathandiza ena mwa kuuzimu?
5 Kuthandiza ena mwa kuuzimu kumatithandiza kuti mavuto amene timakumana nao asatifooketse. Trisha, mpainiya wa nthawi zonse anaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona pambuyo pakuti makolo ake alekana. Iye anati: “Ndinavutika kwambili maganizo pamene makolo anga analekana.” Tsiku lina Trisha anakhumudwa kwambili ndipo anafuna kungokhala panyumba. Ngakhale zinali conco, iye anapita kukatsogoza phunzilo la Baibo kwa ana atatu amene anali pa mavuto aakulu. Anao anasiidwa ndi atate ao ndipo mkulu wao anali kuwavutitsa. Trisha anati: “Anao anali kuvutika kwambili kuposa mmene ndinali kuvutikila. Pamene ndinali kuphunzila nao, nkhope zao zinali zacimwemwe kwambili. Anao anali ngati dalitso la Yehova pa tsiku limenelo.”
6, 7. (a) Kodi cikhulupililo cathu cimalimba bwanji ngati tiphunzitsa ena coonadi ca m’Baibo? (b) Kodi kuona ophunzila Baibo akusintha miyoyo yao mwa kugwilitsila nchito mfundo za m’Malemba, kumakhudza bwanji mmene timaonela nzelu za Mulungu?
6 Pamene tiphunzitsa ena coonadi ca m’Baibo, cikhulupililo cathu cimalimba. Mtumwi Paulo anakamba za Ayuda ena amene anali kucita zosiyana ndi zimene anali kuphunzitsa. Iye anati: “Kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha?” (Aroma 2:21) Koma zimenezo ndi zosiyana kwambili ndi zimene apainiya amacita. Iwo amapeza mipata yambili yolalikila ndi kutsogoza maphunzilo a Baibo. Kuti acite zimenezi mogwila mtima, io amakonzekela phunzilo lililonse ndipo nthawi zina amakonzekela kukayankha mafunso mu utumiki. Mpainiya wina wochedwa Janeen anati: “Nthawi zonse ndikamaphunzitsa ena coonadi ndimaona kuti mfundo za coonadi zimakhazikika kwambili mumtima ndi m’maganizo anga. Zimenezi zathandiza kuti cikhulupililo canga cilimbe.”
7 Tikaona ophunzila Baibo akusintha miyoyo yao mwa kutsatila mfundo za m’Baibo, timayamikila kwambili nzelu za Mulungu. (Yes. 48:17, 18) Zimenezi zimatilimbikitsanso kuti tiziyesetsa kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibo pa umoyo wathu. Mpainiya wina wochedwa Adrianna anati: “Anthu sangakhale ndi umoyo wabwino ngati adalila nzelu zao. Koma akayamba kudalila malangizo anzelu a Yehova, umoyo wao umakhala wopindulitsa.” Phil ananena zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Timaona mmene Yehova amathandizila anthu kusintha umoyo wao pambuyo pakuti io alephela kusintha paokha.”
8. Kodi timamva bwanji tikamalalikila ndi abale athu?
8 Kugwila nchito yolalikila ndi abale athu, kumatilimbitsa mwa kuuzimu. (Miy. 13:20) Apainiya ambili amathela nthawi yaitali mu ulaliki ndi alaliki anzao. Izi zimawapatsa mpata waukulu wakuti ‘alimbikitsane.’ (Aroma 1:12; Ŵelengani Miyambo 27:17.) Lisa amene ndi mpainiya anati: “Kunchito nthawi zambili kumakhala mzimu wampikisano ndi kaduka. Masiku onse ndimamva anthu akudyela anzao misece ndi kulankhulana mau oipa. Amafuna kukhala oyamba pa ciliconse. Nthawi zina anthu amandiseka ndi kundinyoza cifukwa cokhala ndi khalidwe lacikristu. Koma kulalikila ndi Akristu ena kumandilimbikitsa. Ndikaweluka mu utumiki, ndimakhala wosangalala ngakhale kuti ndili wotopa kwambili.”
9. Kodi kucita upainiya ndi mwamuna kapena mkazi wathu kumalimbitsa bwanji cikwati?
9 Kucita upainiya ndi mwamuna kapena mkazi wathu kumalimbitsa cikwati. (Mlal. 4:12) Madeline, amene akucita upainiya ndi mwamuna wake anafotokoza kuti: “Ine ndi mwamuna wanga timakambitsilana zocitika mu ulaliki ndi nkhani za m’Baibo zimene tingagwilitsile nchito mu ulaliki. Caka ciliconse tikamacita upainiya, cikwati cathu cimalimba.” Nayenso Trisha anati: “Ine ndi mwamuna wanga timayesetsa kuti tisaloŵe m’nkhongole ndipo zimenezi zathandiza kuti tisamakangane pa nkhani ya ndalama. Nthawi zonse timakhala otangwanika kupanga maulendo obwelelako ndi kutsogoza maphunzilo a Baibo. Zimenezi zatithandiza kuti tizikondana kwambili ndi kukhala olimba kuuzimu.”
10. Kodi cidalilo cathu pa Yehova cimakula bwanji tikamaona mmene iye amatithandizila cifukwa coika zinthu za Ufumu patsogolo?
10 Timadalila kwambili Yehova tikamaika patsogolo zinthu za Ufumu ndi kuona iye akutithandiza ndi kuyankha mapemphelo athu. Akristu onse okhulupilika amadalila Yehova. Conco, apainiya amaona kuti kudalila kwambili Yehova kumawathandiza kuti apitilize kucita utumiki wa nthawi zonse. (Ŵelengani Mateyu 6:30-34.) Curt, amene ndi mpainiya ndiponso woyang’anila dela wogwilizila, anavomela kukacezetsa mpingo wina umene unali pa mtunda woyenda ndi galimoto kwa maola aŵili ndi hafu. Iye ndi mkazi wake amenenso ndi mpainiya, analibe mafuta okwanila m’galimoto yao kuti afike ku mpingo ndi kubwelela, ndipo anali asanalandile ndalama ku nchito. Curt anati, “Ndinayamba kuganiza kuti sindinafunike kupita kukacezetsa mpingowo.” Atapemphela, io anaganiza zakuti adzakwanitsa kutumikila cifukwa cokhulupilila kuti Mulungu adzawasamalila. Atatsala pang’ono kunyamuka, mlongo wina anafika ndi kuwauza kuti anawabweletsela mphatso. Iye anawapatsa ndalama zimene anafunikila kuti akwanitse kuyenda ulendowo ndi kubwelela. Curt ananena kuti, “Zinthu zotele zikamacitika kaŵili-kaŵili, ndimaona kuti Yehova akundithandiza.”
11. Kodi ndi madalitso otani amene apainiya amapeza?
11 Apainiya aona kuti pamene amatenga mbali mokwanila mu utumiki wa Yehova ndi kukulitsa ubwenzi wao ndi iye, ‘amapeza’ madalitso oculuka. (Deut. 28:2) Ngakhale n’conco, apainiya naonso amakumana ndi mavuto. Palibe mtumiki wa Mulungu amene sakumana ndi mavuto amene anayamba cifukwa ca kupanduka kwa Adamu. Nthawi zina Akristu ena amaleka kucita upainiya kaamba ka mavuto, koma n’zotheka kulimbana nao kapena kuwapewa. Kodi n’ciani cingathandize apainiya kupitiliza utumiki wamtengo wapatali umenewu?
PITILIZANI KUCITA UPAINIYA
12, 13. (a) N’ciani cimene mpainiya angacite ngati amalephela kukwanilitsa maola oikika? (b) N’cifukwa ciani n’kofunika kwambili kuti mpainiya akhale ndi ndandanda yoŵelenga Baibo, kucita phunzilo laumwini, ndi kusinkha-sinkha?
12 Apainiya ambili amakhala ndi zocita zambili. Izi zingacitse kuti azilephela kukwanilitsa zinthu zina, conco afunika kukhala ndi ndandanda yabwino. (1 Akor. 14:33, 40) Ngati mpainiya amalephela kukwanilitsa maola oikika, ayenela kuonanso mmene amagwilitsila nchito nthawi yake. (Aef. 5:15, 16) Ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimathela nthawi yaitali bwanji pa zosangulutsa? Kodi ndi zinthu ziti zimene ndiyenela kusintha? Kodi ndiyenela kusintha nthawi imene ndimacita nchito zina zakuthupi?’ Mpainiya aliyense ayenela kudzifunsa mafunso amenewa nthawi zonse kuti aone ngati pali zinthu zina zimene ayenela kusintha.
13 Mpainiya ayenela kukhala ndi nthawi yoŵelenga Baibo, kucita phunzilo laumwini, ndi kusinkha-sinkha. Motelo, iye amafunikila kukhala wodziletsa kuti zinthu zosafunika kweni-kweni zisamuonongele nthawi yocita zinthu zofunika kwambili. (Afil. 1:10) Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti mpainiya wafika panyumba m’madzulo pambuyo pakuti walalikila kwa nthawi yaitali. Iye afuna kukonzekela misonkhano. Koma ayamba kuŵelenga ndi kutumiza mauthenga a pa foni. Kenako iye akutsegula wailesi ndi kuyamba kumvetsela pulogalamu imene amakonda kwambili. Iye wangozindikila kuti waononga kale pafupi-fupi maola aŵili asanayambe kukonzekele misonkhano. N’cifukwa ciani zimenezi zingakhale vuto kwa mpainiya? Akatswili othamanga amasamalila matupi ao kuti apitilize nchito yao. Mofananamo, apainiya afunika kukhala ndi ndandanda yotsatilika bwino yocita phunzilo laumwini kuti akhale ndi thanzi mwa kuuzimu ndi kuti apitilize utumiki wa nthawi zonse.—1 Tim. 4:16.
14, 15. (a) N’cifukwa ciani apainiya ayenela kukhala ndi umoyo wosalila zambili? (b) Kodi apainiya afunika kucita ciani akakumana ndi mavuto?
14 Apainiya afunika kukhala ndi umoyo wosalila zambili kuti akwanitse nchito yao. Yesu analimbikitsa ophunzila ake kukhala ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi. (Mat. 6:22) Iye anakhala ndi umoyo wosalila zambili kuti acite utumiki wake popanda zoceukitsa. Yesu anati: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlenga-lenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiletu poti n’kutsamila mutu wake.” (Mat. 8:20) Mpainiya amene afuna kutsanzila Yesu, ayenela kukumbukila kuti munthu akakhala ndi zinthu zambili za kuthupi amafunikanso nthawi yambili yosamalila zinthuzo.
15 Apainiya amadziwa kuti utumiki wao ndi wopatulika, koma saona Akristu ena kukhala otsika. M’malo mwake amakumbukila kuti utumiki umenewu ndi mphatso ya kwa Mulungu. Conco mpainiya aliyense afunikila kudalila Yehova kuti apitilize utumiki wake. (Afil. 4:13) Nthawi zina apainiya angakumane ndi mavuto. (Sal. 34:19) Zikatelo, apainiya ayenela kudalila Yehova kuti awathandize m’malo mosiya utumiki wao. (Ŵelengani Salimo 37:5.) Pamene apainiya aona kuti Mulungu akuwathandiza mwacikondi, io amayandikila kwambili Atate wao wakumwamba.—Yes. 41:10.
KODI MUNGAYAMBE UPAINIYA?
16. Kodi muyenela kucita ciani ngati mufuna kuyamba upainiya?
16 Ngati mufuna kulandila madalitso ofanana ndi amene atumiki a nthawi zonse amapeza, muyenela kumuuza Yehova colinga canu. (1 Yoh. 5:14, 15) Funsani atumiki a nthawi zonse kuti akuuzeni zimene zinawathandiza kuti ayambe upainiya. Khalani ndi zolinga zimene zingakuthandizeni kuti mudzakhale mpainiya. Izi ndi zimene Keith ndi Erika anacita. Asanakwatilane, io anali kucita upainiya. Atakwatilana, anagula galimoto ndi nyumba monga mmene anzao anacitila. Iwo anati: “Tinaganiza kuti zinthu zimenezi zidzatibweletsela cimwemwe, koma zimenezo sizinacitike.” Pamene Keith analeka nchito, anayamba upainiya wothandiza. Iye anakamba kuti: “Kucita upainiya wothandiza kunandikumbutsa cimwemwe cimene munthu amakhala naco akakhala mu utumiki.” Iwo anakhala paubwenzi ndi banja lina limene linali kucita upainiya. Banjalo linawathandiza kuona cimwemwe cimene cimabwela kaamba kokhala ndi umoyo wosalila zambili ndi kucita upainiya. Kodi Keith ndi Erika anacita ciani? Iwo ananena kuti “Tinalemba zolinga zathu za kuuzimu pa pepala ndi kulimata pa filiji, ndipo tinali kuconga colinga ciliconse cimene takwanilitsa.” M’kupita kwa nthawi, io anayambanso upainiya.
17. N’cifukwa ciani n’kwanzelu kusintha zinthu pa umoyo wanu kuti muyambe upainiya?
17 Kodi mungayambe upainiya? Ngati pali pano muona kuti simungakwanitse, yesetsani kuyandikila kwambili Yehova mwa kutenga mbali mokwanila pa nchito yolalikila. Pambuyo popemphela ndi kudzipenda, mudzaona kuti pali zinthu zina zimene mungasinthe pa umoyo wanu kuti muyambe upainiya. Mukayamba upainiya mudzakhala ndi madalitso ambili ndipo simudzadandaula kuti munadzimana zinthu zina. Mudzakhala ndi cimwemwe coculuka cimene cimabwela kaamba koika zinthu za Ufumu patsogolo. (Mat. 6:33) Mudzakhalanso ndi nthawi yaikulu yoganizila ndi kukambilana ndi anthu ena za Yehova. Izi zidzakuthandizani kukonda kwambili Yehova ndi kumusangalatsa.
[Zithunzi papeji 29]
Tikamacita zambili mu utumiki wa nthawi zonse, timakhala ndi umoyo wokhutilitsa (Onani ndime 9)