LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 11/1 tsa. 5
  • Bodza Lakuti Mulungu Ndi Wankhanza

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Bodza Lakuti Mulungu Ndi Wankhanza
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 11/1 tsa. 5

NKHANI YA PACIKUTO | MABODZA AMENE AMALEPHELETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU

Bodza Lakuti Mulungu Ndi Wankhanza

ZIMENE ANTHU AMBILI AMAKHULUPILILA Katekisimu wa Akatolika amati: “Pambuyo pa imfa, mizimu ya anthu amene anali kucita zoipa imapita ku helo kumene imakazunzika ndi ‘moto wosatha.’” Abusa ena a cipembedzo amakamba kuti anthu amene ali ku helo ndi otalikilana kothelatu ndi Mulungu.

ZIMENE BAIBO IMANENA “Moyo umene ukucimwawo ndi umene udzafe.” (Ezekieli 18:4) “Akufa sadziŵa ciliconse.” (Mlaliki 9:5) Conco, popeza kuti moyo umafa ndipo akufa sadziŵa ciliconse, kodi n’zotheka kuti munthu wakufa azunzike ndi “moto wosatha”?

M’Baibo, mau a Ciheberi ndi Cigiriki amene nthawi zambili amatembenuzidwa kuti “helo,” kweni-kweni amatanthauza manda a anthu onse. Mwacitsanzo, pamene Yobu anadwala matenda opweteka kwambili, iye anapemphela kuti: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’manda [“m’helo,” Baibo ya Douay-Rheims].” (Yobu 14:13) Mwacionekele, Yobu sanali kunena za kukapuma kumalo ozunzilako anthu, koma anali kunena za kukapuma kumanda a anthu onse.

N’CIFUKWA CIANI KUDZIŴA ZIMENEZI N’KOFUNIKA? Ngati timakhulupilila kuti Mulungu ndi wankhanza, sitingamukonde. Mwacitsanzo, Rocío, wa ku Mexico anati: “Kuyambila ndili mwana ndinaphunzila kuti kuli moto wa helo. Ndinali kucita mantha kwambili cakuti ndinayamba kuona kuti Mulungu ndi woipa mtima. Ndinali kuganiza kuti iye ndi waukali ndiponso wosaganizila ena.”

Kudziŵa zimene Baibo imanena zokhudza ziweluzo za Mulungu ndi mmene akufa alili kunathandiza Rocío kuti aziona kuti Mulungu ndi wacikondi. Iye anati: “Ndinamasuka kwambili ndipo ndinalibenso nkhawa. Ndinayamba kukhulupilila kuti Mulungu amatifunila zabwino, amatikonda ndi kuti n’zotheka kukhala naye pa ubwenzi. Iye ali ngati tate amene amagwila ana ake pa dzanja ndipo amawafunila zabwino.”—Yesaya 41:13.

Anthu ambili amapita kuchalichi cifukwa coopa moto wa helo. Koma Mulungu safuna kuti anthu azimulambila cifukwa cakuti amacita naye mantha. Ndiye cifukwa cake Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako.” (Maliko 12:29, 30) Komanso, tikadziŵa kuti Mulungu sacita zinthu zopanda cilungamo, tingakhale ndi cikhulupililo cakuti iye adzaweluza mwacilungamo mtsogolo. Mofanana ndi bwenzi la Yobu, Elihu, tinganene ndi mtima wonse kuti: “Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani