LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 5/1 tsa. 16
  • Kuyankha Mafunso A m’Baibulo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyankha Mafunso A m’Baibulo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • ‘Citani Zimenezi Pondikumbukila’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kutifela?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Mgonelo wa Ambuye—Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 5/1 tsa. 16

Kuyankha Mafunso A m’Baibulo

N’cifukwa ciani tiyenela kukumbukila imfa ya Yesu?

Imfa ya Yesu ndi yapadela kwambili m’mbili ya anthu. Iye anafa kuti abwezeletse moyo wa anthu mmene unafunika kukhalila. Anthu sanalengedwe kuti azicita zoipa, kudwala kapena kuti azifa. (Genesis 1: 31) Koma ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu woyamba, Adamu. Ngakhale n’conco, Yesu anapeleka moyo wake kutipulumutsa ku ucimo ndi imfa.—Ŵelengani Mateyu 20:28; Aroma 6:23.

Mulungu anaonetsa cikondi cacikulu potumiza mwana wake padziko lapansi kuti adzatifele. (1 Yohane 4:9, 10) Yesu anauza otsatila ake kuti azikumbukila imfa yake pa mwambo wosavuta mwa kugwilitsila nchito mkate ndi vinyo. Mwa kucita zimenezi caka ciliconse timasonyeza kuyamikila cikondi cimene Mulungu ndi Yesu anationetsa.—Ŵelengani Luka 22:19, 20.

Ndani ayenela kudya mkate ndi kumwa vinyo?

Nthawi yoyamba pamene Yesu anali kuuza ophunzila ake kuti azikumbukila imfa yake, anachula za pangano. (Mateyu 26:26-28) Panganoli linatsegula mwai kwa ophunzilawo ndi anthu ena ocepa wokakhala mafumu ndi ansembe kumwamba pamodzi ndi Yesu. Ngakhale kuti anthu mamiliyoni ambili amakumbukila imfa ya Yesu, ndi okhawo ali m’panganoli amene ayenela kudya mkate ndi kumwa vinyo.—Ŵelengani Chivumbulutso 5:10.

Kwa zaka pafupifupi 2,000, Yehova wakhala akusankha amene adzakhale mafumu. (Luka 12:32) Ciŵelengelo cao ndi cocepa poyelekezela ndi amene adzakhala padziko kosatha.—Ŵelengani Chivumbulutso 7:4, 9, 17.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 5 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Buku limeneli lipezekanso pa Webusaiti ya www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani