LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 11/1 masa. 11-13
  • Pemphelo—Kodi Lingakuthandizeni Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pemphelo—Kodi Lingakuthandizeni Bwanji?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Timakhala ndi mtendele wa m’maganizo.
  • Timatonthozedwa ndi kulimbikitsidwa tikakumana ndi mayeselo.
  • Timalandila nzelu zocokela kwa Mulungu.
  • Kodi Mapemphelo Angakuthandizeni Bwanji?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/1 masa. 11-13
Mkazi akupemphela ndipo akuganizila za amai ake amene ndi wodwala

Pemphelo—Kodi Lingakuthandizeni Bwanji?

Tisanacite ciliconse, mwacibadwa timadzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzapeza phindu lotani?’ Kodi n’kulakwa kufunsa funso limeneli pa nkhani ya pemphelo? Osati kwenikweni. Mwacibadwa, timafuna kudziŵa ngati cimene tifuna kucita cili ndi phindu lililonse. Ngakhale munthu wabwino Yobu anafunsa kuti: “Nditamuitana, kodi angandiyankhe?”—Yobu 9:16.

M’nkhani zoyambilila, taona umboni wakuti pemphelo n’lofunika kwambili osati polambila cabe kapena tikapanikizika maganizo. Mulungu woona amamva mapemphelo. Ngati tipemphela m’njila yovomelezeka ndipo timapempha zinthu zoyenela, Mulungu adzatimvetsela. Ndipo iye amatipempha kuti timuyandikile. (Yakobo 4:8) Conco, kodi tidzapindula bwanji ngati timapemphela tsiku ndi tsiku? Tiyeni tikambilane ena mwa mapindu a pemphelo.

Timakhala ndi mtendele wa m’maganizo.

Mukakumana ndi mavuto paumoyo wanu, kodi mumada nkhawa kwambili? Panthawi ngati imeneyi, Baibulo limatilimbikitsa ‘kupemphela mosalekeza,’ komanso kuti ‘zopempha zathu zidziŵike kwa Mulungu.’ (1 Atesalonika 5:17; Afilipi 4:6) Baibulo limatitsimikizila kuti ngati tipemphela kwa Mulungu, “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima [yathu] ndi maganizo [athu].” (Afilipi 4:7) Ngati tiuza Atate wathu wakumwamba nkhawa zathu, tidzakhala ndi mtendele wa m’mganizo. Ndipotu iye amatilimbikitsa kucita zimenezi. Lemba la Salimo 55:22 limati: “Umutulile Yehova nkhawa zako, Ndipo iye adzakucilikiza.”

“Umutulile Yehova nkhawa zako, Ndipo iye adzakucilikiza.”—Salimo 55:22

Anthu ambili padziko lonse lapansi akhalapo ndi mtendele umenewo. Mkazi wina dzina lake Hee Ran wa ku South Korea anakamba kuti: “Ndikakhala ndi mavuto aakulu, ndimapemphela ndipo ndikatelo, ndimamva bwino ndipo ndimamva kuti ndili ndi mphamva zopilila mavutowo.” Nayenso Cecilia wa ku Philippines anakamba kuti: Monga kholo, ndimada nkhawa kwambili ndi ana anga komanso amai anga amene tsopano sakwanitsa kundidziŵa cifukwa ca ukalamba ndi matenda. Koma ndimakwanitsa kucita zofunika za tsiku ndi tsiku ndili ndi nkhawa zocepa cifukwa ca pemphelo. Ndikudziŵa kuti Yehova adzandithandiza kuwasamalila.”

Timatonthozedwa ndi kulimbikitsidwa tikakumana ndi mayeselo.

Kodi ndinu wopanikizika maganizo cifukwa cakuti moyo wanu uli pangozi kapena mukukumana ndi mavuto aakulu? Kupemphela kwa “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse” kungatipatse mpumulo waukulu. Baibulo limatiuza kuti iye “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Mwacitsanzo, panthawi ina pamene Yesu anapanikizika maganizo, “anagwada ndi kuyamba kupemphela.” Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? “Mngelo wocokela kumwamba anaonekela kwa iye ndi kumulimbikitsa.” (Luka 22:41, 43) Mwamuna wina wokhulupilika Nehemiya, anaopsezedwa ndi anthu oipa amene anayesetsa kumuletsa kugwila nchito ya Mulungu. Iye anapemphela kuti: “Inu Mulungu wanga, limbitsani manja anga.” Zocitika zimene zinatsatilapo, zikuonetsa kuti Mulungu anamuthandiza kugwila bwino nchito yake. (Nehemiya 6:9-16) Ponena za pemphelo, Reginald wa ku Ghana anafotokoza kuti: “Ndikapemphela, makamaka pamene ndili pamavuto, ndimamva kuti ndafotokozela munthu amene ali ndi njila yondithandizila ndipo amanditsimikizila kuti ndisade nkhawa.” Zoonadi, Mulungu amatitonthoza tikapemphela kwa iye.

Timalandila nzelu zocokela kwa Mulungu.

Zinthu zina zimene timasankha zimatikhudza ndipo zingakhudzenso anthu ena amene timakonda. Nanga tingasankhe bwanji zinthu mwanzelu? Baibulo limati: “Ngati wina akusoŵa nzelu [makamaka panthawi ya mayeselo], azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka moolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.” (Yakobo 1:5) Tikapempha nzelu kwa Mulungu, iye amatipatsa mzimu woyela kuti utithandize kusankha zinthu mwanzelu. Ndipo tiyenela kupempha mzimu woyela cifukwa Yesu anatitsimikizila kuti, “Atate wakumwamba adzapeleka moolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.

Mwamuna apemphela

“Ndinapemphela kwa Yehova mosalekeza kuti andithandize kusankha zinthu mwanzelu.”—Kwabena wa ku Ghana

Ngakhale Yesu anaona kuti kupempha Atate wake kuti am’thandize kusankha zinthu mwanzelu n’kofunika. Baibulo limatiuza kuti pamene Yesu anafuna kusankha amuna 12 kuti akhale otsatila ake, “anacezela kupemphela kwa Mulungu usiku wonse.”—Luka 6:12.

Mofanana ndi Yesu, anthu ambili masiku ano amalimbikitsidwa akaona mmene Mulungu wawathandizila kusankha zinthu mwanzelu. Regina wa ku Philippines anafotokoza mavuto osiyanasiyana amene anakumana nao. Mavuto monga kupezela banja lake zinthu zofunika pambuyo pa imfa ya mwamuna wake, kucotsedwa nchito, ndi kulela ana. N’ciani camuthandiza kusankha zinthu mwanzelu? Iye anakamba kuti: “Mwapemphelo ndimadalila thandizo la Yehova.” Kwabena wa ku Ghana, anakamba cifukwa cake anapempha Mulungu kuti amuthandize. Iye anati: “Ndinacotsedwa pa nchito ya zomangamanga imene inali ya malipilo abwino.” Poganizila zocita, iye anati: “Ndinapemphela kwa Yehova mosalekeza kuti andithandize kusankha zinthu mwanzelu.” Iye anapitiliza kuti: “Ndimakondwela kuti Yehova anandithandiza kusankha nchito imene imandithandiza kupeza zofunika za paumoyo ndi kucita zinthu za kuuzimu.” Inunso, Mulungu adzakutsogolelani ngati mupempha thandizo pa zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wanu ndi iye.

Takambilana zinthu zocepa cabe za mmene pemphelo lingakuthandizileni. (Kuti mudziŵe zambili onani bokosi lakuti “Ubwino wa Pemphelo.”) Koma kuti inu mulandile madalitso amenewa, coyamba muyenela kudziŵa Mulungu ndi cifunilo cake. Ngati mufuna kudziŵa za Mulungu, tikukulimbikitsani kupempha wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kuphunzila Baibulo.a Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuyandikila “Wakumva pemphelo.”—Salimo 65:2.

a Kuti mudziŵe zambili, pemphani a Mboni za Yehova a m’dela lanu kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.jw.org.

Ubwino wa Pemphelo

Timakhala ndi Mtendele wa m’maganizo “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.

Timatonthozedwa ndi Mulungu “Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

Timatsogozedwa kuti tisankhe zinthu mwanzelu “Conco ngati wina akusowa nzelu, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka moolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.”—Yakobo 1:5.

Timathandizidwa kupewa mayeselo “Pemphelani kosalekeza, kuti musaloŵe m’mayeselo.”—Luka 22:40.

Timakhululukidwa macimo “Ndipo anthu anga ochedwa ndi dzina langa akadzicepetsa n’kupemphela, n’kufunafuna nkhope yanga, n’kusiya njila zao zoipa, ine ndidzamva ndili kumwamba n’kuwakhululukila chimo lao.”—2 Mbiri 7:14.

Timapeza njila yothandizila ena “Pembedzelo la munthu wolungama limagwila nchito mwamphamvu kwambili.”—Yakobo 5:16.

Timalimbikitsidwa mapemphelo athu akayankhidwa “Ndipo Yehova anamuuza kuti [Solomo]: ‘Ndamva pemphelo lako ndi pempho lako lopempha cifundo kwa ine.’”—1 Mafumu 9:3.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani