Mau Oyamba
MUGANIZA BWANJI?
Nkhani ya amuna anayi okwela pa mahosi ni imodzi mwa nkhani zodziŵika kwambili m’buku la Chivumbulutso. Anthu ena amacita nayo mantha. Ena amacita nayo cidwi. Onani zimene Baibo imakamba zokhudza maulosi monga amenewa:
“Wodala ndi munthu amene amaŵelengela ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mau a ulosi umenewu.”—Chivumbulutso 1:3.
Magazini iyi ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza mmene tingapindulile na nkhani ya amuna anayi okwela pa mahosi.