LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 6 masa. 12-14
  • N’cifukwa Ciani Pali ma Baibo Osiyana-siyana?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Pali ma Baibo Osiyana-siyana?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • BAIBO YOYAMBILILA
  • BAIBO YA CIGIRIKI YA SEPTUAGINT
  • BAIBO YA M’CILATINI YOCHEDWA VULGATE
  • ZIMASULILO ZA BAIBO ZIWONJEZELEKA
  • Yehova Mulungu Amakonda Kukamba ndi Anthu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Mau a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 6 masa. 12-14
Ma Baibo osiyana-siyana alembedwa, kupulintiwa, na kuikidwa pa zipangizo

N’cifukwa Ciani Pali ma Baibo Osiyana-siyana?

N’cifukwa ciani pali zimasulilo zambili zosiyana-siyana za Baibo masiku ano? Kodi mamasulidwe atsopano a Baibo amakuthandizani kuimvetsetsa kapena ayi? Kudziŵa ciyambi cake kungakuthandizeni kuwayelekezela bwino.

Koma coyamba tifunse kuti, n’ndani analemba Baibo paciyambi? Nanga anailemba liti?

BAIBO YOYAMBILILA

Nthawi zambili, Baibo imagaŵidwa m’zigawo ziŵili. Cigawo coyamba cili na mabuku 39, ndipo muli “mawu opatulika a Mulungu.” (Aroma 3:2) Mulungu anauzila amuna okhulupilika kulemba mabuku amenewa pa nthawi yaitali. Anawalemba pafupi-fupi zaka 1,100 kuyambila mu 1513 B.C.E. mpaka ca kumapeto kwa caka ca 443 B.C.E. Ambili mwa mabuku amenewa anawalemba m’Ciheberi, ndiye cifukwa cake cigawo cimeneci timacicha Malemba a Ciheberi, cimadziŵikanso kuti Cipangano Cakale.

Cigawo caciŵili cili na mabuku 27 amenenso ni “mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Mulungu anauzila ophunzila a Yesu Khristu okhulupilika kulemba mabuku amenewa pa nthawi yocepa. Anawalemba pafupi-fupi zaka 60 kuyambila mu 41 C.E. kufika mu 98 C.E. Ndipo ambili analembedwa m’Cigiriki, conco cigawo cimeneci timacicha Malemba Acigiriki Acikhiristu, cimadziŵikanso kuti Cipangano Catsopano.

Mabuku 66 ouzilidwa amenewa onse pamodzi amapanga Baibo yathunthu—Uthenga wocoka kwa Mulungu kupita kwa anthu. Nanga n’cifukwa ciani panafunika zimasulilo zina za Baibo? Onani zifukwa zitatu zotsatilazi.

  • Kuti anthu aziŵelenga Baibo m’citundu cawo.

  • Kuti acotsemo zolakwa zimene zinapangidwa pokopela, na kubwezamo mau ake a paciyambi.

  • Kuti acotsemo mau ena acikale na kuikamo ena osavuta kumva.

Onani mmene anatsatilila mfundo zimenezi pomasulila ma Baibo aŵili oyambilila.

BAIBO YA CIGIRIKI YA SEPTUAGINT

Pafupifupi zaka 300 Yesu asanabadwe, akatswili odziŵa Ciyuda anayamba kumasulila Malemba a Ciheberi m’citundu ca Cigiriki. Baibo imene anamasulila inayamba kuchedwa kuti Baibo ya Cigiriki ya Septuagint. N’cifukwa ciani anaimasulila? Kuti athandize Ayuda ambili amene panthawiyo anali kukamba Cigiriki m’malo mwa Ciheberi, kuti amve “malemba oyela.”—2 Timoteyo 3:15.

Baibo ya Septuagint inathandizanso anthu mamiliyoni ambili amene sanali Ayuda ndipo anali kukamba Cigiriki, kudziŵa zimene Baibo imaphunzitsa. Inawathandiza bwanji? Pulofesa W. F. Howard anakamba kuti: “Kuyambila capakati pa zaka 100 zoyambilila, Baibo ya Septuagint inakhala ya machechi achikhristu. Amishonale a machechiwo anali kuyenda m’masunagoge ‘kufotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa wakuti Yesu ndiye Mesiya.’” (Machitidwe 17:3, 4; 20:20) Ici ndiye cifukwa cimodzi cinacititsa Ayuda “kusuliza Baibo ya Septuagint,” malinga na zimene katswili wina wa Baibo dzina lake F. F. Bruce anakamba.

Ophunzila a Yesu akalandila mabuku a Malemba Acigiriki Acikhristu, anali kuwaphatikiza pamodzi na Baibo ya Septuagint ya Malemba Aciheberi na kupanga Baibo ya thunthu imene tili nayo masiku ano.

BAIBO YA M’CILATINI YOCHEDWA VULGATE

Patapita zaka 300 Baibo itatha kulembedwa, katswili wina wa zacipembedzo dzina lake Jerome anatulutsa Baibo ya m’Cilatini, imene m’kupita kwa nthawi, inadzachedwa Latin Vulgate. Ma Baibo a m’Cilatini analiko osiyana-siyana. Nanga n’cifukwa ciani panafunika ina yatsopano? Buku ya The International Standard Bible Encyclopedia inati: “Jerome anafuna kukonzanso mau ena amene sanamasulidwe bwino, kukonza zimene zinalakwika, kucotsamo mau ena osafunika amene anawonjezelamo, na kubwezeletsa mau ena amene anacotsedwamo.”

Jerome anakonza zambili mwa zolakwika zimenezi. Koma patapita nthawi, akulu-akulu a machechi anapanga colakwa cacikulu. Iwo analengeza kuti Baibo ya Latin Vulgate ndiyo Baibo yokha yololeka, ndipo anacita zimenezi kwa zaka zambili. M’malo mothandiza anthu wamba kumvetsetsa Baibo, Baibo imeneyi inacititsa kuti anthu azilephela kuimvetsetsa, cifukwa m’kupita kwa nthawi anthu sanali kudziŵa Cilatini olo pang’ono.

ZIMASULILO ZA BAIBO ZIWONJEZELEKA

Anthu anapitiliza kutulutsa ma Baibo ena atsopano. Mwacitsanzo, ca m’ma 400 C.E. anatulutsa Baibo ina yochuka yochedwa Syriac Peshitta. Koma ca m’ma 1300 C.E., m’pamene anapanganso makonzedwe ena akuti anthu wamba aziŵelenga Baibo m’citundu cawo.

Kumapeto kwa zaka za m’ma 1300 C.E., John Wycliffe wa ku England anayamba kumasulila na kutulutsa Baibo m’Cizungu cimene ngakhale anthu wamba anali kumvela. M’kupita kwa nthawi, Johannes Gutenberg atayamba zopulinta-pulinta, akatswili ambili a Baibo anayamba kutulutsa ma Baibo osiyana-siyana m’zinenelo zambili zimene anthu anali kukamba zungulile Europe yonse.

Pamene ma Baibo a m’Cizungu anaculuka, anthu otsutsa anakamba kuti sikunali kofunikila kutulutsa ma Baibo osiyana-siyana m’citundu cimodzi. Mu 1700 C.E., mzungu wina amene anali mtsogoleli wacipembedzo, dzina lake John Lewis analemba kuti: “Citundu cimasila, conco n’kofunika kukonzanso ma Baibo ena akale kuti akhale na Citundu cimene anthu amakamba, cimene m’badwo umene ulipo ungamvetsetse.”

Masiku ano kuposa kale lonse, akatswili a Baibo ndiwo ali pa malo oyenelela opendanso ma Baibo ena akale. Iwo amamvetsetsa bwino ngako zinenelo zakale za m’Baibo, ndipo ali na mipukutu imene inapezeka posacedwa. Izi zimawathandiza kudziŵa mau enieni apaciyambi a m’Baibo.

Conco kukhala na zimasulilo zatsopano za Baibo n’kothandiza kwambili. Koma tiyenela kusamala na ma Baibo ena.a Komabe, tingapindule kwambili ngati okonzanso Baibo angacite zimenezo cifukwa cokonda kwambili Mulungu.

Kuti muŵelenge Baibo m’zinenelo zosiyana-siyana pa intaneti kapena pa cipangizo canu ca makono, pitani pa www.jw.org. Onani polemba kuti MABUKU > BAIBULO

a Onani nkhani yakuti, “Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino?” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008.

DZINA LOPATULIKA LA MULUNGU M’BAIBO

Dzina la Mulungu m’cidutswa ca mpukutu wa Septuagint wa m’nthawi ya Yesu

Dzina la Mulungu m’cidutswa ca mpukutu wa Septuagint wa m’nthawi ya Yesu

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, lili na dzina lopatulika la Mulungu lakuti Yehova m’Malemba a Ciheberi na m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Koma m’ma Baibo a Cizungu ambili masiku ano, dzinali mulibe. M’malomwake anaikamo dzina lakuti “Ambuye.” Omasulila ena amakamba kuti cifukwa cimodzi cocitila zimenezi n’cakuti, dzina lenileni la Mulungu limene limaimilidwa na zilembo zochedwa Tetragalamatoni (YHWH), silionekela olo pang’ono m’Baibo ya Cigiriki ya Septuagint imene inamasulidwa kucoka m’Malemba a Ciheberi. Koma kodi izi n’zoona?

Ca pakati pa zaka za m’ma 1900, kunapezeka zidutswa zakale kwambili za Baibo ya Septuagint za m’nthawi ya Yesu. Zidutswa zimenezo zili na dzina lopatulika la Mulungu lolembedwa m’Ciheberi. Zioneka kuti patapita nthawi, okopa Baibo anacotsamo dzina la Mulungu na kuikamo dzina la Cigiriki lakuti Kyʹri·os, lotanthauza kuti “Ambuye.” Koma mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, dzina la Mulungu linabwezeletsedwa m’malo ake.

KODI COONADI CA M’BAIBO CINASINTHIDWA?

Mpukutu wa Yesaya wa m’Nyanja Yakufa

Mpukutu wa Yesaya wa m’Nyanja Yakufa, wakhala zaka 2,000. Mau ake amafanana kwambili na mau ali m’Baibo masiku ano

N’zoona kuti okopa Baibo analakwitsa zina poikopa. Koma zolakwa zimenezo sizinasinthe coonadi ca m’Baibo. Buku ina inati: “Palibe ciphunzitso coona cacikhristu cimene ni cozikidwa pa Malemba okaikitsa.”—Our Bible and the Ancient Manuscripts.

Okopa Baibo aciyuda analakwitsa zinthu zing’ono-zing’ono poikopa. Buku ina inati: “Alembi aciyuda amene anakhalako m’zaka zoyambilila za Cikhristu anakopa Baibo ya Ciheberi mobweleza-bweleza, ndipo anaikopa molondola kwambili.” —Second Thoughts on the Dead Sea Scrolls.

Mwacitsanzo, mpukutu wa Yesaya umene unapezeka pa Mipukutu ya m’Nyanja Yakufa, ni wakale kwambili na zaka 1000 kuyelekezela na mau a m’mipukutu ina imene ilipo kale. Kodi ufanana bwanji na mau a m’mipukutu ina imene ilipo kale? Buku ina inati: “Ni mwa apa na apo pamene mau ena okayikitsa anawonjezeledwa kapena kucotsedwa.”—The Book. A History of the Bible.

Zolakwika monga kusinthanitsa zilembo, mau, kapena ziganizo zimene okopa ena anapanga mosasamala, zikuzindikilidwa mosavuta na kukonzedwa. Buku ina inati: “Palibe buku ina yakale zungulile dziko lonse imene mau ake ali na maumboni ambili monga Cipangano Catsopano.”—The Books and the Parchments.

“Okhulupilila amene ali na nkhawa ayenela kukhala otsimikiza kuti Baibo ni yolondola, cifukwa pafupifupi mau ake onse akale kwambili amene anali olembedwa pa gumbwa wa ku Iguputo, akufanana kwambili na mau a m’mipukutu ina imene ilipo. Mauwa ni olondolabe olo kuti anakopedwa na manja mobweleza-bweleza na kupulintidwa kambili-mbili.”—The Book. A History of the Bible.

Conco, kodi coonadi ca m’Baibo cinasinthidwa? Ndithudi ayi!

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani