LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp18 na. 3 masa. 6-7
  • Kodi Mulungu Amakudziŵani Bwino?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mulungu Amakudziŵani Bwino?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE CILENGEDWE CIMATIPHUNZITSA
  • ZIMENE BAIBO IMATIPHUNZITSA PA NZELU ZA MULUNGU
  • MULUNGU NI WACIFUNDO KWAMBILI
  • Mulungu Amakudziŵani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kodi Mulungu Ni Wacifundo Zoona?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Inde, Moyo Ukali na Phindu kwa Imwe!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Kodi Baibo Inganithandize Ngati Nili na Maganizo Ofuna Kudzipha?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
wp18 na. 3 masa. 6-7
Mapikica oonetsa mwamuna ali wakhanda, wacicepele, pa tsiku la cikwati cake, komanso ali na mkazi na ana ake

“Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” —SALIMO 139:16

Kodi Mulungu Amakudziŵani Bwino?

ZIMENE CILENGEDWE CIMATIPHUNZITSA

Ganizilani za mgwilizano umene umakhala pakati pa amphundu, umene anthu ambili angakonde kukhala nawo. Amphundu amagwilizana mwapadela kwambili. Nancy Segal, amene ni mkulu wa za maphunzilo pa Yunivesiti yochedwa Twin Studies Center, amene nayenso ni mphundu anati: “Amphundu ena pokambilana amadziŵa mosavuta zimene mnzake atanthauza na mmene akumvelela.” Mayi wina pofotokoza mgwilizano umene ulipo pakati pa iye na mphundu mnzake anati: “Aliyense amadziŵa zonse zokhudza mnzake.”

Kodi n’ciani cimapangitsa kuti azimvetsetsana bwino conco? Kafuku-fuku wina anati ngakhale kuti zimadalila malo kumene anakulila, komanso mmene analeledwela, zioneka kuti kufafana kwa majini n’kumene maka-maka kumapangitsa amphundu kumvetsetsana bwino.

GANIZILANI IZI: Kukamba zoona, Mlengi amene anapanga majini mwa njila yapadela imeneyi, amadziŵa bwino kwambili mmene aliyense wa ife anapangidwila. N’cifukwa cake wamasalimo Davide anati: “Munali kundicinga m’mimba mwa mayi anga. Mafupa anga sanali obisika kwa inu, pamene munali kundipanga m’malo obisika. . . . Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.” (Salimo 139:13, 15, 16) Mulungu yekha ndiye amatidziŵa bwino na kumvetsetsa mmene majini athu anapangidwila, komanso mavuto onse amene asintha umunthu wathu. Mulungu amatidziŵa mwapadela kwambili. Amadziŵa mmene tinapangidwila. Izi zimatitsimikizila kuti zoonadi amadziŵa zonse zokhudza ife.

ZIMENE BAIBO IMATIPHUNZITSA PA NZELU ZA MULUNGU

Davide anapemphela kuti: “Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa. Inu mumadziwa ndikakhala pansi kapena ndikaimilila. Mumadziwa maganizo anga muli kutali. Ndisananene kanthu, inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.” (Salimo 139:1, 2, 4) Kuonjezela apa, Yehova amadziŵa mmene timamvelela mu mtima, komanso “amazindikila maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.” (1 Mbiri 28:9; 1 Samueli 16:6, 7) Kodi mavesi aya amatiphunzitsa ciani za Mulungu?

Ngakhale kuti tingalephele kumuuza zonse za mu mtima mwathu m’pemphelo, komanso mmene timvelela, Mlengi wathu amaona osati cabe zimene timacita, koma amamvetsetsanso cifukwa cake timacita zimenezo. Cinanso, iye amadziŵa zinthu zabwino zimene timafunitsitsa kucita, ngakhale tilephele kucita zinthuzo. Popeza Mulungu ndiye anaika cikondi m’mitima yathu, amakhala wofunitsitsa kuona na kudziŵa ngati zolinga zathu na maganizo athu kwa ena amakhala acikondi.—1 Yohane 4:7-10.

Palibe cimene Mulungu sadziŵa. Iye amadziŵa mavuto athu ngakhale pamene ena saŵadziŵa, kapena kuwamvetsetsa bwino-bwino.

Malemba amatitsimikizila kuti

  • “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzelo lawo.”—1 PETULO 3:12.

  • Mulungu analonjeza kuti: “Ndidzakupatsa nzelu ndi kukulangiza njila yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anila.”—SALIMO 32:8.

MULUNGU NI WACIFUNDO KWAMBILI

Kodi kudziŵa kuti Mulungu amamvetsetsa mavuto athu, na mmene timvelela kungatithandize kupilila mavuto? Ganizilani zimene zinacitikila Anna wa ku Nigeria. Iye anati: “N’nayamba kuona kuti kukhala na moyo kulibe phindu, cifukwa ca mavuto othetsa nzelu amene n’nakumana nawo. N’nali mkazi wamasiye, komanso n’nali kudwazika mwana wanga wa mkazi amene anali m’cipatala na matenda a kuculuka madzi mu ubongo (hydrocephalus). Nthawi imodzi-modzi n’nali kudwala khansa ya kumaŵele, ndipo n’nali kufunika opaleshoni, kuikidwa m’mashini, komanso kulandila cithandizo camankhwala amphamvu. Kulandila cithandizo m’cipatala panthawi imene mwana wanga akulandilanso cithandizo m’cipatala cimodzi-modzi, zinali zovuta kwambili kuti nipilile.”

Nanga n’ciani cinathandiza Anna kupilila? Iye anati: “N’nayamba kuganizila malemba monga Afilipi 4:6, 7, imene ikamba kuti, ‘mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.’ Nthawi iliyonse nikakumbukila lembali, nimadzimva kuti nili pa ubwenzi wolimba na Yehova, ndipo nimadziŵa kuti amandimvetsetsa kwambili kuposa ine mwini. Nimalimbikitsidwanso kwambili na abale komanso alongo akuuzimu mu mpingo wacikhristu.

“Ngakhale kuti nikali kudwala, umoyo wanga komanso wa mwana wanga wakhalako bwino. Cifukwa Yehova ali ku mbali yathu, taphunzila kuganizila zinthu zabwino pamene tilimbana na mavuto. Yakobo 5:11 imatitsimikizila kuti: ‘Anthu amene anapilila timawacha odala. Munamva za kupilila kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa, mwaona kuti Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.’” Yehova anamvetsetsa bwino-bwino mavuto amene Yobu anali kukumana nawo, ndipo naise tidziŵe kuti amamvetsetsa mavuto onse amene tikumana nawo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani