Pansi pa ulamulilo wa Mulungu, zolengedwa zake zonse zinali zogwilizana komanso zinali pa mtendele
N’cifukwa Ciani Tifunikila Ufumu wa Mulungu?
Kuciyambi kwa mbili ya anthu, Mlengi wathu, amene dzina lake ni Yehova, ndiye yekha anali Wolamulila. Iye anali kulamulila mwacikondi. Anapanga malo okongola ochedwa munda wa Edeni, n’colinga cakuti anthu akhalemo. Ndiponso anaŵapatsa cakudya cokwanila. Kuwonjezela apo, anaŵapatsa nchito zokhutilitsa. (Genesis 1:28, 29; 2:8, 15) Sembe anthu anapitiliza kukhala pansi pa ulamulilo wacikondi wa Mulungu, akanakhalabe okondwela na mtendele mpaka lelo.
Anthu oyambilila anakana Mulungu kukhala Wolamulila wawo
Baibo imatiuza kuti mngelo wina wopanduka, amene pambuyo pake anayamba kuchedwa kuti Satana Mdyelekezi, anatsutsa ulamulilo wa Mulungu. Anati anthu angakhale acimwemwe popanda citsogozo ca Mulungu na ulamulilo wake. N’zomvetsa cisoni kuti makolo athu oyamba, Adamu na Hava, anamvela Satana na kupandukila Mulungu.—Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9.
Cifukwa cakuti Adamu na Hava anakana Mulungu monga Wolamulila wawo, anataya Paradaiso na ciyembekezo cawo cokakhala na moyo wosatha, komanso wathanzi langwilo. (Genesis 3:17-19) Cosankha cawo cinakhudzanso ana amene anakhala nawo pambuyo pake. Baibo imati cifukwa cakuti Adamu anacimwa, ‘ucimo unaloŵa m’dziko ndi imfa kudzela mwa ucimo.’ (Aroma 5:12) Ucimo unabweletsanso vuto lina ili lalikulu: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.” (Mlaliki 8:9) M’mawu ena, tingati anthu akamadzilamulila okha, nthawi zonse zotulukapo zake zimakhala mavuto.
CIYAMBI CA ULAMULILO WA ANTHU
Nimurodi anapandukila Yehova
Munthu woyamba wochulidwa m’Baibo kukhala wolamulila anali Nimurodi. Iye anapandukila ulamulilo wa Yehova. Kucokela m’nthawi ya Nimurodi, anthu aulamulilo saseŵenzetsa mphamvu zawo moyenela. Zaka pafupi-fupi 3,000 zapitazo, Mfumu Solomo analemba kuti: “Ndinaona misozi ya anthu amene akupondelezedwa, koma panalibe wowatonthoza. M’manja mwa opondelezawo munali mphamvu.”—Mlaliki 4:1.
Ni mmenenso zinthu zilili masiku ano. Mu 2009, buku la bungwe la United Nations linakamba kuti “mavuto ambili amene timakumana nawo amabwela” cifukwa ca ulamulilo woipa. Ndipo izi zicita kuonekelatu masiku ano.
NTHAWI YOCITAPO KANTHU!
Dzikoli lifunikila olamulila abwino komanso boma labwino. Ndipo n’zimene Mlengi wathu analonjeza!
Ngakhale maboma abwino a anthu alephela kucotsapo mavuto akulu-akulu amene anthu amakumana nawo
Mulungu anakhazikitsa Ufumu, kapena kuti boma limene lidzaloŵa m’malo maulamulilo onse a anthu. Ndipo iwo wokhawo ndiwo “udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Umenewu ndiwo Ufumu umene anthu ambili amapemphelela kuti ubwele. (Mateyu 6:9, 10) Koma sikuti Mulungu iye mwini ndiye adzalamulila m’bomali. M’malo mwake, iye anasankha wina amene panthawi ina anali na moyo monga munthu, kuti akhale Wolamulila. Kodi Mulungu anasankha ndani?