Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Yoweli
1. Kodi tingatsanzile bwanji kudzicepetsa kwa Yoweli pamene tilalikila?
1 Kodi mneneli Yoweli anali ndani? Baibo imangonena kuti anali “mwana wa Petueli.” (Yow. 1:1) Mneneli wodzicepetsa ameneyu anagogomeza kwambili uthenga wa Yehova, ndipo sanadzichukitse pokhala mthenga. Mofananamo, pamene tili muutumiki tiyenela kupeleka ulemelelo wonse kwa Yehova ndi kugwilitsila nchito Baibo, m’malo mofuna kutamandidwa kapena kuchuka. (1 Akor. 9:16; 2 Akor. 3:5) Kuonjezelapo, uthenga umene timalengeza umatipatsa mphamvu. Kodi ndi mbali ziti za ulosi wa Yoweli zimene zingatipangitse kukhala acangu komanso kukhala ndi ciyembekezo lelolino?
2. Kodi kuyandikila kwa tsiku la Yehova kuyenela kutilimbikitsa kucita ciani?
2 “Tsiku la Yehova lili pafupi.” (Yow. 1:15): Ngakhale kuti mau awa analembedwa zaka zambili zapitazo, tikukhala m’masiku a kukwanilitsika kwa ulosiwu. Kuipila-ipila kwa mikhalidwe ya padziko komanso kupanda cidwi kwa anthu ndi kunyozedwa kumene timakumana nako m’gawo lathu, ndi umboni woonekelatu wakuti masiku otsiliza a dongosolo loipa lino la zinthu ayandikila. (2 Tim. 3:1-5; 2 Pet. 3:3, 4) Tikamaganizila kwambili za kuyandikila kwa mapeto, m’pamene tidzaika utumiki wathu patsogolo mu umoyo wathu.—2 Pet. 3:11, 12.
3. N’cifukwa ciani ulaliki ndi wofunika maka-maka pamene tikuyandikila citsautso cacikulu?
3 “Yehova adzakhala citetezo kwa anthu ake.” (Yow. 3:16): Kugwedezeka kumene vesili lifotokoza kukutanthauza zimene zidzacitike pamene Yehova azidzapeleka ciweluzo pa cisautso cacikulu. Timatonthozedwa kudziŵa kuti Yehova adzapulumutsa atumiki ake okhulupilika panthawi imeneyo. (Chiv. 7:9, 14) Tikamacita nchito yolalikila ndi kuona mmene Yehova amatisamalila ndi kutilimbikitsa, tidzalimbitsa cikhulupililo cathu ndipo tidzakhala okhoza kupilila pa citsautso cacikulu cimene cibwela.
4. N’cifukwa ciani tiyenela kusangalala komanso kusaopa zamtsogolo?
4 Ngakhale kuti ena amati uthenga wa Yoweli umacititsa mantha, uthenga umenewu umapatsa anthu a Mulungu ciyembekezo cabwino cakuti adzapulumuka. (Yow. 2:32) Conco, tiyeni tisaope zamtsogolo ndipo tilalikile mwacangu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu komanso kulabadila mau opezeka pa Yoweli 2:23 akuti: “Kondwelani ndi kusangalala cifukwa ca Yehova Mulungu wanu.”