Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Mika
1. Kodi Mika ayenela kuti anadzifunsapo funso lotani? Nanga n’cifukwa ciani tinganene kuti zimene anali kulengeza zinakwanilitsidwa?
1 ‘Kodi dongosolo loipali la zinthu lidzatha liti?’ Mneneli Mika ayenela kuti anadzifunsapo funso limeneli polengeza uthenga wa ciweluzo ca Yehova pa ufumu wa Israeli ndi Yuda. Ndipo zimene Mika anali kulengeza zinacitikadi. Mau a Yehova onena za kuonongedwa kwa Samariya anakwanilitsidwa Mika akali ndi moyo mu 740 B.C.E. (Mika 1:6, 7) Pambuyo pake, Yerusalemu anaonongedwa mu 607 B.C.E. (Mika 3:12) Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Mika pamene tiyembekezela ciweluzo ca Yehova?
2. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife oleza mtima poyembekeza tsiku la Yehova? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kucita zimenezi?
2 Lezani Mtima: Mika analemba kuti: “Ine ndidzadikilila Yehova. Ndidzayembekezela moleza mtima Mulungu wa cipulumutso canga.” (Mika 7:7) Koma Mika sanakhale cabe ndi kuyembekezela mapeto. Iye anapitilizabe kutumikila mokangalika monga mneneli wa Yehova. Pamene tiyembekezela tsiku la Yehova, nafenso tiyenela kucita ‘nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu.’ (2 Pet. 3:11, 12) Kuleza mtima kwa Yehova kumapatsa anthu mpata wakuti alape. (2 Pet. 3:9) Conco, timatsatila malangizo a m’Baibo akuti tizitsatila citsanzo ca kuleza mtima kwa aneneli.—Yak. 5:10.
3. N’cifukwa ciani tiyenela kupempha Yehova kuti atipatse mzimu woyela?
3 Dalilani Mphamvu za Yehova: Ngakhale kuti Mika anali ndi nchito yovuta, anadalila Yehova kuti acite nchitoyo. (Mika 3:8) Ndiye cifukwa cake Mau a Yehova amatilimbikitsa kudalila mphamvu za Mulungu. Iye amapeleka moolowa manja mphamvu kwa anthu otopa kuti akwanitse kumtumikila. (Sal. 84:5, 7; Yes. 40:28-31) Kodi inuyo munalandilapo mphamvu zake pomtumikila? Kodi mumapemphela kwa Yehova nthawi zonse kuti akupatseni mphamvu yake ya mzimu woyela?—Luka 11:13.
4. Kodi tingaphunzile ciani pa citsanzo cabwino ca Mika masiku ano?
4 Mika anaona kuti kucita cifunilo ca Mulungu kunali kofunika kwambili pa umoyo wake. Ngakhale kuti anali kukhala ndi anthu oipa, iye anakhalabe wokhulupilika. Mofanana ndi Mika, cikhulupililo cathu cimayesedwa tsiku lililonse. Conco, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kuti “tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kale-kale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5.