Bokosi La Mafunso
◼ Kodi ana ayenela kuphunzila ciani kuti akhale okhwima kuuzimu?
Makolo acikristu amacita zambili kuti alele ana ao “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Mwacitsanzo, makolo apeza kuti kuphunzila lemba la tsiku m’mawa uliwonse pamodzi ndi ana ao n’kothandiza kwambili. Panthawi ya kulambila kwa pabanja ndi pa zocitika zina, mabanja angaonelele vidiyo ndi kuikambilana mfundo zake pamodzi. Angakambilanenso nkhani zina za m’buku la Zimene Acinyamata Amafunsa, komanso angacite seŵelo nkhani ina ya m’Baibulo ndi kuyeseza pamodzi. Komabe, kuti ana akhale “okhwima mwa kuuzimu,” ayenela kuphunzitsidwa mfundo za coonadi ca m’Baibulo mozama.—Aheb. 6:1.
Ganizilani zimene timaphunzitsa anthu amene timakumana nao m’gawo lathu. Paulendo woyamba kapena ulendo wotsatila, nthawi zambili timayesetsa kuyambitsa phunzilo la Baibulo mwa kugwilitsila nchito buku lakuti Zimene Baibulo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Tikamaliza buku limeneli, timagwilitsila nchito buku lakuti “Khalanibe M’cikondi ca Mulungu.” N’cifukwa ciani timatelo? Buku la Zimene Baibulo Imaphunzitsa limathandiza ophunzila kudziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibulo. Buku la “Khalanibe M’cikondi” limawaphunzitsa mmene angagwilitsile nchito mfundo za m’Baibulo paumoyo wao wa tsiku ndi tsiku. Kuphunzila mabuku onse aŵili kumathandiza atsopano kuti akhale “ozikika mozama” mwa Kristu ndi ‘okhazikika m’cikhulupililo.’ (Akol. 2:6, 7) Kodi mabuku amenewa sangathandizenso ana athu? Iwonso afunika kudziŵa za dipo, Ufumu ndiponso mkhalidwe wa anthu akufa. Ana ayenelanso kudziŵa cifukwa cake Mulungu walola kuvutika ndi mmene timadziŵila kuti tili m’masiku otsiliza. Afunika kutsimikiza kuti Mboni za Yehova zili ndi coonadi. Acicepele naonso amafunika kumvetsa mfundo za m’Baibulo ndi kudziŵa mmene angagwilitsile nchito “mphamvu zao za kuzindikila.” (Aheb. 5:14) Makolo ayenela kuganizila msinkhu wa ana ao ndiponso zimene anawo angamvetse akamaphunzila. Komabe, ana ambili amakwanitsa kuyamba kuphunzila coonadi ca m’Baibulo cozama ngakhale kuti akali aang’ono.—Luka 2:42, 46, 47.
Pofuna kuthandiza makolo, pa webusaiti ya jw.org padzakhala njila zothandiza kuphunzila, zocokela m’buku lakuti Zimene Baibulo Imaphunzitsa. Mabanja angapeze zimenezi pa Webusaiti yathu poona pamene palembedwa kuti “BIBLE TEACHINGS > TEENAGERS.” Mtsogolomu, padzaikidwanso njila zina zothandiza kuphunzila zocokela m’buku la “Khalanibe M’cikondi.” Ngakhale zili conco, tingagwilitsilenso nchito mabuku enieniwo. Makolo angaone ngati azigwilitsila nchito mfundo zimenezi pa mbali ina ya Kulambila kwao kwa Pabanja, potsogoza phunzilo la Baibulo ndi mmodzi wa ana ao, kapena pophunzitsa mwana wao kucita phunzilo laumwini.