LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 7/14 tsa. 4
  • Maulaliki Acitsanzo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Maulaliki Acitsanzo
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Gwilitsilani Nchito Kapepala Katsopano Konena za Webu Saiti Yathu
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Maulaliki a Citsanzo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Maulaliki a Citsanzo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 7/14 tsa. 4

Maulaliki Acitsanzo

Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?

Mpatseni mwininyumba kapepala kauthenga kuti aone mutu kenako kambani kuti: “Muli bwanji? Tikugwila nchito yapadela yogaŵila anthu uthenga uwu wofunika imene ikucitika padziko lonse. Ndipo kapepalaka ndi kanu.”

Ngati mukusiya kapepala pa nyumba imene palibe anthu, mukaike pamalo oti anthu ena sangakaone ndipo mukapinde bwinobwino.

Ngati mwininyumba waonetsa cidwi ndipo akufuna mukambitsilane, mungamufunse zimene iye akuganiza pa mafunso amene ali ndi mayankho ocita kusankhapo omwe ali patsogolo pa kapepala kameneko. Tsegulani kapepala ndi kumuonetsa zimene lemba la Salimo 119:144, 160 limanena. M’fotokozeleni kuti kapepalako kakunena za Webu saiti imene ingamuthandize kupeza mayankho a m’Baibulo okhutilitsa. Mwina mungamuonetse kavidiyo kakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? Musanacoke, mungamuonetsenso mafunso atatu amene ali kumbuyo kwa kapepala ndi kum’pempha kuti akuuzeni funso limene afuna kuti adziŵe yankho lake. Muuzeni kuti mudzabwelanso kuti mukamuonetse mmene angapezele yankho la m’Baibulo pa funso limenelo pogwilitsila nchito jw.org. Mukadzabwelelako mukakambilane yankho mwa kuona pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.

Ngati mukuitanilanso anthu ku msonkhano wa cigawo, mungapeleke tumapepala twa ciitano kwa mwininyumba pa nthawi imodzi ndiyeno mungaonjezele kuti, “Kuonjezela pa kapepala kameneko, takupatsani kena kokuitanilani ku cocitika cina cimene cidzakhalako ndipo munthu aliyense angapezekepo kwaulele.”

Nsanja ya Mlonda August 1

Ngati mukugaŵila magazini kumapeto kwa mlungu mungakambe kuti: “Tikugaŵilanso magazini imene yangotuluka kumene. Magazini imeneyi ndi Nsanja ya Mlonda, imene ikupeleka yankho pa funso lakuti: Kodi Mulungu Amacita Nanu Cidwi?”

Galamukani! August

Ngati mukugaŵila magazini ya Galamukani! kumapeto kwa mlungu munganene kuti: “Tikugaŵilanso magaziniyi yatsopano. Magazini ya Galamukani! imeneyi ikuyankha funso lakuti: Kodi Anthu Angakhazikitse Bwanji Mtendele?”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani