Kukonzekela n’Kofunika Kuti Tiziphunzitsa Mwaluso
Yesu anafunsidwa funso lokhudza moyo wosatha kaŵili konse. Koma panthawi zonsezi, iye anayankha mogwilizana ndi zosoŵa za wofunsayo. (Luka 10:25-28; 18:18-20) Ngakhale kuti timalidziŵa bwino buku lophunzilila Baibulo, tifunika kukonzekelabe tili ndi wophunzila m’maganizo mwathu. Kodi ndi mfundo ziti zimene angavutike kumvetsetsa kapena kuzivomeleza? Ndi malemba ati amene tidzaŵelenga naye? Nanga tidzaphunzila zinthu zoculuka motani? Mwina tingafunike kukonzekela fanizo, mmene tidzafotokozela mfundo inayake kapena mafunso angapo kuti tithandize wophunzila kumvetsetsa nkhaniyo. Popeza Yehova ndi amene amakulitsa mbeu za coonadi mumtima mwa munthu, tifunika kum’pempha kuti atithandize pokonzekela phunzilo. Tifunikanso kum’pempha kuti athandize wophunzila wathu, ndi kuti adalitse khama lathu pothandiza wophunzilayo mwakuuzimu.—1 Akor. 3:6; Yak. 1:5.