Seŵenzetsani Zinthu Zopezeka m’Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa Mogwila Mtima
Wophunzila akadziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa ndi kucita zimene akuphunzila, adzakula mwakuuzimu ndi kubala zipatso. (Sal. 1:1-3) Tingathandize wophunzila wathu kukula mwakuuzimu mwa kuseŵenzetsa zinthu zina zothandiza zopezeka m’buku la Zimene Baibo lmaphunzitsa.
Mafunso Amene Ali Kuciyambi kwa Nkhani: Kuciyambi kwa nkhani iliyonse, kuli mafunso amene ayankhidwa m’nkhaniyo. Mungafunse mafunso amenewa pofuna kuthandiza wophunzila kukhala ndi cidwi. Mwinanso mungapemphe wophunzilayo kuti ayankhe mafunsowo mwacidule. Akapeleka yankho lolakwika, musamuongolele panthawi imeneyo. Mayankho ake adzakuthandizani kudziŵa mfundo zimene mufunika kuzifotokoza momveka bwino. —Miy. 16:23; 18:13.
Zakumapeto: Wophunzila akamvetsetsa ndi kuvomeleza nkhani imene mukuphunzila, mungamulimbikitse kuti akaŵelenge zakumapeto. Pa phunzilo lotsatila, mungapitemo mwacidule kuti muone ngati anamvetsetsa zimene anaŵelenga. Komabe, mukaona kuti afunika kum’thandiza kumvetsetsa nkhaniyo, zingakhale bwino kukambilana zakumapeto panthawi imene mucita phunzilo. Ŵelengani ndime ndipo m’funseni mafunso amene munakonzelatu.
Bokosi Lobwelelamo: Kothela kwa nkhani iliyonse kuli bokosi lobwelelamo limene likupeleka mayankho a mafunso amene ali kuciyambi kwa nkhani. Mungakambilane bokosi limeneli pofuna kuthandiza wophunzila kumvetsetsa mfundo zazikulu. Ŵelengani mfundo iliyonse pamodzi ndi malemba ake. Ndiyeno, pemphani wophunzila kuti afotokoze mmene mfundozo zikugwilizanilana ndi malemba.—Mac. 17:2, 3.