Bokosi La Mafunso
◼ Ndi Liti Pamene Tingaleke Kuphunzila Baibulo Ndi Munthu Wina?
Tikaona kuti wophunzila Baibulo sapita patsogolo mwakuuzimu, mwanzelu tingaleke kuphunzila naye. (Mat. 10:11) Ganizilani izi: Kodi wophunzilayo amapezeka panthawi imene munapangana kuti muziphunzila? Kodi amakonzekela zimene mudzaphunzila kukali nthawi? Kodi amapezeka pa misonkhano ina ya mpingo? Kodi amauzako ena zimene amaphunzila? Kodi akusintha umoyo wake mogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo? Komabe, tiyenela kuzindikila kuti anthu amapita patsogolo mosiyanasiyana malinga ndi msinkhu wao ndiponso maluso ao. Ndipo ngati mwasankha kuleka kuphunzila naye Baibulo, muuzeni kuti ndi womasuka kudzayambanso kuphunzila mtsogolo.—1 Tim. 2:4.